Zofunikira Zoyambirira
Mutu 25: Lamulo la Kudzisunga


Mutu 25

Lamulo la Kudzisunga

Atate athu Akumwamba adatipatsa mphamvu yopatulika yokhala ndi ana. Iwo adatiuza mmene tingagwiritsile ntchito mphamvu zimenezi. Ngati tingazigwiritse ntchito moyenera, tingakhale osangalala kwambiri.

Atate athu Akumwamba Atiuza Kuti Tikhale ndi Ana Ndi Kumvera Lamulo La Kudzisunga

Adamu ndi Hava atakwatirana, Atate athu Akumwamba adawauza kuti abereke ana. Iwo adauza Adamu ndi mkazi wake Hava kuti abereke ana kuti mizimu yakumwamba ibwere padziko lapansi n’kulandira matupi mnofu ndi mafupa. Thupi la mnofu ndi mafupa ndi imodzi mwa mphatso zazikulu kwambiri zomwe Atate athu Akumwamba atipatsa. Atate athu Akumwamba ali ndi thupi la mnofu ndi mafupa, ndipo amafuna kuti ana ake akhale ngati Iwo.

Mphamvu yokhala ndi ana ndi yopatulika kwambiri. Atate athu Akumwamba atipatsa lamulo lotiuza mmene tingagwiritsire ntchito mphamvuzi. Lamulo limeneli limatchedwa lamulo la kudzisunga. Limati tizigonana ndi munthu amene tidakwatirana naye mwalamulo. Izi zikutanthauza kuti sitiyenera kugonana tisadalowe m’banja, ndipo tikalowa m’banja tiyenera kugonana ndi mwamuna kapena mkazi wathu basi.

Kuchotsa mimba, kapena kuchotsa mwana wosabadwa m’kati mwa mayi ake ndi kumulola kuti afe kapena kupha mwanayo akadali m’mimba mwa mayiyo, n’kulakwa pokhapokha ngati pali zochitika zina zapadera, zimene ziyenera kuganiziridwa mosamalitsa ndi pemphero ndi chithandizo cha a bishopu athu kapena pulezidenti wa nthambi. Sitikuyenera kuthandiza wina aliyense kuchotsa mimba.

Makolo ndi amene akuyenera kuphunzitsa ana awo lamulo la kudzisunga. Makolo akuyenera kuwaphunzitsa kuti matupi awo ndi opatulika ndipo sakuyenera kulora aliyense kukhudza mbali zina za thupi lawo. Ayenera kuwongolera malingaliro olakwika ndi mawu omwe ana awo amaphunzira kwa ena.

Ana akamakula ayenera kuphunzitsidwa kuti Atate athu Akumwamba adatipatsa mphamvu zokhala ndi ana komanso kuti kugwiritsa ntchito mphamvu zimenezi tikalowa m’banja n’kwabwino. Ana athu akamafika dzaka 12 kapena 13, tikuyenera kukhala titawathandiza kale kumvetsa mmene ana amapangidwira. Tikuyenera kuwaphunzitsa adakali aang’ono m’njira yozama kwambiri kuti atetezedwe ku zinthu zoipa kapena ziphunzitso zabodza.

Zokambirana

  • Nchifukwa chiyani Atate athu Akumwamba adatipatsa mphamvu zokhala ndi ana?

  • Kodi Lamulo la Kudzisunga ndi chiyani?

  • Kodi tikuyenera kuphunzitsa ana athu chiyani za matupi awo?

Satana Amafuna Kuti Tiphwanye Lamulo la Kudzisunga

Satana amafuna kutiletsa kubwelera kwa Atate athu Akumwamba. Satana amafuna kuti tiphwanye lamulo la kudzisunga. Iye amafuna kuti tiziganiza kuti mphamvu zokhala ndi ana si zopatulika. Amafuna kuti tiziganiza kuti kuphwanya lamulo la kudzisunga si tchimo.

Satana amagwiritsa ntchito njira zanzeru kutinyengelera kuti tiphwanye lamuloli. Amayesa kutichititsa kuganiza kuti kulora ena kuona ndi kugwira matupi athu n’kovomerezeka. Satana amafuna kuti tiziganiza zoipa. Iye amatilimbikitsa kuti tiziona zithunzi, mafilimu, ndi magule amene amatiyesa kukhala osadzisunga. Amatilimbikitsanso kuti tizichita nawo magule ndi kumvetsera nkhani, nthabwala, ndi nyimbo zimene zingatikope kuti tisadzisunge. Satana amafuna kuti tizichita zinthu zimenezi kuti matupi athu asaoneke ngati opatulika, choncho tidzagwiritsa ntchito mphamvuzo pobereka ana m’njira yolakwika.

Nthawi zina Satana amatiyesa ndi kamveredwe kathu. Satana amadziwa tikakhala osungulumwa, osokonezeka, kapena osasangalala. Amasankha nthawi za kufooka izi kuti atipangitse kumphwanya lamulo la kudzisunga. Iye amafuna kuti tiziganiza kuti tiri ndi ufulu wogwilitsila nchito mphamvuzo m’njila iliyonse imene tingafune kugwiritsila ntchito mphamvuzo. Iye amayesa kutipangitsa kuganiza kuti palibe choipa chimene chingatichitikire ngati tiphwanya lamulo la kudzisunga.

Atate athu Akumwamba angatipatse mphamvu kuti tigonjetse mayesero a Satana. Iwo safuna kuti tidziona zinthu zoipa kapena kuganiza zoipa. Iwo alonjeza kuti sadzalola Satana kutiyesa kuposa mmene ife tingathere kugonjetsa. Iwo akonza njira yoti tigonjetsere mayesero.

Tikhoza kupemphera kwa Atate athu Akumwamba kuti atithandize kulimbana ndi Satana. Pamene tipemphera, Atate athu Akumwamba adzatumiza Mzimu Woyera kuti atithandize. Mzimu Woyera udzatithandiza kukumbukira kuti matupi athu ndi opatulika komanso kuti mphamvu yobala ana ndi yopatulika. Mzimu Woyera adzatithandiza kuti tisagwiritse ntchito mphamvuyi molakwika. Iye adzatithandiza kusankha zinthu zabwino zimene tingaone, kuziŵelenga ndi kuziganizila. Iye adzatithandiza kukumbukira kuti kuphwanya lamulo la kudzisunga kudzatipangitsa kukhumudwa, ndipo kumvera lamuloli kungatithandize kukhala osangalala.

Zokambirana

  • Nchifukwa chiyani Satana amafuna kuti tiphwanye lamulo la kudzisunga?

  • Kodi tingachite chiyani kuti tigonjetse mayesero a Satana?

  • Kodi Atate athu Akumwamba angatithandize bwanji kumvera lamulo la kudzisunga?

Kuphwanya Lamulo la kudzisunga Ndi Tchimo Lalikulu Kwambiri

Kugonana kumakhala kwabwino ndi koyera ngati kuli pakati pa mwamuna ndi mkazi wake amene amakondana ndi kulemekezana. Ndi njira imene Atate athu Akumwamba atipatsa kuti tikhale ndi ana. Zimakhalanso njira yoti mwamuna ndi mkazi asonyeze chikondi chawo kwa wina ndi mnzake ndi kuyandikirana m’maganizo mwawo. Koma kugonana ndi munthu wosakwatirana ndi tchimo lalikulu.

Kuphwanya lamulo la kudzisunga kumatipangitsa kukhala osasangalala. Tikazindikira kuti sitinamvere Atate athu Akumwamba, timadzimva kulakwa komanso kuchita manyazi. Tidzazindikira kuti tagwiritsira ntchito molakwa mphamvu yopatulika imene adatipatsa ndi kuti takhumudwitsa ena. Kuswa lamulo la kudzisunga kungachititse kuti mwana abadwe popanda banja loyenera.

Machimo awiri okha ndi aakulu kuposa kumphwanya lamulo la kudzisunga. Awa ndi kukana Mzimu Woyera ndi kupha. Amene aphwanya lamulo la kudzisunga akhoza kukhululukidwa. Atate athu Akumwamba adanena kuti ngati akhala ndi chikhulupiliro mwa Yesu ndi kulapa machimo awo, Iye adzawakhululukira. Iwo amene amaphwanya lamulo la chiyero ndipo osalapa sadzatha kukhala ndi Atate athu Akumwamba.

Anthu amene adagwiliridwa kapena kuchitidwa nkhanza zokhudza kugonana alibe mlandu wophwanya lamulo la kudzisunga.

Chikhululukiro chingabwere pokhapokha kudzera mu chikhulupiliro mwa Yesu ndi kulapa. Tikuyenera kuzindikira kuti tachimwa ndi kumva chisoni moona mtima chifukwa cha cholakwa chimene tachita. Tikuyenera kusiya kuchita chinthu chomwe chiri cholakwika ndi kuvomereza tchimolo kwa Atate athu Akumwamba, kwa anthu omwe tidawapweteka nawo, komanso ku ulamuliro woyenera wa unsembe (bishopu, pulezidenti wa nthambi, pulezidenti wa sikeki, kapena pulezidenti wa mishoni). Atate athu Akumwamba anena kuti Iwo adzawakhululukira amene ali ndi chikhulupiliro mwa Yesu, aulula machimo awo kwa Atate athu Akumwamba ndi kwa mtsogoleri woyenerera wa Mpingo, ndi kulapa moona mtima. Aliyense amene sachita zonsezi sadalape moona mtima ndipo sadzakhululukidwa.

Zokambirana

  • N’chifukwa chiyani kuswa lamulo la kudzisunga ndi tchimo lalikulu chonchi?

  • Kodi chingachitike n’chiyani kwa ife tikaphwanya lamulo la kudzisunga?

  • N’chifukwa chiyani tikuyenera kumvera lamulo la kudzisunga?

  • Kodi tikuyenera kuchita chiyani kuti tilape za kuswa lamulo la kudzisunga?

Kumvera Lamulo la Kudzisunga Kumatipatsa Chimwemwe

Tikamamvera lamulo la kudzisunga, timasonyeza chitsanzo chabwino kwa ana athu. Tikudziwa kuti Atate athu Akumwamba amasangalala nafe chifukwa chowamvera. Tikamamvera lamuloli, a m’banja lathu amadziwa kuti timawakonda, ndipo sitiyenera kudziimba mlandu kapena kuchita manyazi. Timakhala ngati Atate wathu wakumwamba. Atate athu Akumwamba amatidalitsa ife ndi ana athu, kapena ana amene tidzakhala nawo, pamene timvera lamulo la kudzisunga.

Kugwiritsa ntchito mphamvu zomwe Atate athu Akumwamba adayika m’matupi athu m’banja kumabweretsa chisangalalo. Kwa okwatirana, kugonana kungabweretse chimwemwe. Kungawayandikiritse pamodzi ndi malingaliro amphamvu achikondi. Ana amene angabadwe ndi mdalitso wochokera kwa Atate athu Akumwamba. Ngakhale kuti nthawi zina ana amabweretsa nkhawa kapena chisoni kwa makolo awo, iwo amabweretsanso chimwemwe chachikulu. Zina mwa zimwemwe zazikulu zimene tikudziwa m’moyo wathu zidzabwera pamene ana athu akukula, kuphunzira, kukwatiwa, ndi kukhala ndi ana awo.

Zokambirana

  • Kodi timalandira madalitso otani tikamamvera lamulo la kudzisunga?

  • N’chifukwa chiyani timakhala osangalala tikamatsatila lamulo la kudzisunga kuposa pamene sitilitsatila?

Print