Zofunikira Zoyambirira
Mutu 22: Kumvera


Image
Ubatizo wa Khristu, ndi Greg Olsen

Yesu adasonyeza kumvera Atate Ake pa kubatizidwa.

Mutu 22

Kumvera

Atate athu Akumwamba adatiuza zinthu zimene tikuyenera kuchita kuti tikhale osangalala komanso kuti tibwelere kukakhala nawo. Kodi tingaphunzire bwanji kuchita zimenezi?

Atate athu Akumwamba Amatipatsa Malamulo Chifukwa chakuti amatikonda

Atate athu Akumwamba amafuna kuti tizisangalala padziko lapansi pano chifukwa amatikonda. Iwo amafunanso kuti tibwelere kwa Iwo kuti tikhale ndi chimwemwe chimene Iwo ali nacho. Tingachite zimenezi pokhapokha ngati titagwiritsa ntchito kuthekera kumene Iwo atipatsa kuti tifanane naye.

Atate athu Akumwamba amadziwa zimene tiyenera kuchita kuti tikhale ngati Iwo. Iwo atipatsa malamulo otiuza zimene tiyenera kuchita. Amatiuzanso zimene si zabwino kwa ife.

Lamulo lirilonse limene Atate athu Akumwamba apereka ndi la ubwino wathu ndipo lingatithandize. Malamulo amenewa akhonza kukhala malangizo kwa ife pa moyo wathu, ndipo ngati tiwatsatira tidzakhala osangalala.

Tonsefe timaphwanya malamulo a Atate athu Akumwamba. Chifukwa chakuti taphwanya malamulo a Atate athu Akumwamba, tachimwa. Chifukwa chakuti tachimwa, tinalekanitsidwa ndi Atate athu Akumwamba. Chilango choyenera cha machimo athu ndi chakuti ife tilekanitsidwe ndi Atate wathu Akumwamba kwamuyaya.

Koma Atate athu Akumwamba amatikonda. Iwo akonza njira yolipira ku chilango cha machimo athu. Iwo adatumiza Mwana wawo, Yesu kudzalipira chilango cha machimo athu. Yesu adalipira chilango chimenecho, ndipo ife tikhonza kubwelera kwa Atate athu Akumwamba mwa kukhala ndi chikhulupiliro mwa Yesu. Kukhala ndi chikhulupiliro mwa Yesu kumatanthauza kumudalira ndi kukhala otsatira ake omvera. Anthu amene amakhulupilira Yesu amamvera malamulo ake. Njira yoyamba yobwelera kwa Atate athu Akumwamba ndiyo kukhala ndi chikhulupiriro mwa Yesu, kuyesera mowona mtima kumvera Iye. Ndiye, ngati tipitiliza kukhala okhulupirika kwa Yesu, Iye adzatithandiza kumvera malamulo onse a Atate athu Akumwamba, ndipo Atate athu Akumwamba adzatikhululukira machimo athu.

Ena mwa malamulo a Yesu ndi a mamembala onse a Mpingo. Izi amazipereka m’malemba opatulika ndi kudzera kwa Aneneri Ake. Malamulo ena amatipatsa aliyense payekha, kudzera mwa Mzimu Woyera. Mwachitsanzo, malembo opatulika ndi aneneri amatiuza kuti mamembala onse a mpingo ayenera kuthandiza kuphunzitsa uthenga wabwino kwa ena. Koma Mzimu Woyera udzatiuza aliyense wa ife zomwe tingachite aliyense payekha kuti tiphunzitse uthenga wabwino kwa achibale athu, abwenzi, ndi oyandikana nawo. Ngati tiwerenga malemba, kumvera mawu a aneneri, ndi kutsatira kunong’oneza kwa Mzimu Woyera, tidzadziwa nthawi zonse zinthu zomwe tiyenera kuchita.

Zokambirana

  • Kodi malamulo a Atate athu Akumwamba ndi Yesu amaonetsa bwanji chikondi chawo pa ife?

  • Kodi tingadziwe bwanji zimene Atate athu Akumwamba ndi Yesu atiuza kuti tichite?

Lamulo Lirilonse la Atate athu Akumwamba Ndilofunika

Tiyenera kukhala ofunitsitsa kuchita chirichonse chimene Yesu amatilamula ife kuti tichite. Malamulo ake onse ndi ofunika ndipo amatithandiza kutikonzekeretsa kukhala ndi Atate athu Akumwamba. Baibulo limakamba nkhani ya mwamuna wina dzina lake Namani. Iye anadwala kwambiri ndipo ankafuna kuti mneneri wina dzina lake Elisa amuchiritse. Iye adachoka kunyumba kwake n’kupita kudziko limene Elisa ankakhala. Elisa adatumiza mthenga kukauza Namani kuti akasambe kasanu ndi kawiri mumtsinje wa Yorodano, ndipo adachira.

Namani adakwiya pamene adauzidwa kuti achite zimenezi. Adadzifunsa kuti n’chifukwa chiyani ayenela kupita ku Mtsinje wa Yorodano, popeza kumene adali kukhala kudali mitsinje ikuluikulu. Koma ngakhale kuti adakwiya, kenako Namani adasankha kumvera. Chifukwa adamvela, adachiritsidwa. Akadapanda kumvera, sakadachiritsidwa.

Anthu ena amaganiza kuti malamulo a Yesu ndi ovuta kuwatsatira. Pa nthawi ina padali mnyamata wina dzina lake Nefi, amene pamodzi ndi azichimwene ake adapemphedwa kuchita chinthu chovuta kwambiri. Yesu adawauza kuti abwerere ku mzinda wa Yerusalemu kuti akatenge malemba ofunika kwambiri. Abale ake adanena kuti sangachite izi. Zidali zovuta kwambiri. Koma Nefi adanena kuti adzachita monga Yesu adamuuzira iye kuti achite. Iye adanena kuti pamene Yesu watiuza kuti tichite chinthu, mosasamala kanthu kuti chikuwoneka chovuta chotani kwa ife, iye amatithandiza kuchichita.

Yesu adatiuza kuti tiyenera kuyesetsa kukhala monga Iye ndi Atate athu Akumwamba. Iye sakadatiuza ife kuchita izi pokhapokha Iye akadadziwa kuti ife tingakhoze kuchita ichi.

Yesu ali ngati Atate athu Akumwamba chifukwa sadachitepo tchimo. Tonse tidachimwa, koma titha kukhala ngati Atate athu Akumwamba kudzera mu chikhulupiliro mwa Yesu ndi kulapa.

Nthawi zina sitingamvetse chifukwa cha lamulo limodzi la Yesu. Koma ngati tikonda Yesu ndi kum’khulupilira, tidzachita zimene watiuza. Tidzamvera ngakhale kuti sitikumvetsa chifukwa chake watiuza kuchita zinazake. Adamu ndi Hava adachita izi. Yesu adauza Adamu ndi Hava kuti apereke nsembe* kwa Atate athu Akumwamba. Tsiku lina mngelo adafika kwa Adamu n’kumufunsa chifukwa chake ankapereka nsembe. Adamu adanena kuti sadadziwe chifukwa chake, koma Yesu adamuuza kuti achite zimenezo. Kenako mngeloyo adauza Adamu chifukwa cha lamulo ndipo adaphunzitsa Adamu uthenga wabwino. Yesu adasangalala ndi Adamu chifukwa Adamu adamumvera ngakhale asadadziwe chifukwa chimene adaperekera lamulolo.

Tiyenera kumvera malamulo a Yesu chifukwa timamukonda komanso timafuna kumumvera. Atate athu Akumwamba adanena kuti amasangalala ndi anthu amene amafuna kumvera Yesu. Iye amamva chisoni pamene ana ake samvera Yesu kufikira pachitika chinachake chimene chimawakakamiza kumvera. Atate athu a Kumwamba amafuna kuti ana awo onse aphunzire kukonda Yesu ndi kumumvera, chifukwa ndi njira yokhayo imene angabwelere kwa Atate athu Akumwamba.

Zokambirana

  • N’chifukwa chiyani kutsatila malamulo a Yesu n’kofunika ngakhale pamene akuoneka kuti ndi ovuta kuwatsatila?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera malamulo ngakhale kuti sitikuwamvetsa?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera chifukwa timafuna kumvera?

Tikamakonda Atate athu Akumwamba, Timafuna Kumvera Yesu

Yesu adachita zonse zimene Atate athu Akumwamba adamulamula kuchita. Yesu adamvera Atate athu Akumwamba chifukwa ankakonda Atate athu Akumwamba. Satana adayesa Yesu kuti asamvere Atate athu Akumwamba. Yesu sadachite zimene Satana adamuyesa.

Lamulo Loyamba ndi Lofunika Kwambiri Ndilo Kukonda Atate athu Akumwamba

Tikamakonda Atate athu Akumwamba, tidzafuna kuwamvera ngati mmene Yesu ankachitira. Tikhoza kukonda kwambiri Atate athu Akumwamba tikamaphunzira zambiri za Iwo. Tiyenera kuphunzira za Iye ndi zimene amatichitira. Timaphunzira izi powerenga malemba komanso kumvetsera atsogoleri a Mpingo wa Yesu Khristu. Tikamakonda Atate athu Akumwamba, tidzakondanso Yesu chifukwa cha zimene Yesu adachita kutithandiza kubwelera kwa Atate athu Akumwamba. Timaphunzira kukonda Yesu mwa kuchita zinthu zimene amatilamula kuchita. Pamene chikondi chathu pa Atate athu Akumwamba ndi Yesu chikukula, kumvera malamulo awo kumakhala kosavuta.

Lamulo Lalikulu Lachiwiri Ndilo Kukonda Anthu Onse

Yesu adatiuza kuti tizikonda ndi kuthandiza anthu ena. Iye watiuza kuti tiziwachitira mofanana ndi mmene timafunira kuti atichitire. Iye adati sitiyenera kunena zoipa zokhudza iwo. Tiyenera kuwakhululukira zolakwa zawo. Tiyenera kuthandiza ena m’njira iliyonse imene tingathe.

Tikamakonda Atate athu Akumwamba ndi Yesu, timakonda komanso kuthandiza ena. Pamene tikonda ndi kutumikira Yesu ndi anthu ena, kumvera Atate athu Akumwamba ndi malamulo a Yesu kumakhala kosavuta.

Zokambirana

  • Kodi malamulo awiri akuluakulu ndi ati?

  • Kodi chitsanzo cha Yesu chingatithandize bwanji kumvera malamulo a Atate athu Akumwamba?

  • Kodi tingaphunzire bwanji kukonda Atate athu Akumwamba ndi Yesu ndi kufuna kumvera malamulo awo?

Dalitso Lirilonse limene Timalandira limadza Chifukwa Cha kumvera

Atate athu Akumwamba amatidalitsa tikamamvera malamulo Awo. Iwo amalonjeza madalitso pa lamulo lililonse limene timamvera. Nthawi zonse tikamamvera lamulo, timalandira madalitso kamba ka kumverako. Ngati sitimvera lamulo, sitingayembekezere kulandira dalitso lolonjezedwa.

Ena mwa madalitso amene amabwera chifukwa chomvera malamulo a Atate athu Akumwamba ndi chisangalalo, kumasuka ku mantha, thanzi labwino, kudziwa zambiri komanso kuthekera. Dalitso lalikulu limene Atate athu Akumwamba alonjeza kwa ife ndi lakuti tingakhale ngati Iwo ndi kukhala nawo kwamuyaya. Tikhonza kulandira madalitso amenewa tikamamvera malamulo awo onse.

Pamene tikuyesetsa ndi mtima wonse kumvera malamulo a Atate athu Akumwamba, n’kofunika kukumbukira kuti tingathe kuchita zimenezi mothandizidwa ndi Yesu. Tizikumbukiranso kuti tikapanda kumvera, Atate athu Akumwamba adzatikhululukira tikamaika chikhulupiliro chathu mwa Yesu Khristu ndi kulapa. Popeza tonse tidachimwa, tiyenera kuyamikira kwambiri Chitetezero cha Yesu Khristu. Chifukwa cha Chitetezero Chake, Atate athu Akumwamba akhonza kutikhululukira ndi kutidalitsa ndi kutithandiza ife kukhala omvera. Sitingakhale oyenelera madalitso a Atate athu Akumwamba mwa tokha.

Zokambirana

  • Kodi ndi madalitso otani amene angabwere kwa inu chifukwa chomvera Atate athu Akumwamba?

  • Kodi Yesu amatithandiza bwanji kuti tipeze madalitso amenewa?

  • Kodi tingalandire bwanji mphatso yaikulu kwambiri ya Atate athu Akumwamba?

Print