Zofunikira Zoyambirira
Mutu 17: Otsatira a Yesu Khristu


Image
Abraham pa zidikha za Mamre, ndi Grant Romney Clawson

Abraham adachita pangano ndi Ambuye.

Mutu 17

Otsatira a Yesu Khristu

Otsatira a Yesu Khristu ndi osiyana ndi anthu ena. Kodi otsatira ake ndi ndani? Kodi amasiyanitsidwa bwanji?

Otsatira a Yesu Amakonda Atate athu Akumwamba

Otsatira a Yesu ndi anthu amene amamukhulupilira Ndi kumumvera. Amaphunzira dongosolo la Atate athu Akumwamba monga adaphunzitsidwa ndi Yesu ndipo amafuna kulitsatira. Amawakonda Atate athu Akumwamba ndipo amakhulupilira kuti iwo amawafunira moyo wabwino koposa. Amakhulupilira kuti Yesu ndi mwana wa Atate athu Akumwamba. Amakhulupilira kuti Yesu ndi Mpulumutsi wawo. Amakhulupilira kuti Yesu anapanga kuthekera kuti iwo azabwelere kukakhalanso ndi Atate athu Akumwamba. Amakhulupilira kuti potsatira Yesu yekha, ndikumvera malamulo Ake akhoza kukhululukidwa machimo awo ndikubwelera kwa Atate athu Akumwamba.

Amene amatsatira Yesu amayamika Mulungu ndi Yesu pa zimene Mulungu ndi Yesu adawachitira. Iwo amafuna kumumvera Yesu. Iwo amalapa machimo awo. Iwo amabatizidwa ndikulandira mphatso ya Mzimu Woyera. Iwo amazindikira kuti anthu onse ndi ofunika kwa Mulungu. Amayesetsa kuthandiza anthu ena m’njira iliyonse imene angathe.

Otsatira oona a Yesu amapanga malonjezano opatulika. Amalonjeza kwa Atate athu Akumwamba kuti azitchulidwa ndidzina la Yesu Khristu. Izi zikutanthauza kudziwika ngati membala wa Mpingo Wake, kuvomeleza ndikutsatira ziphunzitso zake zonse, ndi kumukumbukira nthawi zonse. Amalonjezanso kuti adzakonda anthu ena ndi kuwathandiza.

Atate athu Akumwamba amapanga malonjezano opatulika kwa otsatira a Yesu. Zina mwa zimene amalonjeza ndizoti:

  1. Kuwavomeleza ngati mamembala a Mpingo wa Yesu Khristu.

  2. Adzawapatsa mphatso ya Mzimu Woyera.

  3. Adzawathandiza kupeza zinthu zimene akusowekera.

  4. Adzawapatsa mphamvu Zawo kuti agwire ntchito Yake.

  5. Adzawapatsa madalitso aakulu tsopano ndi kwanthawi zonse.

  6. Kuwalora kuti azabwelere kukakhala ndi Iye ngati apitiliza kumvera Yesu.

Zokambirana

  • Kodi otsatira a Yesu amasiyana bwanji ndi anthu ena?

  • Kodi otsatira a Yesu amalonjeza kuchita chiyani?

  • Kodi Atate athu Akumwamba ndi Yesu amalonjeza kwa otsatira a Yesu?

Image
Mose aitana Aroni kuutumiki, ndi Harry Anderson

Mose anapereka unsembe kwa Aroni pomusanjika manja.

Yesu amapereka unsembe kwa mamembala oyenelera aamuna a mpingo

Yesu amapereka kwa amuna oyenera a mpingo ulamuliro womuthandiza Iye kuchita ntchito Yake. Ulamuliro umenewu umatchedwa unsembe. Atate athu Akumwamba adapereka ulamuliro umenewu kwa Yesu.

Kukhala ndi unsembe ndi dalitso lalikulu. Unsembe ndi ulamuliro opatulika. Ndi mamembala aamuna okha amene ali otsatira owona a Yesu ndipo akugwira ntchito mwakhama kusunga malamulo Ake, omwe amaloledwa kukhala ndi unsembe.

Pamene munthu ali ndi unsembe, amachita zinthu zimene Yesu amafuna kuti achite. Atha kuphunzitsa anthu ena za Atate athu Akumwamba ndi Yesu Khristu, kuwabatiza, ndikuwapatsa mphatso ya Mzimu Woyera. Mwamuna yemwe ali ndi unsembe, akhoza kudalitsa banja lake pamene akudwala komanso pamene ali ndi mavuto ena. Nthawi zonse anthu akakhulupilira Yesu ndikumvera malamulo ake, Yesu amawapatsa unsembe ndi madalitso ena.

Zokambirana

  • Kodi unsembe ndi chiyani?

  • Chifukwa chiyaniYesu amapereka unsembe kwa mamembala ake achimuna oyenera a mpingo?

Anthu ambiri adakhulupilira Yesu ndikutsatira malamulo ake asadabwere padziko lapansi

Adamu ndi Hava ndi ena mwa ana awo adakhulupilira Yesu ndikutsata malamulo ake asadabwere padziko lapansi

Atate athu Akumwamba adauza Adamu ndi Hava kuti akhulupilire Yesu Khristu ndikusunga malamulo Ake. Adauzidwa kuti tsiku lina adzabwela padziko lapansi. Adamu ndi Hava adalonjeza kuti adzamvera. Adasunga lonjezo lawo. Adabatizidwa, ndipo adalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

Yesu asadabwere padziko lapansi, adapereka unsembe kwa Adamu. Iye adalora kuti Adamu apereke unsembe kwa ana ake amene adamvera Yesu. Adamu adaika manja ake paMutu pa ana ake onse omvera ndipo adam’patsa unsembe. Pambuyo pake, ana a Adamu adapereka unsembe kwa ana awo m’njira yomweyo.

Zokambirana

  • Kodi Adamu ndi Hava adachita chiyani kuti akhale otsatira a Yesu?

  • Kodi otsatira a Yesu adalandira bwanji unsembe?

Abrahamu adadalitsa Yesu ndi kutsata malamulo Ake

Abrahamu ndi banja lake adakhulupilira mwa Yesu. Iwo adakhulupilira kuti Iye adzabwera padziko tsiku lina. Abrahamu adalonjeza Atate athu Akumwamba kuti adzamvera Yesu ndikuchita ntchito Yake. Atate athu Akumwamba adalonjeza Abrahamu kuti ngati angamvere, Atate athu Akumwamba adzamudalitsa iye ndi zidzikulu zake. Izi ndi zina mwa zinthu zimene Atate athu Akumwamba adalonjeza:

  1. Iwo adzapereka kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake unsembe.

  2. Iwo adzapereka kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake malo okhalamo.

  3. Iwo adzapatsa Abrahamu zidzukulu zambiri.

  4. Zidzukulu zochuluka za Abrahamu zidzakhala zotsatira Yesu.

  5. Zidzukulu zochuluka za Abrahamu zidzasankha kuchita ntchito Ya Yesu ndikuphunzitsa anthu ena za Atate athu Akumwamba ndi Yesu.

Abrahamu adaphunzitsa ana ake kukhulupiliraYesu ndi kumvera malamulo Ake. Abrahamu adapereka unsembe kwa mwana wake dzina lake Isake. Isake adapereka unsembe kwa mwana wake Yakobo. Potsatira pake, Atate athu Akumwamba adasintha dzina la Yakobo kukhala Israeli. Israeli adali ndi ana khumi ndi awiri. Adawaphunzitsa kukhulupilira Yesu ndi kumvera malamulo Ake. Iwo adali nawo unsembe. Zidzukulu za ana a Israeli zidatchulidwa mafuko khumi ndi awiri a Israeli.

Zokambirana

  • Kodi Atate athu Akumwamba adalonjeza chiyani kwa Abrahamu?

  • Kodi Israeli anali ndani?

Anthu a Israeli adakhulupiliraYesu ndikumvera malamulo Ake

Chifukwa kudalibe chakudya chokwanira kudziko lawo, Israeli ndi ana ake adapita kukakhala kudziko lotchedwa Igupto. M’kupita kwa nthawi, anthu amene ankakhala ku Igupto adapangitsa ana a Israeli kugwira ntchito molimbika. Adawakakamiza kukhala ku Igupto kuti akhale akapolo awo. Sadawalore kubwelera ku dziko limene Yesu adalonjeza kuwapatsa.

Patatha dzaka zambiri, Atate athu Akumwamba adasankha munthu otchedwa Mose kuti awatsogolere ana a Israeli kuchoka ku Igupto. Mose adagwiritsa ntchito mphamvu ya unsembe kuwathandiza kuti athawe kwa anthu aku Igupto. Adawatsogolera kupita kudziko kumene Yesu adawalonjeza kuti adzawapatsa. Dzikoli limatchedwa Kenani. Lidali ku zambwe kwa mtsinje wa Yolodani ndi Nyanja yakufa.

Zokambirana

  • Kodi ndimphamvu zanji zimene Mose adagwilitsa ntchito kuwathandiza anthu a Yesu kuti athawe ku Igupto?

Anthu a Israeli adasiya kukhulupilira mwa Yesu

Anthu a Israeli atakhala kudziko la Kenani kwa dzaka zambiri, iwo adasiya kukhulupilira mwa Yesu ndi kumvera malamulo Ake. Yesu adatumiza aneneri kuti awauze kuti alape ndi kumvera malamulo Ake. Yesaya, Eliya, ndi Yeremiya adali ena mwa aneneri amene Yesu adawatuma. Kudalinso aneneri ena ambiri.

Koma anthu aku Israeli sadalape. Kotero, Atate athu Akumwamba adalolera anthu ena kuti abwere kudzawalamulira ndi kulanda dziko lawo ndi kubalalitsa ambiri mwa iwo ku maiko ena. Izi zidapangitsa anthuwa kuti adzichepetse ndipo zidawayambitsa kukumbukira Yesu ndikumumvera Iye. KomaYesu asadabadwe ku Betelehemu, anthu a ku Israeli adayambiranso kuchita zoipa, ndipo Atate athu Akumwamba adalolera anthu otchedwa Aroma kuti agwire anthu a ku Israeli. Adalanda malo awo ndi nyumba zawo zopatulika.

Zokambirana

  • Kodi chidachitika ndi chani pamene anthu adaiwala malonjezano awo Kwa Atate athu Akumwamba ndi kusiya kumumveraYesu?

Yesu Adabwera Padziko Lapansi Ndi Kusonkhanitsa Otsatira Ake

Yesu atabwera padziko lapansi, adaphunzitsa anthu kuti iye ndi Mwana wa Mulungu. Iye adaphunzitsa kuti sadzavutika kwamuyaya chifukwa cha machimo awo ngati angamvere zimeneYesu ankaphunzitsa. Adawauza kuti akhulupilire mwa Iye ndikulapa. Iye adati iwo ayenera kubatizidwa. Iye adalonjeza kutumiza Mzimu Woyera kuti uwathandize. Adawaphunzitsa kukonda ndi kumvera Mulungu. Adawaphunzitsa kukonda anthu ena ndi kuwathandiza.

Anthu amene adakhulupilira Yesu ndi kumumvera adakhala otsatira Ake. Iye adasonkhanitsa anthu Ake mu gulu lotchedwa Mpingo wa Yesu Khristu. Adapereka unsembe kwa amuna amene adali atsogoleri ndi aphunzitsi mu Mpingo Wake.

Zokambirana

  • Kodi Yesu adathandiza bwanji anthu kuti amutsate Iye?

  • Kodi anthu adafunikira kuchita chiyani kuti akhale otsatira a Yesu?

Kukhala m’modzi wa otsatira a Yesu ndi Mwayi waukulu kwambiri

Amene amatsatira Yesu ndi osangalala. Iwo amadziwa dongosolo la Atate athu Akumwamba pa Iwo. Iwo amadziwa kuti Atate athu Akumwamba amawakonda iwo. Iwo amadziwa kuti Iye amafuna kuti iwo atsatire Yesu kuti Yesuyo awathandize kubwelera kwa Iye. Iwo amadziwa zinthu zimene ayenera kuchita kuti akhale osangalala. Iwo ali ndi mphatso ya Mzimu Woyera kuti aziwathandiza ndi kuwatonthoza iwo. Akakhala ndi mavuto, iwo amadziwa kutiYesu awathandiza. Iwo amadziwa kuti Mulungu adzawadalitsa chifukwa chokhala ndi chikhulupiliro chotsatira Yesu.

Amene amatsatira Yesu amayamika pa madalitso ambiri amene Atate athu Akumwamba amawapatsa. Iwo amathokoza Atate athu Akumwamba chifukwa cha madalitsowa pamene akupemphera.

Anthu amene Sali otsatira a Yesu akhonza kukhala otsatira Ake. Iwo akhonza kuphunzira za Iye powelenga mawu opatulika ndi kumvetsera kwa atsogoleri a Mpingo Wake. Iwo akhonza kukhulupilira mwa Iye, kulapa, ndi kubatizidwa. Akamumvera Yesu, Iwo akhonza kulandira zinthu zomwezo zimene Mulungu amakhala akuwalonjeza otsatira a Yesu.

Zokambirana

  • Kodi ndi chifukwa chiyani uli mwayi waukulu kwambiri kukhala m’modzi wa otsatira a Yesu?

Print