Zofunikira Zoyambirira
Mutu 13: Chikhulupiliro mwa Yesu Khristu


Image
Kuchiritsa munthu wakhungu, wolemba Carl Heinrich Bloch

Wakhunguyo adali ndi chikhulupiliro kuti Khristu amuchiritsa.

Mutu 13

Chikhulupiliro mwa Yesu Khristu

Kodi tingakhulupilire bwanji Yesu Khristu ngakhale kuti sitidamuone?

Titha Kukhulupilira Yesu Khristu ndi Kumudalira

Kukhala ndi chikhulupiliro kumatanthauza kuti timakhulupilira munthu kapena chinthu chimene sitichiona, ndipo timachita zinthu mogwirizana ndi chikhulupilirocho. Mwachitsanzo, mlimi amakhulupilira kuti mbewu zimamera ngati atabzala ndi kuzisamalira. Chotero amabzala mbewu ndi kuzithilira ndi kuzisamalira. Akachita zimenezi, zomerazo zimakula n’kumupatsa chakudya.

Kukhala ndi chikhulupiliro mwa Yesu kumatanthauza kuti timakhulupilira kuti ali ndi moyo ndipo timamumvera, ngakhale sitikumuwona. Izi ndi zina mwa zinthu zomwe timakhulupilira za Yesu tikakhala ndi chikhulupiliro mwa Iye:

  1. Timakhulupilira kuti Atate athu Akumwamba adasankha Yesu kuti atithandize kutsatira dongosolo la Atate athu Akumwamba.

  2. Timakhulupilira kuti Yesu ndi Mpulumutsi wathu.

  3. Timakhulupilira kuti Iye adabadwa mu dziko lino ngati Mwana wa Atate athu Akumwamba.

  4. Timakhulupilira kuti Iye adabwera padziko lapansi kudzatiphunzitsa mmene tingabwelelere kwa Atate athu Akumwamba.

  5. Timakhulupilira kuti amatikonda.

  6. Timakhulupilira kuti adazunzika chifukwa cha machimo athu kuti tilape komanso kuti tisalangidwe chifukwa cha machimowo.

  7. Timakhulupilira kuti Iye adafa ndipo adaukitsidwa.

  8. Timakhulupilira kuti ziphunzitso Zake ndi zoona.

  9. Timakhulupilira kuti ngati timvera Yesu tikhonza kubwelera kukakhala ndi Atate athu Akumwamba.

Kukhala ndi chikhulupiliro mwa Yesu Khristu ndikofunikira pakubwelera kwathu kwa Atate athu Akumwamba. Tikakhala ndi chikhulupiliro mwa Iye, timam’khulupilira ndi kufuna kuphunzira za Iye. Yesu ndi yekhayo amene angatitsogolere kuti tibwelere kwa Atate athu Akumwamba. Ndi okhawo amene akhulupilira Yesu ndi kumvera Iye akhonza kubwelera ndi kukakhala ndi Atate athu Akumwamba.

Zokambirana

  • Kodi chikhulupiliro ndi chiyani?

  • Kodi chikhulupiliro mwa Yesu ndi chiyani?

  • Kodi zina mwa zinthu zimene timakhulupilira zokhudza Yesu ndi ziti?

  • Ndi chifukwa chiyani tifunika kukhala ndi chikhulupililo mwa Yesu Khristu?

Yesu Adatipatsa Njira Yokulitsira Chikhulupiliro mwa Iye

Yesu adatiuza mmene tingaphunzilire za Iye ndi kukhala ndi chikhulupiliro mwa Iye. Iye watiuza kuti tiziwerenga malemba ndi kuphunzira zimene aneneri adalemba zokhudza Iye. Iye watipempha kuti tizimvera mneneri amene ali ndi moyo masiku ano. Tikamachita zimenezi, timaphunzira zambiri za Yesu.

Pamene tikuphunzira za Yesu, tikuyenera kupemphera. Tikuyenera kupempha Atate athu Akumwamba kuti Atithandize kumvetsa zimene timawerenga komanso kumva zokhudza Yesu. Atate athu Akumwamba Adzatumiza Mzimu Woyera kuti utithandize kumvetsa zinthu zimene tikuphunzira. Mzimu Woyera udzatiuza kuti Yesu ndi Mwana wa Atate athu Akumwamba, kuti Iye ndi Mpulumutsi wathu, ndi kuti ziphunzitso zake ndi zoona.

Mneneri wina dzina lake Alima adanena kuti ngati tikufuna kudziwa ngati chinachake chili choona, tikuyenera kuchiyesa. Iye adayerekezera zimenezi ndi kubzala mbewu. Ngati tibzala mbewu yabwino ndi kuisamalira, imakula, ndipo tidzadziwa kuti inali mbewu yabwino. Ngati mbeuyo siikula, tidzadziwa kuti inali mbewu yoipa. Ngati tikufuna kudziwa ngati zimene Yesu ankaphunzitsa n’zoona, tikuyenera kuziphunzira komanso kuzitsatira.

Kukhulupilira mwa Yesu kumatanthauza zambiri osati kungonena kuti timamukhulupilira. Kumatanthauza kumudalira kwambiri moti timafuna kumumvera pa chilichonse chimene Iye amatilamula kuchita. Ndi okhawo amene amamvera Yesu amene ali ndi chikhulupiliro chenicheni mwa Iye. Ndipo tikamamumvera, chikhulupiIiro chathu mwa Iye chimalimba. Timaphunzira kuti ziphunzitso zake zimachokera kwa Atate athu Akumwamba, osati kwa anthu.

Ngati sitimvera Yesu, chikhulupiliro chathu chimakhala chofooka. Tikamachita zimene iye amatilamula, chikhulupiliro chathu chimakhala cholimba. Chikhulupiliro chathu chingapitilire kukhala champhamvu kufikira titadziŵa motsimikizirika kuti ali moyo, monga ngati kuti tikumuona.

Zokambirana

  • Kodi tingakhale bwanji ndi chikhulupiliro mwa Yesu ngakhale sitikumuona?

  • Ndi chifukwa chiyani tikuyenera kumvera Yesu kuti tikhale ndi chikhulupiliro mwa Iye?

Tikhonza Kulandira Chidziŵitso Chachikulu ndi Mphamvu Tikakhala ndi Chikhulupiliro mwa Yesu

Aneneri amene timawawerenga m’Malemba ankakhulupilira kwambiri Yesu. Chikhulupiliro chimenechi chinawapatsa mphamvu yothandiza anthu awo. Popeza adali ndi chikhulupiliro mwa Yesu, adali ndi mphamvu zochita zinthu zimene sakanatha mwaokha.

Yesu asadabadwe padziko lapansi, Atate athu Akumwamba adamulangiza kuti auze mneneri Nowa kuti amange chombo chifukwa Atate athu Akumwamba adzatumiza chigumula ngati anthu oipa a m’nthawi ya Nowa sadalape. Anthu sadalape. Nowa adakhulupilira Yesu ndipo adamanga chombo. Pamene chigumula chidadza, anthu onse amene sadalape adaphedwa; Koma Nowa ndi banja lake adapulumuka m’chombomo chifukwa chakuti adakhulupilira Yesu ndi kuchita zimene Iye adanena.

Mose adali mneneri amene adatulutsa anthu ake muukapolo. Atate athu Akumwamba adatumiza Yesu kuti akathandize Mose chifukwa Mose ankakhulupilira Yesu ndipo adachita zimene Yesu adamuuza.

Pamene Yesu adali padziko lapansi, mzimayi wina adam’khulupilira kwambiri. Iye adadwala kwa nthawi yaitali, ndipo adakhulupilira kuti ngati atagwila chabe chobvala cha Yesu, iye adzachila. Yesu adali kuyenda m’khamu la anthu. Iye adadzikankhira m’chikhamu cha anthuwo kwa Iye ndi kugwira zobvala zake. Iye adachiritsidwa nthawi yomweyo. Yesu adamuuza kuti chikhulupiliro chake chamuchiritsa.

Mneneri Joseph Smith adali ndi chikhulupiliro mwa Yesu Khristu. Iye adawerenga m’Baibulo kuti Atate athu akumwamba adzayankha mapemphero athu ngati tikhulupilira kuti Iye adzatero. Joseph adapemphera kwa Atate athu Akumwamba. Atate athu Akumwamba ndi Yesu adaonekera kwa Joseph. Atate athu Akumwamba adauza Joseph kuti amvere Yesu ndi kumvera zimene Yesu adamuuza. Joseph adamvera Yesu, choncho adatha kulandira Buku la Mormoni ndi kuthandiza kubwenzeretsa Mpingo wa Yesu Khristu.

Yesu adzatithandizanso ngati tiri ndi chikhulupiliro mwa Iye. Iye adzatithandiza pa mavuto athu. Adzatithandiza ngati takhumudwa. Iye adzatithandiza kugonjetsa uchimo. Tidzatha kuthandiza mabanja athu komanso anthu ena.

Tikakhala ndi chikhulupiliro mwa Yesu, timayamba kutsatira dongosolo la Atate athu Akumwamba. Timayamba kukhala ndi moyo ndikuchita zinthu zomwe zidzatitsogolera kubwelera kwa Atate athu Akumwamba. Ngati tipitiriza, tsiku lina tidzatha kukhala ndi Iwo kwamuyaya.

Zokambirana

  • Kodi tingakhale ndi chidziwitso ndi mphamvu zotani tikakhala ndi chikhulupiliro mwa Yesu?

Print