Zofunikira Zoyambirira
Mutu 36: Moyo Wamuyaya


Image
thambo lodzala ndi kuwala

Iwo amene ali okhulupirika mpaka mapeto adzakwezedwa pamodzi ndi Atate athu Akumwamba ndi Yesu Khristu.

Mutu 36

Moyo Wamuyaya

Kodi tidzapita kukakhala kuti pambuyo pa Chiweruzo Chomaliza?

Aliyense Adzapita Kumalo Amene Tidakonzedwera

Yesu adaphunzitsa kuti Atate athu Akumwamba adatikonzera malo ambiri oti tikhalemo. Aliyense wa ife adzapatsidwa malo amodzi mwa malo anayi, molingana ndi mmene tidaliri okhulupirika kwa Yesu Khristu. Tidzapita ku ufumu umene taukonzekera ndi zisankho zomwe tapanga. Malo anai awa ndi ufumu waselestiyo, ufumu waterestriyo, ufumu watelestiyo, ndi kumidima kunja.

Ufumu wa Selestiyo

Awa ndi malo amene Atate athu Akumwamba ndi Yesu amakhala. Ndi malo amene anthu adzakhala osangalala, ndipo adzakhala okongola kwambiri kuposa mmene tingaganizire. Anthu amene adzakhala mu ufumu umenewu adzakonda Atate athu Akumwamba ndi Yesu ndipo adzasankha kuwamvera. Akuyenera kuti adalapa machimo awo onse ndipo akuyenera kuti adavomera Yesu ngati Mpulumutsi wawo. Akuyenera kuti adabatizidwa ndi kulandira mphatso ya Mzimu Woyera. Akuyenera kukhala ndi umboni wochokera kwa Mzimu Woyera kuti Yesu ndi Mpulumutsi.

Kukhala m’chigawo chapamwamba kwambiri cha ufumu wakuselestiyo kumatchedwa kukwezedwa* kapena moyo wosatha. Kuti athe kukhala m’gawo limeneli la ufumu wakuselestiyo, anthu akuyenera kuti adakwatirana m’kachisi ndipo akuyenera kusunga malonjezo opatulika amene adapanga m’kachisimo. Adzalandira chilichonse chimene Atate athu Akumwamba ali nacho ndipo adzakhala ngati Iwo. Adzakhalanso Okuti akhoza kukhala ndi ana auzimu ndi kupanga dziko latsopano loti akhalemo, ndi kuchita zinthu zonse zimene Atate athu Akumwamba adachita. Anthu amene sadakwatire m’kachisi akhoza kudzakhala m’madera ena a ufumu wa kuselestiyo, koma sadzakwezedwa.

Ufumu wa Terestriyo

Ufumu umenewu si wodabwitsa monga ufumu wa kuselestiyo. Ngakhale kuti Yesu azidzayendera ufumu wa terestriyo, iwo amene amakhala kumeneko sadzakhala ndi Atate athu Akumwamba, ndipo sadzakhala ndi zonse zomwe ali nazo. Amene adzapite ku ufumu wa terestriyo adzakhala anthu olemekezeka. Ena a iwo adzakhala mamembala a Mpingo, ndipo ena sadzakhala. Adzakhala amene sadalandire Yesu padziko lapansi koma kenako adamulandira ku dziko la mizimu. Anthu amene adzakhala kumeneko sadzakhala mbali ya banja lamuyaya koma adzakhala padera, opanda mabanja. Atate athu Akumwamba adzapatsa anthu amenewa chimwemwe chimene akonzekera kulandira.

Ufumu wa Telestiyo

Ufumu umenewu siwapamwamba monga ufumu wa kuselestiyo kapena wakuterestriyo. Atate athu Akumwamba kapena Yesu sadzawayendera iwo okhala kumeneku. Angelo adzawayendera anthu awa, ndipo iwo adzakhala nayo mphamvu ya Mzimu Woyera. Anthu amene amakhala mu ufumu wakutelestiyo ndi amene sanalandire uthenga wabwino kapena umboni wa Yesu, padziko lapansi kapena kudziko la mizimu. Iwo adzazunzika chifukwa cha machimo awo mu ndende ya mizimu mpaka itatha Mileniyamu. Kenako adzaukitsidwa.

Pamene adali padziko lapansili, iwo adali abodza, akuba, ambanda, aneneri onyenga, achigololo, ndi onyoza zinthu zopatulika. Adali anthu amene adavomereza zikhulupiliro za dziko osati ziphunzitso za Yesu. Anthu ambiri adzakhala mu ufumu umenewu. Atate athu Akumwamba adzapatsa anthu amenewa chimwemwe chimene akonzekera kulandira.

Kumidima kunja

Kumidima kunja ndi kumene Satana ndi amene amamutsatira adzakhala. Anthu amenewa adzakhala amene adasankha kukhala ndi Satana. Sadzakhululukidwa. Anthu amenewa adzakhala kosatha mumdima, muchisoni, ndi mukuzunzika pamodzi ndi Satana ndi mizimu yomutsatira.

Zokambirana

  • Kodi tikuyenera kukonzekera ufumu uti kuti tikhale ngati Atate athu Akumwamba?

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene tikuyenera kuchita pano padziko lapansi kuti tikhale oyenelera kukhala ngati Atate athu Akumwamba?

Atate athu Akumwamba adatipatsa Uthenga Wabwino Wotikonzekeretsa ku Moyo Wamuyaya mu Ufumu wa Kuselestiyo

Atate athu Akumwamba amapatsa aliyense wa ife mwayi wokhala ndi moyo wosatha ndi Iwo. Moyo wamuyaya ndi moyo womwe Atate athu Akumwamba ndi Yesu amakhala nawo. Atate athu Akumwamba ndi angwiro. Iwo amadziwa zinthu zonse. Iwo ali ndi mphamvu pa chirichonse. Iwo amalamulira zinthu zonse. Iwo amakhala motsatira choonadi ndi malamulo amuyaya.

Yesu adamvera Atate athu Akumwamba, choncho amakhala ndi Atate athu Akumwamba. Ngati tichita zimene Yesu adatiphunzitsa, tidzatha kukhala ndi moyo monga mmene Iye ndi Atate athu Akumwamba amakhalira. Kukhala ndi moyo wosatha ndi Atate athu Akumwamba ndi mphatso yaikulu kwambiri imene angatipatse. Idzatipatsa chimwemwe chochuluka kuposa chirichonse.

Uthenga Wabwino umatiuza zonse zimene tikuyenera kudziwa komanso zonse zimene tikuyenera kuchita kuti tilandire moyo wosatha. Zimatithandiza kudziwa Atate athu Akumwamba ndi Yesu. Zimatiphunzitsa ife momwe tingakhalire ndi moyo. Popemphera ndi kuphunzira malemba tikhonza kuwadziwa bwino. Tikawadziwa ndi kuwakonda, tidzafuna kumvera mawu awo. Tikamamvera, tidzatha kukhala ngati Iwo n’kukhala oyenera kukhala nawo mpaka kalekale.

Zokambirana

  • Kodi moyo wosatha ndi chiyani? Adzaulandira ndani?

  • Kodi uthenga wabwino umatithandiza bwanji kutikonzekeretsa ku moyo wosatha?

Atate athu Akumwamba Adzatithandiza Tikasankha Kumvera Uthenga Wabwino

Atate athu Akumwamba amadziwa kuti ndi zotheka kwa tonsefe kukhala ndi moyo wabwino ndi kulandira moyo wosatha. Popeza ndife ana awo, tili ndi mphamvu zokhala ngati Iwo. Iwo amadziwa zofooka zimene aliyense wa ife ali nazo ndiponso zimene zingatiyese. Iwo adatilora kubwera padziko lapansi pa nthawi yake komanso malo amene adzatipatsa mwayi wochita zinthu zabwino ndi kuphunzira.

Tsopano ndi nthawi yoti tichite zonse zimene tikuyenera kuchita kuti tilandire moyo wosatha. Atate athu Akumwamba amatikonda ndipo amafuna kuti tipambane. Iwo adatichitira zonse zimene angathe. Iwo adatipatsa dziko lapansi mmene tingaphunzire ndi kukula. Iwo adatumiza Mwana wawo, Yesu Khristu, kuti akhale Mpulumutsi wathu ndi kutiphunzitsa uthenga wabwino. Iwo adatipempha kuti tidzipemphera kwa iwo. Iwo apanga zotheka kuti Mzimu Woyera ukhale wotitsogolera. Tsopano tikuyenera kuchita zinthu zoyenera. Ngati tisankha kukhala ndi chikhulupiliro mwa Yesu KhristuKhristu ndi kumumvera, iye adzatithandiza ndi kutipatsa mphamvu kuti tigonjetse mayesero ndi mavuto ena amene amadza m’miyoyo yathu.

Atate athu Akumwamba atipempha kuti tilandire uthenga wabwino. Kuti tichite zimenezi, choyamba tikuyenera kukhala ndi chikhulupiliro mwa Yesu Khristu. Kenako tikuyenera kulapa machimo athu kuti tibatizidwe ndi kutsimikiziridwa kukhala membala wa Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza. Pamene tatsimikiziridwa, timalandira mphatso ya Mzimu Woyera kuchokera kwa amene ali ndi unsembe. Mzimu Woyera umatiuza aliyense wa ife zimene Yesu akufuna kuti tichite, ndipo kuti tilandire moyo wosatha tikuyenera kukhala moyo wathu wonse kumumvera ndi kumutumikira.

Yesu amafuna kuti tonsefe tizimvera malamulo otithandiza kukonzekera kubwelera kukakhala ndi Atate athu Akumwamba. Izi zikuphatikizapo kumvera lamulo la kudzisunga, kupereka chachikhumi ndi kupereka zopereka, kumvera Mawu a Nzeru, kukhala oona mtima nthawi zonse, ndi kusunga tsiku la Sabata kukhala lopatulika.

Kuti tikhale ngati Atate athu Akumwamba tikuyeneranso kulandira miyambo yoperekedwa mu kachisi, odziwika ngati mphatso.* Tikuyenera kutsindikizidwa kumeneko kuti tikhale pamodzi ndi mabanja athu kwa muyaya. Kenako tikuyenera kufufuza mayina ndi mbiri yokhudza achibale athu amene adamwalira ndi kupereka zimene tapeza ku Mpingo, kuti awachitire miyambo yoyenelera m’kachisi.

Yesu watilamula kuti tichite zinthu zambiri. Izi zikuphatikizapo kuuza ena za uthenga wabwino, kuwakonda ndi kuwathandiza, komanso kukhala chitsanzo chabwino kwa iwo.

Tikuyeneranso kusunga malonjezo onse amene timapanga kwa Atate athu Akumwamba, kupezeka pamisonkhano ya mpingo pafupipafupi, kuphunzitsa banja lathu uthenga wabwino powerenga malemba tsiku ndi tsiku, ndi kupemphera tokha komanso ndi banja lathu tsiku lililonse.

Ngati tikhala ndi chikhulupiliro mwa Yesu Khristu ndi kuyesetsa kumvera malamulo ake onse, tidzalandira moyo wosatha ndi kukhala ngati Atate athu Akumwamba.

Kukhala ngati Atate athu Akumwamba kuli ngati kukwera makwelero. Tikuyenera kuyambira pansi ndi kukwera sitepe iliyonse mpaka titafika pamwamba. Mneneri Joseph Smith adanena kuti ngati tikufuna kukhala ngati Atate athu Akumwamba tikuyenera kuphunzira momwe Iwo amamvera, kuganizira, ndi zochita zawo. Tikamvetsetsa zinthu zokhudza Iwozi, tingathe kuphunzira zinthu zina zonse zokhudza Iwo, mpaka titadziwa mmene tingakhalire monga Iwowo.

Zidzatithandiza kukumbukira kuti Atate athu Akumwamba adali munthu amene adakhala padziko lapansi monga momwe ife timakhalira. Iwo adakhala Atate athu Akumwamba pogonjetsa mavuto, monga mmene ife tikuyenela kuchitila pa dziko lapansi. Komabe, Mneneri Joseph Smith adanena kuti sitidzaphunzira zonse zimene tikuyenera kuphunzira tidakali m’dzikoli. Zidzatitengera nthawi yaitali tikamaliza moyo umenewu kuti tidziwe zinthu zonse zimene tikuyenera kudziwa kuti tikhale ngati Atate athu Akumwamba.

Pamene tiphunzira kusunga malamulo onse a Atate athu Akumwamba, taganizirani mmene tidzakhalire osangalala tikamadzabwelera kwa Iwo ndipo akutiuza kuti Ali Osangalala ndi moyo umene takhala ndipo tidzakhala ngati Iwo ndi kukhala nawo kwamuyaya.

Zokambirana

  • Ndi chifukwa chiyani n’zotheka kuti aliyense wa ife kuti akhale ngati Atate athu Akumwamba?

  • Kodi tikuyenera kuchita chiyani kuti tikhale ndi moyo umene Atate athu Akumwamba ali nawo?

  • Kodi Atate athu Akumwamba amatithandiza bwanji kukhala ngati Iwo?

  • Fotokozani mmene mungamvere mutamva Atate athu Akumwamba akukuuzani kuti mwachita bwino ndipo amakukondani.

Print