Zofunikira Zoyambirira
Mutu 18: Mpingo umene Yesu Adakhazikitsa


Image
Khristu akudzodza Atumwi, ndi Harry Anderson

Yesu Khristu adadzodza Atumwi.

Mutu 18

Mpingo umene Yesu Adakhazikitsa

Yesu adakonza mpingo pamene adali padziko lapansi. Kodi udatchedwa chiyani? Ndani ankatsogolera Mpingo Wake?

Yesu adali Mutu wa Mpingo umene adaukhazikitsa

Pamene Yesu adali padziko lapansi, Iye adakhazikitsa mpingo. Mpingowu udatchedwa Mpingo wa Yesu Khristu. Mamembala a mpingo wa Yesu amatchedwa Oyera Mtima. Yesu mwiniyo adali Mutu wa mpingowu. Iye adautsogolera. Adasankha amuna khumi ndi awiri kuti amuthandize kutsogolera mpingo. Adawatcha Atumwi. Atumwiwa adalinso aneneri. Yesu adaika manja Ake pa Mutu wawo nawapatsa aliyense mwa iwo unsembe. Adawatuma kuti agwire ntchito yake. Atumwi ndi aneneriwa adali atsogoleri mu mpingo wa Yesu Khristu.

Mu Mpingo wa Yesu Khristu, azibambo amene adalandila unsembe amaika manja awo pamitu ya azibambo ena abwino ndikuwapatsa unsembe. Iyi ndinjira yokhayo imene unsembe ungaperekedwe kuchokera kwa munthu m’modzi kupita kwa wina. Unsembe sungagulidwe.

Zokambirana

  • Kodi M’tsogoleri wa Mpingo wa Yesu Khristu adali ndani?

  • Kodi amuna amene adamuthandiza Yesu amatchulidwa chiyani?

Mpingo wa Yesu Khristu udapitilira Padziko Lapansi iye atabwelera kumwamba

Yesu atabwelera kumwamba, Mpingo Wake udapitilira Padziko Lapansi. Umatsogozedwa ndi Atumwi Khumi ndi Awiri. Mtumwi akamwalira, Yesu amasankha munthu wina kuti alowe m’malo mwake. Kudzera mwa Mzimu Woyera, Yesu amadziwitsa Atumwi ena kuti Mtumwi watsopano akhale ndani. Atumwi Khumi ndi Awiri amasankha anthu ena abwino ndikuwapatsa Unsembe kuti athandize kugwira ntchito ya Mpingo wa Yesu. Anthu amenewa amatchedwa a Makumi asanu ndi awiri, mkulu wa nsembe, akulu, mabishopu, ansembe, aphunzitsi, ndi madikoni. Ntchito zawo zafotokozedwa m’Mutu 20.

Yesu Ankatsogolera Mpingo kudzera Muvumbulutso

Mauthenga amene Yesu amapereka kudzera mwa Mzimu Woyera kupita kwa anthu padziko lapansi amatchedwa mavumbulutso. Yesu amatsogolera Mpingo Wake povumbulutsa kwa mneneri ndi atsogoleri ena zinthu zimene akuyenera kuchita.

Yesu asadabwelere kumwamba, Adauza Atumwi Ake adzakhala nawo nthawi zonse. Yesu amatanthauza kuti adzapitiliza kuwatsogolera iwo kudzera mwa Mzimu Woyera.

Zokambirana

  • Kodi Yesu amatsogolera bwanji Mpingo Wake atabwelera kumwamba?

Mpingo wa Yesu Khristu udali ndi ziphunzitso Zake zoona

Atsogoleri a Mpingo wa Yesu Khristu amalandira mavumbulutso kuchokera kwa Yesu kudzera mwa Mzimu Woyera. Mwachitsanzo, Yesu adauza Mtumwi Petulo uthenga wabwino uziphunzitsidwa kwa aliyense osati kwa anthu a Israeli wokha ayi. Yesu adamuuza Mtumwi Paulo zinthu zambiri amayenera kuphunzitsa anthu. Yesu adauza zinthu zambiri za m’tsogolo kwa Mtumwi Yohane.

Pamene adali padziko lapansi, Yesu adaphunzitsa anthu kuti azimukhulupilira, kulapa, ndi kubatizidwa. Adawaphunzitsa kukonda Atate athu Akumwamba ndi kumumvera. Adawaphunzitsa kukonda anthu ena ndi kuwathandiza.

Yesu atabwelera kumwamba, Atumwi adaphunzitsanso zinthu zomwezo zomwe Yesu ankaphunzitsa. Onse amene adafuna kukhala mamembala a Mpingo wa Yesu Khristu adayenera kukhala ndi chikhulupiliro mwa Yesu Khristu, kulapa machimo awo, ndi kubatizidwa. Iwo adalandira mphatso ya Mzimu Woyera, monga momwe Yesu adalonjezera. Adaphunzira kukonda Atate athu Akumwamba ndi kumumvera. Adaphunzira kukonda ndi kutumikira anthu ena.

Zokambirana

  • Kodi anthu ankayenera kuchita chiyani kuti alowe Mpingo wa Yesu Khristu?

Amene adali mu Mpingo wa Yesu Khristu Adalandira Mphatso za Uzimu

Iwo amene adali a Mpingo wa Yesu Khristu adalandira mphatso za uzimu. Zina mwa mphatsozo zidali chikhulupiliro cha kuchiritsa odwala, kuthekera konenera za m’tsogolo, ndi mphamvu ya kuona masomphenya.

Zokambirana

  • Kodi zina mwa mphatso za uzimu ndi ziti?

Mpingo wa Yesu siudalinso pa dziko lapansi

Yesu atabwelera kumwamba, Atumwi ake adatsogolera mpingo. Anthu ambiri adakhala mamembala a Mpingo. Koma ena a iwo adayamba kuphunzitsa ndi kukhulupilira zinthu zabodza, m’malo mwa zimene Yesu ndi Atumwi ankaphunzitsa. Mwachitsanzo, anthu ena ankaphunzitsa kuti Atate athu Akumwamba alibe thupi la m’nofu ndi mafupa.

Anthu oipa adayamba kuzunza atsogoleri komanso anthu ena a mumpingo. Anthu oipa adapha Atumwi ndi atsogoleri ena amene adali ndi unsembe. Adaphanso anthu ena ambiri a Mpingo wa Yesu Khristu.

Anthu ankaphunzitsa zinthu zabodza mpaka palibe amene adakhulupilira ziphunzitso zoona za Yesu. Palibe amene adali ndi unsembe, kotelo palibe amene akanagwira ntchito ya Yesu padziko lapansi kapena kulandira malangizo kuchokera kwa Yesu m’malo mwa ana onse a Atate athu Akumwamba. Nthawi imene panalibe amene amakhulupilira ziphunzitso zoona za Yesu ndipo palibe amene adali ndi ulamuliro wake imatchedwa Mpatuko.

Pa nthawi ya Mpatuko, anthu adayambitsa mipingo yosiyana ndi umene Yesu adayambitsa. Iwo ankaphunzitsa zinthu zimene Yesu sankaphunzitsa. Iwo adalibe unsembe. Iwo ankachita miyambo yosiyana ndi miyambo imene inkachitika mu Mpingo wa Yesu. Iwo adalibe vumbulutso lochokera kwa Yesu. Sadaphunzitse malamulo onse a Uthenga Wabwino monga Yesu ndi Atumwi ake adawaphunzitsira. Aneneri adali atanena kuti zonsezi zidzachitika.

Zokambirana

  • Kodi Mpatuko udachitika bwanji?

Yesu Adalonjeza Kuti Adzabwenzeretsa Mpingo Wake Padziko Lapansi

Yesu ankadziwa kuti anthu adzataya mphamvu Zake ndi ziphunzitso zoona. Choncho adakonza njira kuti mpingo woona udzakhazikitsidwenso pa dziko lapansi.

Mtumwi Yohane adaona m’masomphenya nthawi imene uthenga wabwino udzabwenzeretsedwe padziko lapansi. Iye adaona kuti Yesu adzatumiza angelo kuti akaphunzitse anthu choonadi ponena za Atate athu Akumwamba. Yesu adzaonetsetsa kuti ana onse a Atate athu Akumwamba alandire uthenga wabwino, unsembe, madalitso, ndi zinthu zina zonse zofunika kuti iwo athe kubwelera kwa Atate wathu wa Kumwamba.

Zokambirana

  • Ndi chifukwa chiyani Yesu adakonza njira yokonzanso mpingo wake padziko lapansi?

Print