Zofunikira Zoyambirira
Mutu 27: Mawu a Nzeru


Mutu 27

Mawu a Nzeru

Amodzi mwa madalitso aakulu amene Atate athu Akumwamba atipatsa ndi matupi athu amnofu ndi mafupa. Iwo atipatsa lamulo la thanzi kuti litithandize kusamalila matupi athu. Kodi mukudziwa chiyani za lamulo la thanzi?

Matupi Athu Ndi Opatulika

Chifukwa chimodzi chofunika kwambiri chobwera padziko lapansi ndicho kudzalandira matupi a mnofu ndi mafupa. Timafunika matupi kuti tikhale ngati Atate athu Akumwamba. Ndi matupi a mnofu ndi mafupa okha amene tingaphunzire zinthu zimene tikuyenera kudziwa kuti tikhale ngati Iwo. Tikhonza kukhala ndi ana. Tikhonza kulandira miyambo yofunikira kuti tibwelere kukakhala ndi Atate athu Akumwamba. Popanda matupi sitikadatha kuchita izi.

Chifukwa mizimu yathu imakhala m’matupi athu, thupi ndi lopatulika. Tikakhala ndi chikhulupiliro mwa Yesu Khristu ndikuyesera kumvera Iye, Atate athu Akumwamba amatumiza Mzimu Woyera kuti ukhale nafe. Mzimu Woyera sangakhale nafe ngati tiri osamvera komanso osasamalira matupi athu.

Tikafa, mizimu yathu imasiya matupi athu. Pomwe Yesu adafa, mzimu wake udachoka m’thupi lake. Patapita masiku atatu, mzimu wake udalowanso m’thupi lake ndipo adaukitsidwa. Yesu adali ndi mphamvu yakuuka kwa akufa; ndipo chifukwa cha nsembe yake kwa ife, ifenso tidzaukitsidwa tikadzafa. Mizimu yathu ndi matupi athu zidzasonkhanitsidwa pamodzi. Yesu ankadziwa kuti tifunika kukhala ndi matupi osafa mnofu ndi mafupa kuti tikhale ngati Atate athu Akumwamba ndi kukhala nawo kwamuyaya.

Atate athu Akumwamba amafuna kuti tizisamalira bwino matupi athu. Tikamasamalira bwino matupi athu, titha kukhala athanzi, amphamvu ndi kuchita zinthu zina zimene iwo amafuna. Tonsefe tiyenera kusankha kuti tizisamalira bwino matupi athu kapena kuchita zinthu zowavulaza. Timadziwa kuti matupi athu ndi ofunika m’moyo uno komanso ukatha moyo uno. Tikuyenera kuwasamalira bwino. Atate athu Akumwamba sasangalala tikapanda kusamalira matupi athu.

Makolo ndi amene akuyenera kuphunzitsa ana awo kuti matupi awo ndi mphatso yopatulika yochokera kwa Atate athu Akumwamba ndi kuwafotokozera chifukwa chake matupi awo ndi ofunika kwambiri. Ana akamvetsa chifukwa chake n’kofunika kusamalira matupi awo, sangafune kutsatira mayesero a Satana.

Zokambirana

  • Chifukwa chiyani tili ndi matupi amnofu ndi mafupa?

  • N’chifukwa chiyani matupi athu ndi opatulika?

  • N’chifukwa chiyani tikuyenera kuphunzitsa ana athu kufunika kosamalira matupi awo?

Atate athu Akumwamba Adatipatsa Lamulo Laumoyo

Atate athu Akumwamba atiuza zinthu zina zimene zili zabwino kwa matupi athu ndi zina zimene sizili bwino. Izi zalembedwa m’Malemba ndipo zimatchedwa Mawu a Nzeru.

Atate athu a Kumwamba adavumbulutsa Mawu a Nzeru kwa Mneneri Joseph Smith. Ndi lamulo. Tikuyenera kumvera lamuloli kuti tikhale ndi matupi ndi maganizo amphamvu.

Mawu a Nzeru amatiphunzitsa zomwe ziri zabwino kwa matupi athu. Tikuyenera kudya ndi kumwa zinthu zokhazo zomwe zili zabwino kwa matupi athu. Tikuyenera kudya zipatso, ndiwo zamasamba, ndi tirigu. Tikuyenera kudya zakudya zimenezi moyenera komanso tisamadye kwambiri. Sitikuyenera kudya nyama yambiri.

Zokambirana

  • Ndi zakudya ziti zomwe zili zabwino kwa matupi athu?

Atate athu Akumwamba atiuza Zomwe Siziri Zabwino Kwa Matupi Athu

Atate athu Akumwamba amadziwa kuti Satana adzayesa kutinyengelera kuti tigwiritse ntchito molakwika matupi athu. Atate athu Akumwamba adatiuza zinthu zina zimene siziri bwino ku matupi athu. Kumwa mowa sikwabwino ku thupi lathu. Atate athu Akumwamba adatilamula kuti tisamamwe mowa, zakumwa zoledzeretsa, ndi zakumwa zina zomwe ziri ndi mowa. Zinthu zimenezi zingayambitse matenda ndipo zingabweretse kupanda chimwemwe m’nyumba. Anthu akamamwa zinthu zimenezi sangathe kuganiza bwino. Zakumwa zimenezi nthawi zambiri zimachititsa anthu kusankha zinthu zoipa, kunama, kuwononga ndalama zawo zonse, ndiponso kuphwanya lamulo la kudzisunga. Mayi woyembekezera akamamwa zakumwa zoledzeretsa, akhoza kuvulaza mwana wosabadwayo. Anthu amene amamwa zakumwa zoledzeretsa amabweretsa mavuto aakulu.

Atate athu Akumwamba atiuzanso kuti fodya ndi wovulaza thupi lathu. Sitikuyenera kusuta kapena kutafuna fodya. Asayansi atsimikizira kuti fodya amayambitsa matenda ndipo akhoza kuvulaza ana osabadwa.

Atate athu Akumwamba atiuzanso kuti tisamwe khofi ndi tiyi. Sitikuyenera kumwa khofi ndi tiyi chifukwa ziri ndi mankhwala oopsa. Tisagwiritse ntchito mankhwala, kupatula mankhwala omwe madokotala amatipatsa.

Atate athu Akumwamba atiuza kuti mowa, fodya, ndi mankhwala zingatithandize ngati tidziŵa kuzigwilitsira ntchito bwino. Iwo adati mowa uyenera kugwiritsidwa ntchito posambitsa matupi athu okha. Fodya atha kugwiritsidwa ntchito pochiritsa mabala a ng’ombe zodwala. Nthawi zina mankhwala amatithandiza tikadwala. Koma tisanayese kugwilitsila ntchito zinthu zimenezi, tikuyenela kuphunzira kwa anthu anzeru zimene tikuyenela kugwilitsira nchito komanso mmene tingazigwilitsire nchito. Ngati tizigwilitsa ntchito molakwika, zikhoza kukhala zoopsa.

Tisalowetse m’matupi mwathu chirichonse chimene sichiri bwino kwa ife. Mawu a Nzeru amatiuza za zinthu zina zoipa kwambiri. Ndi lamulo lofunika.

Mawu a Nzeru samatiuza zonse zomwe sitiyenera kugwiritsa ntchito. Tikuyenera kuzindikira kuti chilichonse chimene chili chovulaza thupi kapena maganizo athu, ngakhale kuti sichidatchulidwe m’Mawu a Nzeru, sichikuyenera kugwiritsidwa ntchito. Tikuyenera kusamalira matupi athu m’njira zina, monga kuwasambitsa kaŵirikaŵiri kuti akhale aukhondo ndi kuchita maseŵera olimbitsa thupi ndi kupuma mokwanira.

Zokambirana

  • Kodi tikudziwa bwanji kuti zinthu zina si zabwino kwa thupi lathu?

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene sitikuyenera kuloŵetsa m’matupi athu?

  • Kodi kupuma ndi kuchita masewera olimbitsa thupi zikugwirizana bwanji ndi lamulo la thanzi la Atate athu Akumwamba?

  • Kodi matupi athu tiyenera kukhala aukhondo bwanji?

Madalitso Aakulu Amabwera Chifukwa Chomvera Mawu a Nzeru

Ngati timvera Mau a Nzeru, Atate athu Akumwamba adzadalitsa matupi athu kuti akhale amphamvu kuposa mmene akadakhalira tikapanda kumvera lamuloli. Tidzakhala okhonza bwino kugwira ntchito yawo pano padziko lapansi. Iwo adanena kuti tikamvera lamuloli tidzatha kuthamanga mosatopa ndi kuyenda osakomoka. Ili ndi dalitso lalikulu.

Atate athu Akumwamba adalonjezanso kutidalitsa ndi nzeru zazikulu ndi chidziwitso ngati timvera Mawu a Nzeru. Mzimu Woyera udzatiululira zinthu zambiri zofunika zomwe sitikadatha kuzidziwa. Satana sadzakhala ndi mphamvu pa ife. Ngati timvera Mawu a Nzeru, tidzakhala athanzi komanso tikukonzekera moyo wamuyaya* ndi Atate athu Akumwamba.

Zokambirana

  • Kodi ndi madalitso otani amene timapeza tikamamvera Mawu a Nzeru?

Print