Zofunikira Zoyambirira
Mutu 10: Malemba


Mutu 10

Malemba

Atate athu Akumwamba atipatsa mabuku anayi opatulika kuti atithandize. Kodi mukudziwa mayina a mabuku anayiwa?

Atate athu Akumwamba Amasonyeza Kuti Amatikonda Potipatsa Malemba Opatulika

Atate athu Akumwamba adauza aneneri kuti alembe zinthu zimene amafuna kuti tizidziwa. Zolemba zimenezi zimatchedwa malemba. Iwo ndi opatulika kwambiri chifukwa zinthu zimene ziri mmenemo zimachokera kwa Atate athu Akumwamba. Ndi zazikulu komanso zofunika kwambiri kuposa chirichonse chimene munthu angalembe popanda thandizo la Atate athu Akumwamba.

Atate athu Akumwamba amatipatsa zolemba izi kuti zitithandize. Poziwerenga tikhonza kuphunzira za dongosolo lalikulu la Atate athu Akumwamba la kwa ife. Tikhonza kuphunzira za moyo wathu ndi Iwo tisanabadwe. Tikhonza kuphunzira za Yesu Khristu. Tikhonza kuphunzira zinthu zimene tikuyenera kuchita kuti tikhale osangalala komanso kuti tikhale ngati Atate athu Akumwamba.

Malemba amenewa amatithandiza kudziŵa kuti Atate athu Akumwamba amatikonda ndipo amafuna kuti tichite zinthu zabwino. Amatiuza za anthu ena amene adaphunzira za Atate athu Akumwamba. Amatiuza kuti Iwo amakonda anthu onse. Timawerenga m’malemba amenewa kuti anthu akasankha kumvera Atate athu Akumwamba, amakhala osangalala ndipo amawathandiza. Akapanda kuwumvera, sasangalala ndipo salandira thandizo lawo.

Zokambirana

  • Kodi malemba ndi chiyani?

  • Kodi tingaphunzire chiyani pa malemba?

Tili ndi Mabuku Anayi a Malemba

Mabuku anayi a malemba ndi Baibulo, Buku la Mormoni, Chiphunzitso ndi Mapangano, ndi Ngale ya Mtengo Wapatali. Onse ali ndi mawu a Atate athu Akumwamba ndi Yesu Khristu. Onse amaphunzitsa ziphunzitso zowona za Atate athu Akumwamba ndi Yesu Khristu.

Baibulo

Mubaibulo muli mawu a Atate athu Akumwamba amene adaperekedwa kwa anthu kuyambira munthawi ya Adamu mpaka pamene Atumwi* a Yesu adakhalako. Mawu awa ndi otinso tiphunzire ndikutsata lero. Baibulo lagawidwa m’magawo awiri. Izi ndi Chipangano Chakale ndi Chipangano Chatsopano.

Chipangano Chakale chimayamba ndi nkhani ya mmene Atate athu Akumwamba adalengera dziko lapansi ndi kutumiza mwamuna ndi mkazi oyamba padziko lapansi. Chipangano Chakale chili ndi nkhani za aneneri ambiri monga Nowa, Abrahamu, Israeli, Mose, Yesaya, ndi Eliya. Nkhanizi zikufotokoza mmene Atate athu Akumwamba ankathandizira anthu pochita zabwino. Zikufotokozanso kuti pamene anthu sadamvere aneneri ndipo sadamvere zimene Atate athu Akumwamba ankaphunzitsa, sakanatha kulandira thandizo lawo.

Chipangano Chatsopano ndi gawo lachiwiri la Baibulo. Limanena nkhani ya kubadwa ndi moyo wa Yesu padziko lapansi. Liri ndi ziphunzitso zabwino za Yesu ndi nkhani zambiri za chikondi chake pa anthu ndi mmene iye adawathandizira. Likufotokoza momwe adayitanira Atumwi kuchokera mwa omutsatira ndi momwe adawaphunzitsira Atumwiwa ndi kuwapatsa mphamvu kuti agwire ntchito yake. Otsatira ake ankadziwa kuti Iye ndi Ambuye. Pambuyo pake olemba adamutcha Iye Ambuye Yesu Khristu.

Chipangano Chatsopano chimanena za mmene Yesu adavutikira ndi kufera anthu onse. Chipangano Chatsopano chikumaliza ndi nkhani za mmene Atumwi ake adaphunzitsira ena za Iye, zinthu zimene zidzachitike Yesu asadabwerenso, ndiponso kutha kwa dziko.

Anthu a dziko lapansi sadalandire Atumwi koma ankawaseka, kuwazunza, ndi kuwapha. Pamene Atumwi ndi aneneri onse adafa, padalibe amene adatsala kuti alembe mawu a Atate athu Akumwamba.

Baibulo liri ndi mawu a Atate athu Akumwamba pokhapokha ngati lamasuliridwa molondora.

Buku la Mormoni

Buku la Mormoni liri ndi ziphunzitso za Atate athu Akumwamba kwa anthu amene ankakhala m’mayiko a ku America. Mbali zina za nkhaniyi zidalembedwa dzaka 2,000 Yesu Khristu asadabadwe. Mbali ina imayamba pafupifupi zaka 600 Yesu Kristu asadabwere ndipo idatha zaka 400 kuchokera pamene Iye adabadwa. Bukuli liri ndi ziphunzitso zofunika za Atate athu Akumwamba. Buku la Mormoni lidalembedwa kuti lithandize anthu nthawi imeneyo komanso tsopano kudziwa kuti Yesu ndi Mpulumutsi wa dziko lonse lapansi.

Zambiri za mu Buku la Mormoni zimanena za gulu la anthu amene adayenda kuchokera ku Yerusalemu kupita ku America. Iwo adayenda ulendowu zaka 600 Yesu Khristu asadabadwe. Iwo ankatsogoleredwa ndi mneneri dzina lake Lehi ndi mwana wake Nefi. Awiri mwa abale ake a Nefi adali oipa ndipo sadamvere abambo awo. Iwo ankatchedwa Lamani ndi Lemueli.

Pamene Lehi adamwalira, anthu a m’banja lake adapatukana m’magulu awiri. Iwo amene adatsatira Nefi ankatchedwa Anefi. Iwo amene adatsatira Lamani ankatchedwa Alamani. Magulu ang’onoang’ono amenewa adakula kukhala mitundu ikuluikulu. Anefi ndi Alamani adamenyana nkhondo zambiri wina ndi mnzake. Atate athu Akumwamba ankadalitsa ndi kuteteza anthu amene ankamvera malamulo awo.

Atate athu Akumwamba adasankha aneneri ambiri kuti aziphunzitsa ndi kutsogolera anthu awo ku America. Nkhani za miyoyo yawo ndi ziphunzitso zawo zimapezeka mu Buku la Mormoni. Ena mwa aneneri ofunika kwambiri mu buku ili ndi Nefi, Yakobo, Benjamini, Alma, Mormoni, ndi Moroni. Amuna onsewa adalemba mbiri ya anthu a Atate athu Akumwamba ku Amerika. Mormoni adatenga zolemba izi zolembedwa ndi aneneri ndipo adaziika izo pamodzi mu buku limodzi.

Aneneri adauza anthuwo kuti Yesu akadzamaliza ntchito yake ku Yerusalemu adzabwera kudzayendera dziko lawo. Yesu adaonekeradi kwa anthu abwino a ku America. Adawaphunzitsa uthenga wabwino* ndi zinthu zimene ayenera kuchita kuti abwelere kwa Atate athu Akumwamba atamwalira.

Anthu adakhulupilira Yesu ndi kumumvera kwa dzaka dzambiri. Iwo adali abwino ndipo ankakhala mwamtendere. Kenako adayamba kuiwala za Yesu. Adasiya kumvera aneneri awo. Iwo akhachita zinthu zoyipa.

Mormoni, mmodzi wa aneneri otsiriza mu bukumu, adapereka mbiri ya anthu ake, Anefi, kwa mwana wake Moroni. Pambuyo pa kuphedwa kwa anthu ake onse mu nkhondo yaikulu ndi Alamani, Moroni adakwilira muphiri mbiri imene aneneri adalemba ya anthu ake.

Mbiriyo idakwiliridwa m’phirimo kwa dzaka mazana ambiri. Potsirizira pake, mu 1820, Atate athu Akumwamba adasankha Joseph Smith kuti akhale mneneri Wawo ndipo adatumiza Moroni, munthu woukitsidwa,* kuti akasonyeze Joseph kumene mbiriyi idakwiliridwa. Joseph adamasulira mbiriyi mu Chingerezi. Lero imadziwika kuti Buku la Mormoni.

Buku la Mormoni lidalembedwa kusonyeza kuti Atate athu Akumwamba amadziwa ndi kukonda anthu kulikonse padziko lapansi. Buku la Mormoni limaphunzitsa kuti Yesu ndi Mpulumutsi wa anthu onse padziko lapansi ndipo ndi Mwana wa Atate athu Akumwamba.

Chiphunzitso ndi Mapangano

Chiphunzitso ndi Mapangano ali ndi mawu a Atate athu Akumwamba kwa anthu a nthawi zamakono. Liri ndi malangizo okonzekera Mpingo wa Yesu Khristu. Likufotokoza ntchito za mamembala ndi atsogoleri. Lilinso ndi ziphunzitso zomwe zidatayika kwa nthawi yaitali kwa anthu a dziko lapansi. Limafotokoza ziphunzitso zina za mubaibulo.

Chiphunzitso ndi Mapangano ali ndi mauthenga kwa ife amene tikukhala lero. Limatichenjeza za zinthu zimene zidzachitike ngati sitimvera Atate athu Akumwamba. Limatiuzanso za zinthu zodabwitsa zimene Atate athu Akumwamba atikonzera ngati tiwamvera.

Ngale Yamtengo Wapatali

Ngale ya Mtengo Wapatali ili ndi buku la Mose, buku la Abrahamu, ndi zolemba zina zouliridwa za Joseph Smith.

M’buku la Mose muli masomphenya amene Atate athu Akumwamba adapereka kwa Mose. Likufotokoza za Kulengedwa kwa dziko lapansi. Liri ndi ziphunzitso zimene zidasochera m’Baibulo.

Buku la Abrahamu limasimba za Kulengedwa kwa dziko lapansi ndi za Atate athu Akumwamba ndi mphamvu Yawo.

Zolemba za Joseph Smith zimafotokoza momwe Atate athu Akumwamba adamuyitanira kuti akhale mneneri. Amaphatikizanso zina mwa zomwe iye adamasulira za Baibulo ndi mawu olongosola zina za zikhulupiliro za Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza. Mawu awa amatchedwa Mfundo za Chikhulupiliro.

Mneneri wa Atate athu Akumwamba amene ali ndi moyo lero amalembanso zinthu zimene Atate athu Akumwamba amamuuza. Atate athu Akumwamba adadziwitsa zinthu zambiri zazikulu ndi zofunika kwa aneneri m’mbuyomu. Iwo akupitiriza kudziwitsa zinthu zazikulu ndi zofunika kwa mneneri Wawo lero lino.

Zokambirana

  • Kodi mabuku anayi a m’Malemba amene tili nawo masiku ano ndi ati?

  • Ndichifukwa chiyani buku lililonse la mabuku amenewa lili lofunika kwa ife?

Atate athu Akumwamba Adzatithandiza Tikamaphunzira Malemba

M’Malemba, Atate athu Akumwamba amatiphunzitsa dongosolo Lawo lakuti tibwelere kwa Iwo. Powerenga malemba tikhoza kuphunzira zinthu zimene Iwo amafuna kuti tidziwe ndi kuchita. Ngati sitiwerenga malemba, sitidzadziwa zimene ziri mmenemo. Sitidzadziwa zimene Atate athu Akumwamba akufuna kuti tichite.

Tikuyenera kuwerenga malemba tsiku lirilonse. Tikuyeneranso kuwerenga kwa mabanja athu kuchokera m’malemba. Tikuyenera kuthandiza mabanja athu kumvetsetsa malemba. Tikuyenera kuphunzitsa ana athu kuti awa ndi mabuku opatulika ochokera kwa Atate athu Akumwamba. Tikuyenera kuwathandiza kudziwa zimene ziri m’mabuku amenewa komanso kuti aziyamika pa iwo.

Zokambirana

  • Kodi Atate athu Akumwamba angatithandize bwanji tikamawerenga malemba?

Print