Zofunikira Zoyambirira
Mutu 12: Chitetezero cha Yesu Khristu


Mutu 12

Chitetezero cha Yesu Khristu

Yesu adavutika kwambiri chifukwa cha machimo athu. N’chifukwa chiyani adasankha kutifera?

Atate athu Akumwamba Adatumiza Yesu Khristu Padziko Lapansi Kuti Akhale Mpulumutsi Wathu

Tifunika kukhala ndi matupi amnofu ndi mafupa kuti tikhale ngati Atate athu Akumwamba, koma Atate athu Akumwamba ankadziwa kuti tonsefe tidzafa ndi kutaya matupi athu chifukwa Adamu ndi Hava sadamvere Atate athu Akumwamba. Mwa kudya chipatso chimene Atate athu Akumwamba adawauza kuti asadye, adzafa, ndipo adzafanso aliyense wobadwa pambuyo pawo. Komanso, Atate athu Akumwamba ankadziwa kuti tonsefe tidzachimwa pamene tiri padziko lapansi, ndipo chifukwa cha machimo athu sitidzatha kubwelera kukakhala ndi Iwo. Tidzafunika thandizo kuti tilipire chilango cha machimo athu ndi kukhala omvera kuti tibwelere kwa Atate athu Akumwamba. Tinkafunika thandizo kuti tipezenso matupi athu a mnofu ndi mafupa tikadzamwalira. Yesu adati adzatithandiza. Iye adzakhala Mpulumutsi wathu.

Tinkafunika munthu wopanda uchimo kuti alipire machimo athu. Yesu yekha ndi amene akadatha kuchita zimenezi. Iye sadachimwepo. Iye adali ndi mphamvu pa imfa, kotero kuti adatha kutithandiza ife kukhalanso ndi matupi athu tikafa. Iye adatikonda ife kwambiri. Iye adali wokonzeka kuvutika chifukwa cha machimo athu kuti tikhale oyera kwa iwo. Iye adali wokonzeka kutifera kuti tidzakhalenso ndi moyo tikamwalira. Nsembe ya Yesu kwa ife imatchedwa Chitetezero.

Zokambirana

  • Ndichifukwa chiyani kudali kofunika kuti Atate athu Akumwamba atumize Yesu pa dziko lapansili?

Mazunzo a Yesu Amasonyeza Kuti Iye ndi Atate athu Akumwamba Amatikonda Kwambiri

Atate athu Akumwamba amatikonda kwambiri moti adatumiza Mwana wawo, Yesu, padziko lapansi ndipo adamulola kuti avutike ndi kutifera. Yesu amatikonda kwambiri moti adamva zowawa komanso imfa chifukwa cha ife. Yesu ankadziwa kuti mavutowo adzakhala aakulu kwambiri. Zidali pafupifupi kuposa momwe Iye akadatha kupilira. Koma ankafuna kuti tikhale ngati Atate athu Akumwamba.

Yesu adapita kumalo otchedwa Munda wa Getsemane. Kumeneko adagwada ndi kupemphera kwa Atate athu Akumwamba kuti amuthandize. Iye adafunsa Atate wathu wakumwamba, ngati n’kotheka, kuti asavutike. Koma adanena kuti adzachita zimene Atate athu Akumwamba ankafuna kuti achite. Yesu sadakakamizidwe kuvutika. Adasankha kuvutika chifukwa idali gawo la dongosolo la Atate athu Akumwamba kuti tiyeretsedwe ku machimo athu.

Ku Getsemane, Yesu adazunzika chifukwa cha machimo aanthu onse, ngati kuti adali ake. Kuzunzika kwake chifukwa cha machimo onsewa kudali kwakukulu kuposa momwe aliyense wa ife angamvetsere. Ululu udali waukulu kwambiri moti adanjenjemera. Mwazi udatuluka kuchokera m’mabowo aliwonse a thupi Lake.

Kenako anthu oipa adabwera n’kupita naye kwa olamulira a ku Yerusalemu. Kumeneko adamulavulira Iye ndikumumenya. Adapanga chisoti chaminga ndi kumuveka pa mutu Pake. Iwo adamuseka Iye ndi kumunyoza Iye.

Olamulirawo adauza asilikali kuti apachike Yesu. Adamunyamula Iye kunyamula mtanda wolemera wa mtengo mpaka kumalo kumene akadafera. Iwo adamupachika Iye pa mtanda pokhomelera misomali m’manja ndi m’mapazi Ake. Pamtanda, adamaliza kuvutika chifukwa cha kusamvera kwa Adamu ndi machimo athu.

Adamusiya popachikidwapo kwa maola ambiri. Ngakhale kuti iye adali kuvutika, ndipo ngakhale kuti anthu ena adali kumusekabe, iye adali phee ndi woleza mtima. Pomaliza, adauza Atate athu Akumwamba kuti akubweza mzimu wawo kwa Iwo, ndipo adafa.

Yesu adali ndi mphamvu zodzipulumutsa yekha ku imfa. Iye akadapitiriza kukhala ndi moyo, koma adasankha kufa kuti tikhalenso ndi moyo ndi Atate athu Akumwamba.

Pamene Yesu adafa, mzimu wake udachoka m’thupi lake.

Yesu adaonekera kwa Atumwi ake ndiponso kwa anthu ena ataukitsidwa. Adawasonyeza Atumwi ake zipsera zotsalira ndi misomali m’manja ndi m’mapazi Ake. Iwo adawakhudza n’kudziŵa kuti ameneyo ndiye mtsogoleri wawo, Yesu, adaukitsidwa. Iye adalankhula nawo ndi kudya nawo.

Zokambirana

  • Kodi Atate athu Akumwamba adasonyeza bwanji kuti amatikonda?

  • Kodi Yesu adasonyeza bwanji kuti amatikonda?

Image
Khristu mu Getsemane, wolemba Harry Anderson

M’munda wa Getsemane ndipo kenako pa mtanda, Yesu adatenga machimo aanthu onse.

Yesu Adapanga Kukhala Kotheka Kuti Tikayeretsedwe ku machimo

Ndi Yesu yekha amene akadatha kulipira machimo athu. Timalandira zabwino zonse za nsembe yake mwa kukhulupilira kuti ali ndi moyo ndi kusunga malamulo ake. Tikuyenera kumva chisoni chifukwa cha machimo athu. Sitikuyenera kuwachitanso. Tikuyenera kutsatira ziphunzitso za Yesu Khristu. Kenako Atate athu Akumwamba amatikhululukira machimo athu.

Zokambirana

  • Ndi chifukwa chiyani mukufuna Yesu kuti akuthandizeni kugonjetsa machimo anu?

  • Kodi mukuyenera kuchita chiyani kuti Chitetezero cha Yesu chithe kulipira machimo anu?

Image
Khristu Pamtanda, wolemba Carl Heinrich Bloch

Yesu adafa pa mtanda chifukwa cha machimo aanthu onse.

Yesu Adapangitsa Kuti Tonse Tikhale Wothekera Kupezanso Matupi Athu

Yesu adafa mwakufuna kwake ndipo adali munthu woyamba kuukitsidwa. Ndi munthu yekhayo amene adali ndi mphamvu yodziukitsa yekha. Iye waperekanso mwayi woti tidzaukitsidwa.

Ngakhale kuti tidzafa, tidzakhalanso ndi moyo. Tikafa, mizimu yathu imasiya matupi athu. Koma popeza Yesu adagonjetsa imfa, mizimu yathu ndi matupi athu zidzalumikizananso kwamuyaya. Sitidzafanso. Imeneyi ndi mphatso imene Yesu adapereka kwa aliyense wobadwa padziko lapansi.

Zokambirana

  • Kodi Yesu adachititsa bwanji kuti tipezenso matupi athu?

  • Kodi ndindani amene atadzaukitsidwe?

Print