Zofunikira Zoyambirira
Mutu 2: Moyo Wathu Kumwamba


Mutu 2

Moyo Wathu Kumwamba

Kodi tidali kukhala kuti tisadabadwe padziko lapansi? Tidatani kumeneko?

Aliyense wa Ife Ndi Mwana wa Atate athu Akumwamba

Tisadabadwe padziko lapansi, tidali kukhala kumwamba. Kumwamba kwathu kudali kodabwitsa komanso kokongola kwambiri kuposa chirichonse padziko lapansi. Tidali a m’banja kumeneko. Tinkakondana komanso tinkasangalala. Atate athu Akumwamba adali Atate amizimu yathu, ndipo pachifukwa ichi nthawi zambiri timawatcha Atate Akumwamba. Chifukwa chakuti ndi Atate athu, amatikonda ndipo amatisamalira.

Munthu aliyense amene amakhala padzikoli adali m’bale kapena mlongo wathu wakumwamba. Mwana wamkulu m’banja lathu lakumwamba adali Yesu Khristu.* Iye ndim’bale wathu wamkulu.

Pamene tidali kumwamba tidalibe matupi anyama ndi mafupa ngati amene tili nawo masiku ano. Tidali mizimu. Mzimu uli ndi mawonekedwe ofanana ndi a munthu. Monga mizimu, tinkakhonza kuyankhulana, kuyendayenda, kupanga zisankho, ndikudziŵa kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choipa.

Sitidali ofanana kumwamba. Tidali osiyana, monga m’mene tiliri tsopano. Tidali ndi zilakolako ndi maluso osiyanasiyana. Tidaphunzira kugwiritsa ntchito luso lathu m’njira zosiyanasiyana.

Zokambirana

  • Kodi kwathu kumwamba kudali kotani?

  • Kodi Atate athu adali ndani?

  • Kodi mchimwene wathu wamkulu adali ndani?

Atate athu Akumwamba Adadziwa Kuti Titha Kukhala ngati Iwo

Popeza Atate athu Akumwamba ndi Atate amizimu yathu, amatidziwa bwino kwambiri. Iwo adatikonda ife. Iwo ankadziwa kuti tidalandira kuchokera kwa Iwo kuthekera kwa kuphunzira zinthu zimene amadziwa komanso kukhala ngati Iwo. Iwo amafuna kuti nthawi zonse tikhale abwino monga m’mene iwo aliri. Amafuna kutithandiza kukulitsa kuthekera kwathu kokhala ngati Iwo.

Zokambirana

  • Kodi Atate athu Akumwamba amamva bwanji za ife, ndipo amatifunira chiyani cha ife?

  • Kodi zimakupangitsani kumva bwanji kudziwa kuti muli ndi Atate Akumwamba?

Image
Tisanakhalepo, ndi Jerry Harston

Tisadabwere padziko lapansi, tidali kukhala kumwamba.

Atate athu Akumwamba Adakonza Dongosolo loti Atithandize

Kumwamba tidaphunzira zinthu zambiri ndipo tidasintha mwamomwe tikadathera, koma padali zinthu zimene sitikadatha kuphunzira ndi kuchita kumeneko. Atate athu Akumwamba adakonza dongosolo loti tiphunzire zambiri.

Adatiyitanira kumsonkhano kumwamba. Tonse tidali kumeneko. Iwo adafotokoza dongosolo lawo lotithandiza kuphunzira ndipo adatiuza kuti ngati titsatira dongosolo lawo tidzakhala ngati Iwo.

Atate athu Akumwamba adati adzapanga dziko lapansi, limene tidzakhalapo kwa kanthawi. Padziko lapansi, sitidzakumbukira moyo wathu ndi Iwo kumwamba. Tikhonza kusankha zinthu zabwino kapena zoipa. Ili lidzakhala yesero loona ngati tingamvere Atate athu Akumwamba pamene tili opanda Iwo.

Malingana ndi dongosolo la Atate athu Akumwamba, aliyense adzalandira thupi la mnofu ndi mafupa. Tidzafunika thupi lotere kuti tiphunzire zinthu zimene Iwo amadziwa ndi kuchita zimene amachita. Pambuyo pake, tidzafa, ndipo mizimu yathu idzasiya matupi athu a mnofu ndi mafupa. Koma mizimu yathu idzalumikizananso ndi matupi athu, ndipo sitidzafanso. Iwo amene adzachite zimene Atate athu Akumwamba adatiuza kuti tichite adzabwelera kukakhala nawo kwamuyaya.

Tidaphunzira kuti aliyense adzakhala ndi mavuto pa dziko lapansi, monga matenda, zowawa, chisoni, ndi imfa. Koma tidazindikira kuti tidzaphunzira pa zinthu zimenezi. Mavuto amenewa adzatha kutiphunzitsa kukondana ndi kuthandizana.

Atate athu Akumwamba adzasankha nthawi ndi malo kuti aliyense waife abadwe padziko lapansi. Iwo ankadziwa kumene angatumize aliyense waife kuti akaphunzire zinthu zimene tiyenera kudziwa. Tonse tidzakhala ndi mwayi wochita zinthu zosiyanasiyana. Atate athu Akumwamba ankafuna kuti tidzachite zinthu zabwino komanso kuti tidzabwelere kwa Iwo. Komabe, sangatikakamize kuchita chirichonse.

Ena a ife tidzatha kusankha kuwamvera. Ngati tidzawamvera, tidzakhala ngati Iwo ndikubwelera kukakhala ndi Iwo. Ena a ife tidzatha kusankha kusawamvera. Ngati sitidzawamvera, sitingathe kudzakhala ngati Iwo ndipo sitidzatha kubwelera kukakhala nawo.

Pamene tidamva dongosolo la Atate athu Akumwamba laife, tidali okondwa kwambiri. Tinkafuna kuti tithe kuphunzira ndi kukula. Aliyense amene adakhala pa dziko lapansi adavomera kukhala ndi moyo mogwirizana ndi dongosolo lawo.

Zokambirana

  • Kodi dongosolo la Atate athu Akumwamba lidali lotani kwa ife?

  • Ndi chifukwa chiyani tidafunikira kuchoka kumwamba?

  • Kodi Atate athu Akumwamba adafuna kuti tichite chiyani pa dziko lapansi?

Print