Zofunikira Zoyambirira
Mutu 14: Kulapa


Mutu 14

Kulapa

Kuchita zinthu zolakwika kumatikhumudwitsa. Kodi tingatani kuti tikhalenso osangalala tikachita zoipa?

Atate athu Akumwamba Adakonza Njira Yoti Tigonjetsere Uchimo

Atate athu Akumwamba ankadziwa kuti tonsefe tidzachita zinthu zoipa padzikoli. Zolakwika zomwe timachita ndi machimo. Timachimwa tikamachita zimene Mulungu watiuza kuti tisachite. Timachimwanso tikapanda kuchita zimene Mulungu watiuza.

Atate athu Akumwamba sachimwa, ndipo salora kuti anthu ochimwa akhale ndi Iwo. Kuti tikhale nawo limodzi tiyenera kulapa machimo athu. Kulapa kumatanthauza kumva chisoni ndi machimo athu ndi kusiya kuwachita.

Atate athu Akumwamba amatikonda. Safuna kuti machimo athu atiletse kubwelera kwa Iwo. Choncho adakonza njira yoti atithandize.

Atate athu Akumwamba adatumiza Yesu kuti atithandize kulapa machimo athu. Yesu amatiphunzitsa zimene tikuyenera kuchita kuti tipewe uchimo. Amatipatsanso mphamvu zochitira zinthu zimenezi. Tikakhulupilira mwa Iye ndi kumutsata, amasintha mitima yathu kuti tisafune kuchimwa, koma kufuna kuchita zabwino zokha. Ngati sitifuna kuzunzika chifukwa cha machimo athu, tikuyenera kukhulupilira mwa Yesu. Iwo amene amakhulupiliradi mwa Yesu amalapa machimo awo.

Tikakhulupilira mwa Yesu ndi kulapa, mazunzo a Yesu amalipira machimo athu ndipo timayeretsedwa. Tikhoza kubwelera kukakhala ndi Atate athu Akumwamba chifukwa ndife oyera.

Zokambirana

  • Kodi kulapa kumatanthauza chiyani?

  • Ndi chifukwa chiyani Atate athu Akumwamba amafuna kuti tilape machimo athu?

  • Ndi chifukwa chiyani anthu amene ali ndi chikhulupiliro mwa Yesu amalapa machimo awo?

Atate athu Akumwamba Atiuza Zimene Tikuyenera Kuchita Kuti Tilape

Kuti tilape, tiyenera kukhulupilira Yesu ndi zimene adaphunzitsa. Tiyenera kukhulupilira kuti Iye adazunzika chifukwa cha machimo athu. Tiyenera kukhulupilira kuti Iye yekha ndi amene angatilipilire machimo athu. Tiyenera kukhulupilira kuti Iye amafuna kuti tigonjetse machimo athu ndipo adzatithandiza kuchita zimenezi. Tiyenera kulimbikira kuchita zimene Iye amatilamula.

Pamene talapa, timalora Yesu kutisintha kukhala mmene iye amafunira. Timasiya kuchita zoipa ndi kuyamba kuchita zabwino. Ngati tanena zinthu zabodza, timasiya ndi kunena zoona zokhazokha. Ngati taba chinthu, timachibwenzera kwa mwiniwake ndipo sitimabanso kalikonse. Ngati tachitira ena zoipa, timasiya ndi kuwachitira zinthu zabwino.

Tikalapa timachita zinthu izi:

Timavomereza tokha kuti tachimwa. Timadziwa kuti tikuchimwa pamene sitikumvera Atate athu Akumwamba. Tikalapa, sitipereka zifukwa zotitchinjiriza popanga zinthu zoipa. Timavomereza kuti talakwitsa, ndipo tikufuna kusintha.

Timamva chisoni ndi zoipa zimene tachita. Tikalapa, timamva chisoni chochokera pansi pa mtima chifukwa chochita zoipa. Sitimangonena kuti tikupepesa chifukwa cha machimo athu. Timamva chisoni kwambiri pochita zimenezi ndipo timalakalaka tikanapanda kuzichita. Timafunanso kuchita zimene Atate athu Akumwamba amatilamula.

Timasiya kuchita zinthu zolakwika. Ngati tingovomereza tokha kuti tachimwa, ndipo ngati tingonena kuti tamva chisoni, ndiye kuti sitinalapedi. Kuti tilape moona mtima, tiyeneranso kusiya kuchita zoipa. Nthawi zina si zophweka kusiya, koma Yesu adabwera padziko lapansi kudzatipatsa thandizo limene tikufunikira. Atate athu Akumwamba amafuna kuti tilore Yesu kuti atithandize chifukwa ndi mmene tingakhalire angwilo ndi kubwelera kukakhala ndi Mulungu.

Timavomereza machimo athu. Mu Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima a M’masiku Otsiriza, kuulura kumatanthauza kuuza Atate Akumwamba ndi mtsogoleri wa Mpingo zomwe talakwitsa. Machimo ena amene timachita amakhudza ife tokha. Tikamapemphera kwa Atate athu Akumwamba, tiyenera kuwauza za machimowo ndi kuwapempha kuti atikhululukire ndi kutithandiza kuwagonjetsa. Ngati tchimo lathu lakhudza munthu wina, tiyenera kuulura kwa munthuyo ndi kwa Mulungu. Tiyenera kuulura machimo oipa kwambiri, monga chigololo, kwa mtsogoleri wathu wa Mpingo, yemwe angathe kukhala a bishopu* athu kapena a pulezidenti athu a nthambi.*

Timachita zonse zomwe tingathe kuti tikonze zolakwika zomwe talakwitsa. Tikalapa, timakonza zinthu zoipa zimene tachita. Mwachitsanzo, ngati tamubera mnansi wathu, timabwenzera zimene tidatenga. Ngati tilibe chinthu chomwe tidatengacho, timachisinthitsa ndi china kapena kulipira.

Timakhululukira machimo a ena. Atate athu Akumwamba Atilamula kuti tizikhululukira ena. Ngati tikufuna kuti atikhululukire, tiyenera kukhululukira ena. Ngati timadana ndi anthu ena chifukwa cha zoipa zimene adachita ndipo sitiwakhululukira, Atate athu Akumwamba sadzatikhululukira.

Timayesetsa ndi mtima wonse kumvera malamulo onse a Yesu moyo wathu wonse. Timapitiriza kusintha zimene timalakwitsa mpaka titachita zoyenera. Timachita zimene tingathe tsiku lirilonse kuti tikonze zinthu zoipa zimene timachita.

Tiyenera kulapa pamene tachita cholakwa. Tikhonza kuganiza kuti kulapa panopa ndi kovuta. Tikhonza kuganiza kuti kulapa kudzakhala kosavuta pambuyo pake, koma sikudzatero. Kulapa kumakhala kovuta kwambiri tikamadikilira kuti tichite. Kudikira kulapa kumatibwezanso m’mbuyo mwauzimu, chifukwa Yesu sangatithandize kuphunzira zambiri za Atate athu Akumwamba ndi kukonzekera kukakhala ndi Atate athu Akumwamba ngati sitilapa zoipa zimene timachita. Tikazindikira kuti tikuchita zinthu zolakwika, tiyenera kulapa nthawi yomweyo.

Zokambirana

  • Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tilape?

Aliyense wa Ife Akhonza Kulapa

Aliyense wa ife akhonza kulapa. Nthawi zina kulapa kumaoneka ngati kovuta kwambiri kwa ife. Tikhonza kuganiza kuti sitingathe kugonjetsa zofooka zathu. Satana amafuna kuti tizikhulupilira zimenezi kuti tipitirize kuchita zoipa. Tiyenera kukumbukira kuti tikhonza kulapa. Sitingathe kuchita tokha. Timafunika thandizo. Aliyense wa ife ndi mwana wa Atate athu Akumwamba, ndipo adatumiza Yesu kuti adzatithandize. Ndi thandizo la Yesu tingathe kuchita zinthu zonse zimene Atate athu Akumwamba adatilamulira.

Yesu adzatithandiza kulapa ngati tipemphera kwa Atate athu Akumwamba kuti atithandize. Iye ndi Atate athu Akumwamba amafuna kuti tizichita zinthu zoyenera. Sakonda zinthu zoipa zimene timachita. Koma amatikondabe ngakhale titachita zinthu zolakwika. Amafuna kuti tilape kuti Atate athu Akumwamba atikhululukire komanso kuti tikhale osangalala.

Zokambirana

  • Ndi chifukwa chiyani tikufunika kulapa ngakhale pamene kulapa kukuoneka kukhala kovuta?

  • Ndani angatithandize kulapa?

Atate athu Akumwamba Amatipatsa Mphotho Tikalapa

Tikayika chikhulupiliro chathu mwa Yesu ndi kulapa, Atate athu Akumwamba amatikhululukira kotheratu. Sitiyenera kuda nkhawa kuti tidzalangidwa chifukwa cha Iwo. Osati kutikhululukira kokha; Amatipatsanso thandizo kuti tisafunenso kuchimwa, koma kuti tichite zabwino zokhazokha nthawi zonse. Yesu amatipatsa thandizo limeneli.

Tiyenera kukumbukira kuti sitidzakhala ngati Atate athu Akumwamba kwanthawi imodzi. Koma pamene tikupitiriza kukhala ndi chikhulupiliro mwa Yesu ndi kulapa machimo athu ndi kugwira ntchito yomvera Yesu, Atate athu Akumwamba amapitiriza kutikhululukira machimo athu. Yesu amapitiriza kutithandiza. Timakhala ngati Atate athu Akumwamba. Pamapeto pake, tikhoza kubwelera kukakhala ndi Atate athu Akumwamba.

Tikalapa timakhala osangalala. Sitikhala achisoni ndi zoipa zimene tachita, koma timasangalala chifukwa tagonjetsa zofooka zathu ndi thandizo la Yesu. Tikatero timadziwa kuti tiri ndi mphamvu zokana mayesero ndi kuchita zinthu zoyenera.

Zokambirana

  • Kodi timalandira mphotho zotani tikalapa?

Print