Zofunikira Zoyambirira
Mutu 1: Mulungu Aliko


Mutu 1

Mulungu Aliko

Nthawi zina anthu amadzifunsa kuti: Kodi kuli Mulungu? Ngati kuli Mulungu, kodi Iye ndi wotani? Ine ndingadziwe bwanji za Iye?

Zinthu Zambiri Zimatisonyeza Kuti Mulungu Aliko

Tikayang’ana zinthu zodabwitsa pa dzikoli, timadziwa kuti pali wina wake wanzeru ndi wabwino amene adakonza ndi kuzipanga. Usiku, tikamaona nyenyezi ndi mapulaneti ambiri nthawi zonse zikuyenda m’malo ake oyenera, timadziwa kuti pali wina wake amene ali ndi mphamvu zazikulu amene adazipanga ndi kumazilamulira. Mulungu ndi amene adalenga zinthu zonsezi.

Pali anthu ena abwino amene adaona ndi kuyankhula ndi Mulungu. Iwo adatiuza m’mene Mulungu aliri ndi zimene amafuna kuti tidzichita. Iwo adatiuza ife kuti Iye ndi Atate athu Akumwamba. Iwo adalemba mabuku opatulika kuti tiphunzire za Iwo.

Aliyense waife atha kudziwa kuti kuli Mulungu komanso kuti ndi Atate athu Akumwamba. Iwo adzatithandiza kudziwa kuti Iwo ndi Enieni komanso kuti tikhonza kuwadziwa bwino.

Zokambirana

  • Kodi ndizinthu ziti zimene zimasonyeza kuti kuli Mulungu?

Atate athu Akumwamba Ndi Munthu Wangwiro

Anthu abwino amene adaona Atate athu Akumwamba adanena kuti Iwo ndi Enieni. Iwo alimoyo. Iwo Amaoneka ngati munthu.

Atate athu Akumwamba sifano kapena nyama. Ali ndi thupi la mnofu ndi mafupa. Thupi lawo limaoneka ngati thupi la munthu, koma ndi losiyana ndi lamunthu.

Thupi lawo silidzafa. Thupi lawo silimva ululu ndipo silingadwale.

Ali ndizomvelera. Amatha kumva chimwemwe kapena chisoni. Iwo amakonda anthu onse ndipo amafuna kuti adzikhala osangalala. Iwo ndi Achifundo komanso Achilungamo. Amangochita zabwino zokhazokha, ndipo amanena zoona zokhazokha. Iwo amadziwa zinthu zonse. Iwo amatha kuchita zinthu zonse. Pali kuwala powazungulira Iwo. Kuwala kwawo ndi kukongola kwawo ndi kwakukulu kuposa zonse zomwe tidaziwonapo.

Atate athu Akumwamba ndi okhawo amene tiyenera kuwalambira. Iwo amakhala m’malo otchedwa kumwamba. Ndi malo okongola kwambiri kuposa dziko lapansi.

Zokambirana

  • Kodi Mulungu ndi munthu wotani?

  • Kodi Mulungu ndi wosiyana bwanji ndi ife?

Atate athu Akumwamba Amasonyeza Kuti Amatikonda M’njira Zambiri

Atate athu Akumwamba amagwiritsa ntchito mphamvu zawo kutithandiza ife. Iwo adapatsa Mwana Wawo, Yesu, kulenga kumwamba ndi dziko lapansi. Adauza Yesu kupanga dzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi. Iwo adauza Yesu kuti aike zomera ndi nyama padziko lapansi. Atate athu Akumwamba adatichitira zinthu zonsezi chifukwa amatikonda. Amafuna kutithandiza kuti tikhale abwino komanso osangalala.

Atate athu Akumwamba amagwiritsa ntchito chidziwitso chawo kuti atithandize. Iwo amadziwa zonse zimene zidachitika m’mbuyomu. Iwo amadziwa zonse zimene zikuchitika panopa. Ndipo akudziwa zimene zidzachitike m’tsogolo. Iwo amadziwa maganizo a tonsefe. Popeza amadziwa zinthu zonse, amadziwa zimene timafunikira kuti tikhale osangalala. Amadziwa kuti, kuti tikhale osangalala tikuyenera kukhala abwino. Iwo amafuna kutithandiza kukhala abwino chifukwa amatikonda.

Zokambirana

  • Kodi Atate athu Akumwamba amasonyeza bwanji kuti amatikonda?

Atate athu Akumwamba Amafuna Kuti Tiwadziwe

Chifukwa chakuti Atate athu Akumwamba amatikonda, adatipatsa moyo komanso dziko lapansi lokongola kuti tidzikhalamo. Iwo amafuna kuti tidziŵe zinthu zimene tiyenela kuchita. Iwo adatilonjeza kuti tikhonza kuwadziwa.

Kuchita zimenezi kutha kutithandiza kuphunzira zambiri za Atate athu Akumwamba:

  1. Titha kuyang’ana dziko limene Iwo adalenga ndikukhala oyamika.

  2. Titha kukhulupilira kuti Atate athu Akumwamba ndi Enieni komanso amatikonda.

  3. Titha kuwerenga zinthu zimene anthu abwino adalemba zokhudza Atate athu Akumwamba.

  4. Titha kuphunzira ndikuchita zimene Iwo amafuna kuti tiphunzire ndi kuchita.

  5. Titha kuyankhula ndi Atate athu Akumwamba ndi kuwapempha kuti atithandize kuwadziwa.

Kudziwa za Atate athu Akumwamba kutha kutithandiza pa moyo wathu. Kudziwa za Iwo kutha kutithandiza kukhala osangalala komanso otetezeka. Iwo ndi abwino ndipo sadzachita zinthu zoipa kwa ife. Titha kuphunzira zinthu zimene Iwo amafuna kuti tidzichita. Titha kuphunzira mmene tingapemphere thandizo lawo. Titha kukhala anthu abwino komanso osangalala.

Zokambirana

  • Kodi tingatani kuti tidziwe ndi kumvetsetsa Atate athu Akumwamba?

  • Kodi kudziwa Atate athu Akumwamba kungatithandize bwanji?

Print