Malembo Oyera
2 Nefi 29


Mutu 29

Amitundu ambiri adzakana Buku la Mormoni—Iwo adzati, Sitikufuna Baibulo lina—Ambuye amayankhula ku maiko ambiri—Iye adzaweruza dziko lapansi kuchokera m’ma buku amene adzalembedwa. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Koma taonani, padzakhala ambiri—patsiku limenelo pamene ndidzapitilize kugwira ntchito yodabwitsa pakati pawo, kuti ndikakumbukire mapangano anga amene ine ndidapanga kwa ana a anthu, kuti ndidzayikenso dzanja langa kachiwiri kulanditsa anthu anga, amene ali a nyumba ya Israeli;

2 Ndiponso, kuti ndikumbukire malonjezano amene ine ndidapanga kwa iwe, Nefi, ndiponso kwa atate ako, kuti ndidzakumbukira mbewu yako; ndipo kuti mawu a mbewu yako ikuyenera kudzatuluka kudzera mkamwa mwanga kupita kwa mbewu yanu; ndipo mawu anga adzamveka kufikira kumalekezelo a dziko lapansi, kukhala muyeso wa anthu anga, amene ali a nyumba ya Israeli.

3 Ndipo chifukwa mawu anga adzamveka—ambiri mwa Amitundu adzati: Baibulo! Baibulo! Ife tiri nalo Baibulo, ndipo sipangathe kukhalanso Baibulo linanso.

4 Koma akutero Ambuye Mulungu: Inu opusa, adzakhala ndi Baibulo; ndipo lidzachokera kwa Ayuda, anthu anga akale achipangano. Ndipo kodi iwo amawathokoza Ayuda chifukwa cha Baibulo limene adalandira kudzera kwa iwo? Inde, kodi Amitundu akutanthauza chiyani? Kodi iwo amakumbukira mazunzo, ndi ntchito, ndi zowawa za Ayuda, ndi khama lawo kwa ine, m’kubweretsa chipulumutso kwa Amitundu?

5 Inu Amitundu, kodi mwawakumbukira Ayuda, anthu anga akale apangano? Ayi; koma inu mwawatembelera iwo, ndipo mwadana nawo, ndipo simudafune kuwabwenzeretsa iwo. Koma taonani, ine ndidzabwenzera zinthu zonsezi pa mitu yanu; pakuti ine Ambuye sindidaiwale anthu anga.

6 Wopusa iwe, amene umati: Baibulo, ife tiri ndi Baibulo, ndipo ife sitikusowanso Baibulo lina. Kodi mwapeza Baibulo kupatulapo kudzera kwa Ayuda?

7 Kodi inu simukudziwa kuti maiko a anthu aposa amodzi? Kodi simudziwa kuti ine, Ambuye Mulungu wanu, ndidalenga anthu wonse, ndipo ndimakumbukira iwo amene ali pa zilumba za nyanja; ndipo kuti ndimalamulira thambo la m’mwamba ndi pansi pa dziko; ndipo ndimabweretsa mawu kwa ana a anthu, inde, ngakhale pa maiko wonse a dziko lapansi?

8 Kotero mukung’ung’udza, chifukwa chakuti mudzalandira ambiri a mawu anga? Kodi simukudziwa kuti umboni wa mafuko awiri ndi mboni kwa inu kuti ine ndi Mulungu, kuti ine ndimakumbukira mtundu umodzi monga wina? Kotero, ndimayankhula mawu omwewo kwa mtundu umodzi ngati unzake. Ndipo pamene maiko awiri adzathamangira limodzi, umboni wa maiko awiriwa udzathamangira limodzinso.

9 Ndipo ndimapanga zimenezi kuti ndikatsimikizire kwa ambiri kuti ine ndi yemweyo dzulo, lero, ndi kunthawi zonse; ndipo kuti ndimayankhula mawu anga monga mwa kufuna kwanga. Ndipo chifukwa chakuti ndayankhula mawu amodzi simukuyenera kuganiza kuti sindingathe kuyankhula ena; pakuti ntchito yanga siidathe; ngakhalenso siidzatha kufikira mapeto a munthu, kapena kuyambira pa nthawi imeneyo ndi ku nthawi zosatha.

10 Kotero, chifukwa chakuti muli ndi Baibulo simukuyenera kuganiza kuti liri ndi mawu anga wonse; ngakhalenso simukuyenera kuganiza kuti sindidapangitse kuti zambiri zilembedwe.

11 Pakuti ndimalamula anthu wonse, wonse aku m’mawa ndi kumadzulo, ndipo ku mpoto ndi kumwera, ndi ku zilumba za nyanja, kuti iwo alembe mawu amene ine ndayankhula kwa iwo; pakuti kuchokera m’mabuku amene adzalembedwa ine ndidzaweruza dziko lapansi, munthu aliyense monga mwa ntchito zake, monga mwa chomwe chalembedwa.

12 Pakuti taonani, ndidzayankhula kwa Ayuda ndipo adzachilemba; ndipo ndidzayankhula kwa Anefi ndipo iwo adzachilemba; ndipo ndidzayankhulanso kwa mafuko ena a nyumba ya Israeli, amene ndawatsogolera kutali, ndipo adzachilemba, ndipo ndidzayankhula kwa maiko wonse a dziko lapansi ndipo adzazilemba.

13 Ndipo zidzachitika kuti Ayuda adzakhala ndi mawu a Anefi, ndipo Anefi adzakhala ndi mawu a Ayuda; ndipo Anefi ndi Ayuda adzakhala ndi mawu a mafuko otaika a Israeli; ndipo mafuko otaika a Israeli adzakhala ndi mawu a Anefi ndi Ayuda.

14 Ndipo zidzachitika kuti anthu anga, amene ali a nyumba ya Israeli, adzasonkhanitsidwa kwawo ku maiko a cholowa chawo; ndipo mawu anganso adzasonkhanitsidwa pamodzi. Ndipo ndidzaonetsa kwa iwo amene alimbana ndi mawu anga ndi kumenyana ndi anthu anga, amene ali a nyumba ya Israeli, kuti ine ndi Mulungu, ndipo kuti ndalonjezana ndi Abrahamu kuti ndidzakumbukira mbewu yake kwa muyaya.

Print