Zofunikira Zoyambirira
Mutu 33: Kubwera Kwa chiwiri kwa Yesu Khristu


Image
Khristu mu Mwinjiro Wofiira, ndi Minerva K. Teichert

Pali zizindikiro zambiri zosonyeza kuti Kudza Kwa chiwiri kwa Yesu Khristu kwayandikira.

Mutu 33

Kubwera Kwachiwiri kwa Yesu Khristu

Yesu Khristu adzabweranso padziko lapansi. Kodi zizindikiro za kubwera kwake zidzakhala zotani, ndipo tingakonzekere bwanji kudzakumana naye akadzabwera?

Yesu Adalonjeza Kuti Adzabweranso Padziko Lapansi

Patapita masiku 40 kuchokera pamene Yesu adaukitsidwa, iye ndi atumwi ake adakumana paphiri lotchedwa Phiri la Azitona. Nthawi yoti Yesu abwelere kumwamba idali itakwana. Iye adachita zinthu zonse zimene Atate athu Akumwamba adamutuma kuti achite. Atumwi ake adaona pamene Yesu ankakwera kumwamba. Pamene Atumwi adali kuyang’anira, angelo aŵiri adabwera ndi kuwauza kuti Yesu adzabweleranso padziko lapansi. Kuyambira nthawi imeneyo mpaka pano, amene akhulupirira Yesu akuyembekezera kubweranso kwake. Kubweranso kwake kumatchedwa Kubwera Kwachiwiri kwa Khristu.

Pa Kubweranso Kwa chiwiri, Yesu adzatsika kuchokera kumwamba ndi mphamvu zazikulu. Iye adzachotsa kuipa konse padziko lapansi, ndipo Satana sadzakhalanso ndi mphamvu pa anthu. Yesu adzalamulira anthu onse amene akhala okhulupirika kwa iye kwa dzaka chikwi chimodzi.

Zokambirana

  • Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu adzabweranso padziko lapansi?

Yesu Watiuza Zomwe Zidzachitike Asadabwere

Yesu adatiuza zinthu zambiri zimene zidzachitike asadabwerenso. Zinthu izi zikutchedwa zizindikiro za Kudza Kwake Kwa chiwiri. Iye watiuza ife kuti tiyang’ane zizindikiro izi ndi kukhala okonzeka kubwera kwake. Iye adanena kuti tikadzaona zinthu zimenezi zikuchitika, tidzadziwa kuti akubwera posachedwapa. Koma sitidzadziwa nthawi yeniyeni ya kudza kwake.

Ngati tiwelenga malemba ndi kukhala okhulupirika mwa Yesu, tidzadziwa zizindikiro za kubwera kwa Yesu. Zinthu zambiri zidzachitika Yesu asadabwerenso padziko lapansi. Zina zachitika kale, zina zikuchitika tsopano, ndipo zina zidzachitika m’tsogolo.

Kubwera kwachiwiri kwa Yesu kusadachitike, uthenga wabwino udzalalikidwa ku mitundu yonse. Zimenezi zidzasangalatsa anthu ambiri komanso zidzawabweretsera madalitso. Zinthu zina zimene zidzachitike zidzayesa chikhulupiliro chathu. Kudzakhala kuipa kwakukulu, zivomelezi, ndi mitundu ina ya chiwonongeko.

Padziko Lapansi Padzakhala Mavuto Aakulu

Yesu adanena kuti tidzadziwa kuti kubwera kwake kwayandikira tikadzaona zoipa, nkhondo komanso mavuto ambiri padzikoli. Iyi idzakhala nthawi ya mavuto aakulu. Kudzakhala zivomelezi, namondwe wamkulu, matenda, ndi njala. Matalala adzawononga zokolola zapadziko lapansi.

Anthu ambiri adzasiya kukonda Atate athu Akumwamba ndipo adzatembenukira kwa Satana. Adzasiyanso kukonda ndi kutumikira anthu ena ndipo adzayamba kuwavulaza. Padziko lapansi padzakhala nkhondo zambiri. Mitundu idzamenyana wina ndi mzake. Nkhondozi zidzapitilira mpaka nkhondo yaikulu ndiponso yomaliza idzachitike, yomwe idzakhala nkhondo yowononga kwambiri kuposa ina iliyonse imene idamenyedwa padziko lapansi. Kenako Yesu adzabwera.

Uthenga Wabwino Wabwenzeretsedwa

Aneneri adanena kuti uthenga wabwino udzabwenzeretsedwa padziko lapansi Yesu asadabwerenso. Uthenga wabwino wabwenzeretsedwa kudzera mwa Mneneri Joseph Smith. Chiphunzitso chirichonse cha uthenga wabwino chomwe chili chofunikira kuti tidziwe ndi kuchita kuti tibwelere kwa Atate athu Akumwamba chabwenzeretsedwa padziko lapansi.

Yesu adanena kuti tidzadziwa kuti akubwera posachedwa pamene Buku la Mormoni lidali litatsindikizidwa ndi kuperekedwa ku dziko lapansi. Kalekale, mneneri Yesaya ndi Ezekieli adanena za Buku la Mormon. Buku la Mormoni linamasuliridwa ndi Mneneri Joseph Smith mu chinenero cha Chingerezi. Kuyambira nthawi imeneyo lamasuliridwa m’zinenero zambiri. Lidzaperekedwa kwa mitundu yonse ya dziko lapansi Yesu asadabwere.

Nyumba ya Israeli Ikuyenera Kusonkhanitsidwanso

Atate athu Akumwamba adati mbumba za nyumba ya Israeli* zikuyenera kumva ndi kuvomereza uthenga wabwino ndi kukonzekera kukumana ndi Yesu akadzabweranso. Iwo amene amavomereza uthenga wabwino akuyenera kuphunzitsa kwa anthu onse, kumanga makachisi, ndi kuchita miyambo mmalo mwa anthu akufa.

Anthu ambiri ochokera m’nyumba ya Israeli, kaya mwa mwazi kapena mwa kutengedwa kukhala ana awo, akutembenuzidwira ku Mpingo pamene avomereza Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu. Dziko Loyera ladalitsidwa chifukwa chosonkhanitsa ambiri a mbumba za Abrahamu. Mbumba za Abrahamu zikuphatikizapo anthu otchedwa Arabu ndi Ayuda, ndi ena. Mbumba za anthu a Buku la Mormoni ku America, omwenso ali mbumba za Abrahamu, akulandira uthenga wabwino ndipo akukhala anthu amphamvu ndi olungama.

Uthenga Wabwino Udzalalikidwa Padziko Lonse Lapansi

Yesu adanena kuti tidzadziwa kuti akubwera posachedwapa pamene otsatira ake adzalalikira uthenga wabwino padziko lonse lapansi. Kuyambira nthawi imene mpingo udabwezeretsedwa, mamishonale akhala akutumizidwa kukalalikira uthenga wabwino m’mayiko osiyanasiyana. Mamishonale ambiri tsopano akulalikira uthenga wabwino pafupifupi kulikonse padziko lapansi. Aliyense wa mpingo akupemphedwa kuti auze achibale ake ndi abwenzi ake za uthenga wabwino, ndipo ambiri akupita kumayiko ena kukalalikira uthenga wabwino, kuti anthu onse akhale ndi mwayi oumva.

Eliya wabwera

Mneneri Malaki m’Baibulo adanena kuti Yesu asadabwere kachiwiri, mneneri Eliya adzabwera padziko lapansi. Adzabweretsanso ulamuliro wotsindikiza mabanja pamodzi kwamuyaya. Iye adzachititsa anthu kufuna kuphunzira za makolo awo akale ndi mbumba zawo ndi kuwathandiza kuti apulumuke. Mu Epulo 1836, Eliya adabwera ndi kubwenzeretsa ulamuliro umenewu kwa Mneneri Joseph Smith. Chifukwa chakuti Eliya adabwera, mabanja tsopano akhonza kutsindikizidwa pamodzi m’kachisi wapadziko lapansi lero lino.

Mzinda Watsopano wa Yerusalemu Udzamangidwa

Yesu adati tidzadziwa kuti akubwera posachedwapa pamene mpingo wake udzamanga mu mzinda wotchedwa Yerusalemu Watsopano. Yesu adanena kuti adzalamulira mumzindawo ndipo anthu olungama adzakhala mmenemo. Iye watiuza kumene mzindawu udzamangidwa. Zidzakhala m’chigawo cha Missouri, m’dziko la United States.

Izi ndi zizindikiro zochepa chabe zomwe zitiwonetsa kuti Yesu akubwera posachedwa. Malemba amatiuza za zizindikiro zina. Ngakhale kuti zizindikiro zambiri zaoneka kale, sitidziwa nthawi yeniyeni imene Yesu adzabwerenso.

Zokambirana

  • Kodi tikudziwa bwanji kuti Kubwera Kwa chiwiri kwa Yesu kuli pafupi?

  • Kodi zizindikiro za Kubwera Kwa chiwiri kwa Yesu ndi ziti?

Tikhonza Kukhala ndi Mtendere ndi Chiyembekezo Ngakhale Kuti Zoipa ndi Mavuto Zikutizinga

Tikuyenera kukhala okonzekera Kubwera Kwachiwiri kwa Yesu. Njira yabwino kwambiri yokonzekelera kubwera kwake ndi kumvera chiphunzitso chake tsiku lirilonse. Tikuyeneranso kumvera malamulo ndi malangizo amene amapereka kwa Pulezidenti wa Mpingo kwa ife lero. Tikuyenera kukhala oyenera kukhala ndi Mzimu Woyera nthawi zonse kuti utsogolere malingaliro athu ndi zochita zathu. Yesu adanena kuti ngati tikhala okonzeka akadzabwera, sitidzachita mantha. Tidzasangalala ndipo tidzafuna kukhala naye. Anthu abwino sadzawonongedwa akadzabwera. Adzakhala padziko lapansi, ndipo ana awo adzakula opanda uchimo. Yesu adzakhala nawo ndipo adzawadalitsa ndi kuwatsogolera.

Yesu akadzabweranso kuchokera kumwamba, anthu oipa adzawonongedwa. Anthu abwino amene adafa adzauka m’manda awo n’kukakumana naye pamene Iye akuchokera kumwamba. Oipa sadzauka m’manda mpaka patapita dzaka zikwi. Nthawi imeneyi ya dzaka zikwi imatchedwa kuti Mileniyamu.*

Pamene Yesu adali padziko lapansi, anthu ochepa adali kudziŵa kuti iye, Mpulumutsi wa dziko, wabwela. Yesu akadzabweranso, aliyense adzadziwa kuti ndi Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, Mpulumutsi wa dziko lapansi.

Zokambirana

  • Kodi kudziwa zizindikiro za kubweranso kwachiwiri kungatithandize bwanji?

  • Kodi ndi chiyani chidzachitikire anthu abwino padziko lapansi Yesu akadzabweranso?

  • Kodi ndi chiyani chidzachitikire anthu oipa amene adzakhale padziko lapansi panthawiyo?

Print