Zofunikira Zoyambirira
Mutu 26: Kuona mtima


Mutu 26

Kuona mtima

Atate athu Akumwamba ndi Oona mtima muzonse zimene amachita. Kodi amafuna kuti ifenso tikhale oona mtima?

Atate athu Akumwamba Amatiuza Kuti Tizikhala Oona Mtima Pazochita Zonse

Kukhala oona mtima kumatanthauza kunena zoona. Kukhala oona mtima kumatanthauza kusanama kapena kuba. Tikamanena zinthu zabodza, tikunama. Tikamanena mbali imodzi yokha ya choonadi, tikunama. Tikamatsogolera anthu kukhulupilila zinthu zabodza, sitikhala oona mtima.

Kuba ndiko kutenga chinthu cha munthu wina popanda chilorezo cha munthuyo. Kutenga chinthu m’sitolo osalipira ndi kuba. Atate athu Akumwamba atiuza kuti tisabe.

Anthu oona mtima amagwira ntchito mwakhama pa maola onse amene amalipidwa. Olemba ntchito oona mtima amalipira amene amawagwirira ntchito mogwirizana ndi zimene antchitowo akuwayenelera. Anthu oona mtima amalipiritsa mwachilungamo pa ntchito zawo ndi zinthu zimene amagulitsa. Tikuyenera kukhala oona mtima ngati tikufuna kukhala ndi Atate athu Akumwamba.

Satana amayesa kutinyengelera kuti tikhale osaona mtima. Tikakhala osaona mtima m’njira iliyonse, timatsatira Satana. Satana amakonda bodza. Satana amafuna kuti tiziganiza kuti kusaona mtima n’kwanzeru. Iye amayesa kutipangitsa kuganiza kuti tidzakhala osangalala tikachita kusaona mtima. Amafuna kuti tiziganiza kuti kusaona mtima si tchimo. Satana amafuna kuti tikhale osaona mtima kuti tikhale osasangalala.

Atate athu a Kumwamba atiphunzitsa kukhala oona mtima nthawi zonse. Iwo amakhumudwa tikamanama. Iwo amafuna kuti tidziŵe kuti kunama n’kulakwa nthawi zonse. Kusaona mtima nthawi zonse n’kulakwa ndipo kumatipangitsa kusasangalala.

Anthu ena amaba zinthu chifukwa choganiza kuti ali ndi ufulu wokhala nazo. Achinyamata ena amabera kusukulu kuti apambane bwino kapena chifukwa choti ophunzira ena amabera. Anthu ena amanama kuti ena aziwaganizira bwino. Palibe chimodzi mwa zifukwa zimenezi chimene chimachititsa kuba kapena kunama kukhala koyenera. Tikamapereka zifukwa zonama, sitikhala oona mtima.

Zokambirana

  • Kodi kuona mtima ndi chiyani?

  • Kodi timatsatira ndani tikakhala oona mtima?

Tikhonza Kukhala Oona Mtima pa Zonse Zimene Timachita

Tikhonza kukhala oona mtima pokhala olimba mtima kuti tinene zoona, ngakhale zitakhala zovuta. Atate athu Akumwamba adzatithandiza kukhala oona mtima tikawapempha. Iwo adzatumiza Mzimu Woyera kuti utithandize ife kusankha kukhala oona mtima. Mzimu Woyera udzatithandiza kudziwa kuti kukhala oona mtima ndi chinthu choyenera kuchita.

Tikamvetsetsa ziphunzitso za Yesu, tidzafuna kukhala oona mtima pa zonse zimene timachita. Yesu watiphunzitsa kuti ndife ana a Atate athu Akumwamba ndipo tonse ndife abale ndi alongo. Iye watiphunzitsa kuti tingakhale osangalala ngati tiri oona mtima. Sitingakhale mwamtendere ngati tiri ndi chinachake m’nyumba mwathu chomwe sichathu. Iye watiphunzitsanso kuti ngati tikhala ndi chikhulupiliro mwa iye, kulapa, ndi kukhala oona mtima moona mtima tingabwelere kukakhala ndi Atate athu Akumwamba ndi kukhala osangalala kwamuyaya.

Tikamvetsetsa zinthu zonsezi, timayamba kufuna kukhala oona mtima. Sitikufuna kunamiza anthu ena. Tikufuna kukondweretsa Atate athu Akumwamba kuti tibwelere kukakhala ndi Iwo. Timafuna kuvomereza zolakwa zathu ndi kukonza kuti Atate athu Akumwamba atikhululukire.

Zokambirana

  • Ngati tanama ngakhale pang’ono, n’chifukwa chiyani tiyenera kulapa?

  • Kodi tingatani kuti tikhale oona mtima m’zonse zimene timachita?

  • Kodi Atate athu Akumwamba angatithandize bwanji kukhala oona mtima?

Kukhala Oona Mtima Kumatipatsa Chimwemwe

Tikakhala oona mtima timamva bwino. Atate athu Akumwamba amasangalala nafe. Sitidziona kuti ndife olakwa. Timamva bwino chifukwa timadziwa kuti palibe chimene tingabisire ena. Sitiyenera kuda nkhawa kuti wina angadziwe kuti tanama.

Tikakhala oona mtima timakhala ngati Atate athu Akumwamba. Tikudziwa kuti tikukonzekera kubwelera kukakhala nawo. Tikakhala oona mtima, anthu ena amatikhulupilira. Tikakhala oona mtima, Atate athu Akumwamba adzatithandiza kuchita zinthu zabwino.

Zokambirana

  • Kodi timamva bwanji tikakhala oona mtima?

  • Kodi dziko likadakhala lotani ngati aliyense akadakhala woona mtima?

Print