Zofunikira Zoyambirira
Mutu 8: Kuyankhulana ndi Atate Akumwamba


Mutu 8

Kuyankhulana ndi Atate Akumwamba

Atate athu Akumwamba amatikonda kwambiri. Iwo akonza njira yoti tizilankhula nawo nthawi iliyonse imene tafuna. Kodi tingayankhule bwanji ndi Atate athu Akumwamba?

Titha Kuyankhula ndi Atate athu Akumwamba

Kuyankhula ndi Atate athu Akumwamba kumatchedwa pemphero. Ngakhale kuti Atate athu Akumwamba amakhala kumwamba, tikhonza kuyankhula nawo ndipo amatimvera. Iwo amafuna kutithandiza. Iwo Adatipempha kuti tidzilankhula nawo. Tikamalankhula nawo, adzatithandiza kuchita zinthu zabwino.

Tikhonza kuwauza Atate athu Akumwamba zinthu zimene timaziganizira. Tikhonza kuwauza kuti timawakonda. Tikhonza kuwauza kuti tikuyamika pa zinthu zimene atipatsa. Tikhonza kuwapempha kuti atithandize.

Tikhonza kuyankhula ndi Atate athu Akumwamba nthawi iliyonse imene tikufuna kuyankhula nawo. Tikuyenera kuyankhula nawo tikakhala patokha Tikakhala patokha tikhonza kuyankhula nawo za mmene tikumvera komanso mavuto athu. Tikuyenera kuyankhula nawo mosachepera m’maŵa ndi usiku uliwonse.

Tikuyeneranso kuyankhula nawo limodzi ndi banja lathu. Tikhonza kuchita zimenezi m’mawa ndi usiku uliwonse. Tikhonzanso kuchita zimenezi tisanadye chakudya chilichonse tikamawathokoza chifukwa cha chakudya chathu.

Atate athu Akumwamba sadzasiya kufuna kuti tilankhule nawo. Iwo adzatikonda nthawi zonse ndipo amafuna kutithandiza. Ngakhale titachita zoipa, amatikondabe. Iwo adzatimvera ndi kutithandiza.

Zokambirana

  • Ndichifukwa chiyani tikuyenera kuyankhula ndi Atate athu Akumwamba?

  • Kodi tikuyenera kuyankhula nawo liti?

Image
mtsikana akugwada m’pemphero

Tikuyenera kupemphera aliyense payekha komanso ngati mabanja m’mawa ndi usiku.

Atate athu Akumwamba Adatiuza Mmene Tingalankhulire Nawo

Tikamapemphera, tikuyenera kuwauza Atate athu Akumwamba zinthu zimene timamva komanso zimene timafunikira. Sitikuyenera kunena mawu ofanana nthawi zonse tikamalankhula nawo. Sitikufunikira kuimba kapena kufuula.

Adatiuza njira yolankhulirana nawo. Tikuyenera kuyankhula nawo mwachindunji, kunena kuti: “Atate athu Akumwamba,” kapena mawu ofanana nawo. Tikuyenera kuyankhula nawo mwachikondi ndi mwaulemu.

Kenako, tikuyenera kuwathokoza chifukwa cha zinthu zimene atichitira.

Izi ndi zina mwa zinthu zomwe tikuyenera kuwathokoza:

  1. Tikuyenera kuwathokoza chifukwa cha dziko lapansi lokongolali, chakudya, zovala, ndi zinthu zina.

  2. Tikuyenera kuwathokoza chifukwa cha ziphunzitso zawo komanso chifukwa cha luso lathu lophunzira zambiri za Iwo.

  3. Tikuyenera kuwathokoza chifukwa cha banja lathu, abwenzi athu, thanzi lathu labwino komanso ntchito yathu.

Kenako timawapempha zinthu zimene timafunikira. Izi ndi zina mwa zinthu zomwe tingafune kuwapempha Iwo:

  1. Tikhonza kuwapempha kuti atithandize kudziwa kuti ndi zinthu ziti zimene zili zoona komanso zimene siziri zoona.

  2. Tikhonza kuwapempha kuti atiteteze, ifeyo ndi achibale athu komanso anzathu.

  3. Tikhonza kuwapempha kuti atithandize kuchita zimene iwo amafuna kuti tichite.

  4. Tikhonza kuwapempha kuti atithandize kusankha zinthu zabwino.

  5. Tikhonza kuwapempha kuti atithandize kulapa machimo athu.

  6. Tikhonza kuwapempha kuti atithandize kupeza chakudya chokwanila patsiku.

  7. Tikhonza kuwapempha kuti atithandize kuthetsa mavuto athu.

  8. Tikhonza kuwapempha kuti athandize achibale kapena anzathu kuthetsa vuto lililonse limene ali nalo.

Tikuyenera kumaliza pemphero lathu ndi kunena kuti, “Mudzina la Yesu Khristu, ameni.” Izi zimatithandiza kukumbukira kuti Yesu ndi Mpulumutsi wathu. Yesu amagwira ntchito motsogozedwa ndi Atate athu Akumwamba kuti atithandize pa zinthu zonse zimene timafunikira. Tikuyenera kunena dzina la Yesu mwaulemu.

Zokambirana

  • Tikamalankhula ndi Atate athu Akumwamba, timayamba bwanji?

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene tingathokoze?

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene tingapemphe?

  • Kodi timanena chiyani tikamaliza kuyankhula ndi Atate athu Akumwamba?

Atate athu Akumwamba Amatiyankha Nthawi Zonse

Tingakhale otsimikiza kuti Atate athu Akumwamba amatimvera. Iwo amadziwa zinthu zimene zili zabwino kwambiri kwa ife. Iwo ndi wokonzeka nthawi zonse kutithandiza.

Nthawi zambiri Atate athu Akumwamba amatumiza yankho kudzera mwa Mzimu Woyera. Mzimu Woyera umatithandiza kumvetsa zinthu zimene tikuyenera kudziwa ndi kuchita. Nthawi zina Mzimu Woyera umamulimbikitsa munthu wina kuti atithandize.

Tikuyenera kukhala ofunitsitsa kuvomereza mayankho a Atate athu Akumwamba. Mwina sangatipatse zinthu zimene tapempha. Mwina sangatiyankhe mmene timayembekezera. Koma amadziwa zimene zili zabwino kwa ife.

Zokambirana

  • Kodi Atate athu Akumwamba amatiyankha bwanji?

  • Ndichifukwa chiyani samatipatsa nthawi zonse zinthu zimene timapempha?

Timakhala Anthu Abwino Popemphera

Mwina sitingadziwe zinthu zoyenera kuchita. Tikhonza kuchita mantha. Mwina sitingadziwe mmene tingathetsere mavuto athu. Mwina sitingadziwe kuti ndi zinthu ziti zomwe zili zoona komanso zomwe sizowona. Titha kudziwa zinthu zoyenera kuchita koma kukhala osalimba mokwanira kuti tizidzichita.

Tikamalankhula ndi Atate athu Akumwamba nthawi zambiri, amatithandiza pamavuto athu. Iwo amatithandiza kudziwa ndi kuchita zinthu zoyenera. Tikadziwa ndi kuchita zinthu zabwino, timakhala anthu abwino. Timakhala ngati Atate athu Akumwamba.

Zokambirana

  • Kodi timakhala bwanji anthu abwino tikamalankhula ndi Atate athu Akumwamba?

Print