Zofunikira Zoyambirira
Mutu 15: Ubatizo


Mutu 15

Ubatizo

Kubatizidwa ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri zimene mungachite padzikoli. Nchifukwa chiyani ubatizo ndi wofunika kwambiri? Kodi njira yolondola yobatizidwira ndi iti?

Atate athu Akumwamba Adatilamula Kuti Tibatizidwe

Kubatizidwa kumatanthauza kuikidwa kwathunthu pansi pa madzi kwa kamphindi ndi kudzutsidwanso ndi munthu amene ali ndi ulamuliro wochita ubatizo. Ubatizo ndi gawo la dongosolo la Atate athu Akumwamba kwa ife. Iwo amatilamula kuti tizibatizidwa pofuna kusonyeza kuti timakhulupilira Yesu Khristu, timawakonda komanso timafuna kuwamvera komanso kuti talapa machimo athu.

Yesu adadziwa kuti Atate athu Akumwamba adalamula ana awo onse kuti abatizidwe. Pamene Yesu adali padziko lapansi, adabatizidwa. Iye adachita zimenezi chifukwa ankafuna kumvera Atate athu Akumwamba. Ankafunanso kutisonyeza kuti tikuyenera kumvera Atate athu Akumwamba ndi kubatizidwa.

Munthu aliyense amene wafika zaka zisanu ndi zitatu, amene amadziwa chabwino ndi choipa, ndiponso amene ali ndi chikhulupiliro mwa Yesu ndipo walapa akuyenera kubatizidwa. Ana osapitilira dzaka zisanu ndi zitatu safunika kubatizidwa. Atate athu Akumwamba samawaweruza chifukwa cha zomwe amachita. Komanso anthu amene maganizo awo sakutha kuzindikira chabwino ndi choipa safunikira kubatizidwa. Anthu ena onse ayenera kubatizidwa ngati akufuna kubwelera kukakhala ndi Atate athu Akumwamba.

Yesu adatiuza nthawi imene tikuyenera kubatizidwa. Iye adauza otsatira ake kuti abatize anthuwo ataphunzira za Iye, kumukhulupilira, ndi kulapa. Iye adapatsa ena mwa azibambo mu mpingo Wake ulamuliro wobatiza anthu.

Zokambirana

  • Ndi chifukwa chiyani Atate athu Akumwamba amafuna kuti tibatizidwe?

  • Ndi chifukwa chiyani Yesu adabatizidwa?

  • Ndani akuyenera kubatizidwa?

Image
Yohane Kubatiza Yesu, ndi Harry Anderson

Khristu adabatizidwa ndi Yohane M’batizi.

Kubatizidwa Ndi Chimodzi mwa Zinthu Zofunika Kwambiri Zimene Tingachite

Pobatizidwa, timaonetsa Atate athu Akumwamba kuti tikufuna kutsatira dongosolo lawo la kwa ife. Timalonjeza kuti tidzalandira Yesu kukhala mtsogoleri wathu ndi kumvera zonse zimene amatiuza kuti tichite. Timalonjeza kuti tidzimukumbukira nthawi zonse komanso zinthu zimene watichitira.

Tikayika chikhulupiliro chathu mwa Yesu Khristu, kulapa machimo athu, ndi kubatizidwa, Atate athu Akumwamba amatikhululukira machimo athu. Iwo Amatilonjeza kuti tikhonza kubwelera kukakhala nawo. Amatilandira ife ngati mamembala a Mpingo wa Yesu. Amatumiza Mzimu Woyera kuti utithandize kuphunzira zambiri za Iwo ndi kutithandiza kuchita zinthu zoyenera. Timalandila madalitso onsewa ngati tipitiliza kuchita zimene tidalonjeza tikabatizidwa.

Tingalandire madalitso amenewa pokhapokha ngati ndife obatizidwa. Iyi ndi njira yokhayo yoti tibwelere kukakhala ndi Atate athu Akumwamba. Iyi ndi njira yokhayo kuti ife tikhale mamembala a Mpingo wa Yesu Khristu. Iyi ndi njira yokhayo yoti tilandire mphatso ya Mzimu Woyera, yomwe ndi ufulu woti Mzimu Woyera utithandize m’miyoyo yathu. Mphatso imeneyi imaperekedwa kwa ife tikabatizidwa. Zinthu zonsezi ndi zofunika kuti tibwelere kukakhala ndi Atate athu Akumwamba.

Zokambirana

  • Kodi timalonjeza chiyani kwa Atate athu Akumwamba tikamabatizidwa?

  • Kodi Atate athu Akumwamba amalonjeza chiyani kwa ife tikabatizidwa?

  • Nchifukwa chiyani ubatizo ndi wofunika kwambiri?

Tiyenera Kukonzekera Tokha Kuti Tibatizidwe

Tiyenera kuchita zinthu zina tisanakonzekere kubatizidwa. Tiyenera kuphunzira za Yesu Khristu ndi kukhulupilira mwa Iye, kulapa machimo athu, ndi kuchita zimene Yesu adatilamula kuchita.

Zokambirana

  • Kodi tikuyenera kuchita chiyani kuti tikonzekere ubatizo?

Image
munthu akubatizidwa

Tiyenera kubatizidwa mwa kumizidwa kuti tikhululukidwe machimo athu.

Ubatizo Umatipatsa Chiyambi Chatsopano

Ubatizo umatithandiza kuyamba moyo watsopano, woyera ku uchimo. Nthawi ina Yesu adanena kuti zili ngati kubadwanso mwatsopano. Iye adanena kuti ngati sitibadwanso mwauzimu, sitingabwelere kukakhala ndi Atate athu Akumwamba.

Mmodzi mwa otsatira a Yesu, dzina lake Paulo, adanena kuti tikuyenera kuyamba moyo watsopano tikabatizidwa. Iye adanena kuti tikaikidwa m’madzi kuti tibatizidwe, zili ngati kukwilira machimo athu onse. Tikatuluka m’madzi, zimakhala ngati takhala munthu woyera, watsopano, wokonzeka kuyamba moyo watsopano. Ubatizo umatiyambitsa ife panjira yobwelera kwa Atate athu Akumwamba.

Print