Zofunikira Zoyambirira
Mutu 5: Yesu Adalenga Dziko Lapansi


Image
dziko lapansi

Mutu 5

Yesu Adalenga Dziko Lapansi

Ndani adapanga dziko lapansi? Chifukwa chiyani Iye adalipanga?

Tinkafunikira Dziko Lapansi

Mbali ina ya dongosolo limene Atate athu Akumwamba adatifotokozera lidali lakuti tichoke kumwamba kwa kanthawi. Tinkafunikira malo oti tipite, kutali ndi pamaso pawo, kukalandira matupi a mnofu ndi mafupa ndi kuyesedwa kuti tisonyeze ngati tingasankhe zolondola. Adafunikira kuti munthu wina atipangire malo amenewa kwa ife. Iwo adasankha Yesu kuti achite zimenezi.

Zokambirana

  • Ndi chifukwa chiyani Mulungu adalongosola zopanga dziko la ife?

Yesu Adalenga Dziko Lapansi

Yesu adapanga dziko lapansi. Adapanga usana ndi usiku. Iye adapanga dzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi. Iye adalekanitsa madzi ndi nthaka yowuma n’kupanga Nyanja zazikulu, Nyanja zazing’ono, ndi mitsinje. Iye adabzala pa dziko lapansi udzu, mitengo, maluwa ndi mitundu ina yonse ya zomera. Kenako adaika pa dziko la pansi nyama, nsomba, mbalame ndi tizilombo. Yesu atachita zonsezi, dziko lapansi lidali litakonzeka kuti anthu azikhalamo.

Atate athu Akumwamba ndiye adapanga mwamuna ndi mkazi. Mwamunayo adatchedwa Adamu, ndipo mkaziyo adatchedwa Hava. Aliyense adali ndi thupi la mnofu ndi mafupa ngati thupi la Atate athu Akumwamba. Ntchito yonseyi yolenga dziko lapansi ndikuikapo zamoyo imatchedwa Chilengedwe. Atate athu Akumwamba adasangalala ndi dziko lapansi ndizinthu zonse zimene adalangiza Yesu kuti ayikemo.

Zokambirana

  • Kodi Adamu ndi Hava adali osiyana bwanji ndi zinthu zina zimene Mulungu adalenga?

Zolengedwa za Atate Akumwamba Zimasonyeza Kuti Amatikonda

Tikukhala m’dziko lokongola limene Atate athu Akumwamba adalangiza Yesu kuti apange. Dzuwa limatipatsa kutentha ndi kuwala. Mvula imapangitsa zomera kukula ndi kutipatsa madzi akumwa. Zomera ndi nyama za pa dziko lapansi zimatipatsa chakudya ndi zovala.

Yesu adatipangira ife zinthu zonsezi, motsogozedwa ndi Atate athu Akumwamba. Tikamaona kuti iye adatipangira zinthu zonsezi, timazindikira kuti Atate athu Akumwamba amatikonda komanso amatisamalira.

Zokambirana

  • Ganizilani zinthu zina zimene Atate athu Akumwamba adatipangira.

  • Kodi tikudziwa bwanji kuti Atate athu Akumwamba amatikonda komanso amatisamalira?

Tingasonyeze Kuti Timayamikira chifukwa cha Dziko Lapansi

Tidzikumbukira nthawi zonse kuti Atate athu Akumwamba adatipangira zonse zapadziko lapansi. Iwo samasangalala tikamaiwala zimenezi. Tingawasonyeze kuti ndife oyamika pa kugwiritsira ntchito mwanzeru zinthu zapadziko lapansi. Tisaononge kalikonse padziko lapansi. Tikuyenera kusamalira dziko lapansi ndi kulisunga loyera. Tikuyenera kuyamika Atate athu Akumwamba chifukwa cha dziko lokongolali tikamapemphera kwa iwo. Timaonetsanso kuti timayamikira dziko lapansi pa kuchita zinthu zimene iwo amafuna kuti tidzichita.

Zokambirana

  • Kodi tingasonyeze bwanji kwa Atate athu Akumwamba kuti timayamikira dziko lapansi?

Print