Zofunikira Zoyambirira
Mutu 16: Mphatso ya Mzimu Woyera


Image
mzimayi akudalitsidwa

Tiyenera kulandira mphatso ya Mzimu Woyera pa kusanjikidwa manja.

Mutu 16

Mphatso ya Mzimu Woyera

Mzimu Woyera umatithandiza kudziwa ndi kumvetsa zinthu zomwe ziri zoona. Kodi tingalandire bwanji mphatso ya Mzimu Woyera?

Mzimu Woyera Ukhoza Kutitsogolera ku Choonadi

Mzimu Woyera ukhoza kuthandiza anthu asanabatizidwe. Amatha kuuza munthu kuti ziphunzitso za Yesu ndi zoona. Nthawi zina amatiuza komwe tingapeze Mpingo woona wa Yesu Khristu. Koma Mzimu Woyera sudzakhala ndi ife mpaka ife titabatizidwa ndi kupatsidwa mphatso ya Mzimu Woyera.

Mu Chipangano Chatsopano timawerenga za munthu wina dzina lake Koneliyo. Iye adali munthu amene adali asadabatizidwe. Mzimu Woyera udamuuza iye kuti ziphunzitso za Yesu zinali zoona. Kenako Koneliyo adabatizidwa ndipo adalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

Atate athu Akumwamba Atipatsa Njira Yolandilira Mphatso ya Mzimu Woyera

Pamene tikuphunzira za dongosolo la Atate athu Akumwamba kwa ife, timafuna kulapa machimo athu ndi kumvera zonse zimene Yesu amatiuza kuchita. Koma sitingachite zimenezi popanda thandizo. Mphatso ya Mzimu Woyera ndi ufulu wokhala ndi chithandizo kuchokera kwa Mzimu Woyera nthawi zonse. Timalandira mphatso imeneyi tikangobatizidwa.

Tiyenera kukonzekera kuti tilandire mphatso ya Mzimu Woyera. Tiyenera kukhulupilira Yesu ndi kuyesetsa kuchita zimene Iye amatilamulira. Tiyenera kulapa machimo athu ndi kubatizidwa.

Tikabatizidwa, iwo amene ali ndi ulamuliro kuchokera kwa Atate athu Akumwamba amayika manja awo pa mutu pathu, kutipatsa ife mphatso ya Mzimu Woyera, ndi kutipanga ife mamembala ovomerezeka a Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza. Iwo amatidalitsanso.

Zokambirana

  • Kodi timalandila bwanji mphatso ya Mzimu Woyera?

Pali njira zambiri zomwe mphatso ya Mzimu Woyera ingatithandizire. Akhoza kutibweretsera mauthenga ochokera kwa Yesu. Iye angatiphunzitse zinthu zambiri zokhudza Yesu ndi Atate athu Akumwamba.

Angatithandize kudziwa mmene tingathetsere mavuto athu. Akhoza kutitonthoza. Iye angatithandize kuti tigonjetse machimo athu. Akhonza kutithandiza kuchita zinthu zoyenera.

Mzimu Woyera ukhonza kutithandiza kumvetsetsa ndi kukonda ena. Akhonza kutithandiza kudziwa mmene tingawathandizire. Iye akhonza kutithandiza kumvetsa ziphunzitso za Yesu. Iye akhonza kutithandiza kudziwa zimene tinganene pophunzitsa anthu za Atate athu Akumwamba ndi Yesu.

Zokambirana

  • Ndi njira ziti zina zomwe mphatso ya Mzimu Woyera ingakhudzire miyoyo yathu?

Tiyenera Kulapa Machimo Athu Kuti Tikhale Ndi Mphatso iyi

Kudzera mu mphatso ya Mzimu Woyera tikhonza kukhala anthu abwino ndikuchita zinthu zabwino. Tikhonza kukhala ngati Atate athu Akumwamba. Koma tiyenera kuyesetsa nthawi zonse kuchita zinthu zabwino, kapena Mzimu Woyera sungakhale nafe. Tiyenera kuyesetsa kuganiza bwino. Tiyenera kuyesetsa kutsatira ziphunzitso za Yesu. Tikachita chinthu cholakwika, tiyenera kulapa. Pamene tikuyesera kuchita zinthu zonsezi, Mzimu Woyera umatithandiza.

Nthawi zina Mzimu Woyera umatitsogolera potipangitsa kukhala ndi malingaliro abwino, amtendere mumitima yathu. Tikayamba kuchita zinthu zolakwika, chimwemwe chimenechi chimatisiya. Nthawi zina titha kumva mawu m’maganizo mwathu akutiuza zimene tiyenera kuchita kapena kusachita. Nthawi zonse tiyenera kukhala okonzeka kumvetsera ndi kumvera zimene Mzimu Woyera amatiuza, chifukwa Mzimu Woyera amatiuza nthawi zonse zimene Yesu akufuna kuti tichite, ndipo ndipakumvera Yesu pokha pamene tingabwelere kwa Atate athu Akumwamba.

Ngati ife sitimvera Mzimu Woyera ndipo ngati ife tiyamba kuchita zinthu zolakwika, Mzimu Woyera umatisiya ife. Iye sadzakhala nafe kapena kutithandiza ngati sitichita zabwino. Koma ngati timvera chitsogozo Chake, Mzimu Woyera udzakhala nafe nthawi zonse. Iye amatithandiza kukhala anthu abwino ndi kukonzekera moyo wokakhala ndi Atate athu Akumwamba.

Zokambirana

  • Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mzimu Woyera utithandize?

Timalandila Madalitso Ena Apadera kudzera mwa Mzimu Woyera

Madalitso ena apadera omwe timalandira kudzera mwa Mzimu Woyera amatchedwa mphatso zauzimu. Yesu amapereka mphatso zimenezi kwa mamembala a mpingo wake woona pamene mpingo Wake uli padziko lapansi. Iye amatipatsa ife mphatso zimenezi kudzera mu mphamvu ya Mzimu Woyera. Tikufunikira kumvetsa bwino mphatso zimenezi kuti tizizigwiritsa ntchito mwanzeru.

Mphatso Yoyankhula Zinenero Zina

Mphatso imodzi imathandiza anthu kuyankhula zinenero zina. Chifukwa chimodzi chimene Yesu adapereka mphatso imeneyi kwa anthu n’chakuti aziwaphunzitsa uthenga wabwino kwa anthu olankhula zinenero zina.

Mphatso Yomasulira Chinenero China

Mphatso ina imathandiza anthu amene akuuzidwa za uthenga wabwino. Mphatso yomasulira ziyankhulo zina imawathandiza kumvetsa uthenga wochokera kwa Yesu woyankhulidwa m’chinenero chimene sachidziwa.

Mphatso Yodziwa Kuti Yesu Ndi Mwana wa Atate athu Akumwamba

Mphatso ina imathandiza anthu kudziwa kuti Yesu ndi Mwana wa Atate athu Akumwamba. Malemba amanena kuti anthu angathe kudziwa kuti Yesu ndi Mpulumutsi pokhapokha ngati Mzimu Woyera wawathandiza kudziwa. Mphatso imeneyi ndi umboni wochokera kwa Mzimu Woyera kuti Yesu ndiyedi Mwana wa Atate athu Akumwamba komanso kuti ndi Mpulumutsi wa dziko lapansi.

Mphatso Yokhulupilira Umboni wa Ena

Mphatso yokhulupilira umboni wa ena imathandiza anthu kudziwa ngati zimene munthu wina amanena zokhudza Yesu ndi zoona. Mzimu Woyera umatithandiza kuzindikira umboni woona ndi kuukhulupilira.

Mphatso ya Chikhulupiliro

Mphatso ya chikhulupiliro imatithandiza kumvera malamulo a Yesu. Popanda chikhulupiliro sitingalandire mphatso zina zauzimu. Popanda chikhulupiliro sitingathe kubwelera kwa Atate athu Akumwamba. Anthu ambiri ali ndi chikhulupiliro cholimba mwa Yesu. Mmodzi wa aneneri mu Buku la Mormoni anali ndi chikhulupiliro chachikulu mwa Yesu kotero kuti Yesu adawonekera kwa iye. Mneneri Joseph Smith adali ndi chikhulupiliro cholimba mwa Yesu Khristu mpakana Atate athu Akumwamba ndi Yesu adawonekera kwa iye.

Mphatso Yomasulira

Mphatso yomasulira imathandiza anthu kumasulira mawu olembedwa a Atate athu Akumwamba komanso a Yesu ndi otsatira ake kuchokera m’chinenero china kupita ku china. Mneneri Joseph Smith adali ndi mphatso imeneyi pamene adamasulira Buku la Mormoni. Mphatso imeneyi imathandiza womasulirayo kumvetsa tanthauzo lolondola la uthengawo, kenako amaumasulira molondola.

Mphatso Yachidziwitso

Mphatso ya chidziwitso imathandiza anthu kumvetsetsa ntchito ya Atate athu Akumwamba ndi Yesu. Atate athu Akumwamba adanena kuti sitingathe kubwelera kwa Iwo ngati sitidziwa kapena kumvetsa zimene akufuna kuti tichite. Tiyenera kudziwa dongosolo lomwe Atate athu Akumwamba Atipatsa kuti tibwelere kwa Iwo.

Yesu wanena kuti chidziwitso chomwe timapeza m’moyo uno chidzatithandiza kudziko la mizimu tikamwalira. Iye amafuna kuti tidziŵe ziphunzitso ndi malamulo ake, za kumwamba ndi dziko lapansi, zinthu zimene zachitika, ndi zinthu za m’maiko athu ndi m’maiko ena. Iye wanena kuti tiyenera kugwiritsa ntchito nzeru imeneyi mwanzeru. Tikuyenera kupempha thandizo la Mzimu Woyera pofunafuna chidziwitso.

Mphatso ya Nzeru

Mphatso imeneyi imathandiza anthu kugwilitsila nchito m’njila yoyenela chidziŵitso cha Atate athu Akumwamba. Tiyenera kugwiritsa ntchito mphatso imeneyi kuti tiwongolere moyo wathu, kuphunzitsa ndi kupereka uphungu wanzeru kwa ena.

Mphatso ya Kuphunzitsa

Mphatso ya kuphunzitsa imathandiza anthu kuphunzitsa uthenga wabwino m’njira yokuti amvetse. Tingapeze mphatso imeneyi mwa kukhulupilira Yesu, kuphunzira ndi kupemphera.

Mphatso ya Ulosi

Mphatso ya ulosi imathandiza anthu kudziwa ndi kumvetsa zinthu zimene zidachitika kale, zimene zikuchitika masiku ano komanso zimene zidzachitike m’tsogolo. Aneneri adapatsidwa mphatso imeneyi, koma ifenso tingakhale nayo kuti ititsogolere pa moyo wathu.

Mphatso ya Chivumbulutso*

Mzimu Woyera umaululira anthu zinthu zimene zingawathandize. Aliyense wa ife akhonza kulandira vumbulutso kuti tithandizike. Koma mavumbulutso a Mpingo wonse amaperekedwa kwa mneneri yekha. Sitingathe kulandira vumbulutso kwa munthu amene ali mtsogoleri wathu mu mpingo. Chilichonse chimene Mzimu Woyera amatiululira chidzagwirizana ndi malamulo ndi ziphunzitso za Atate athu Akumwamba ndi Yesu.

Mphatso Yamachiritso

Mphatso ya machiritso imathandiza anthu odwala kuchira. Ena ali ndi chikhulupiliro choti achiritsidwe ndipo ena ali ndi chikhulupiliro chochiritsa anthu ena.

Mphatso Yochita Zozizwitsa

Mphatso yochita zozizwitsa imaperekedwa kuti ithandize anthu. Chozizwitsa ndi chinthu chimene Atate athu Akumwamba amatichitira chimene chili chachikulu kuposa mphamvu imene tiri nayo tokha. Yesu adanena m’Chipangano Chatsopano ndi m’Buku la Mormoni kuti padzakhala zozizwitsa pakati pa iwo amene akhulupilira mwa Iye.

Satana Akhonza kutsanzira Mphamvu Zauzimu Izi

Satana akhonza kuchititsa zinthu zimene zimatsanzira mphatso zenizeni zauzimu. Akhonza kudzipanga kukhala ngati mngelo. Akhonza kuchititsa zinthu zoipa kuoneka ngati zabwino ndi zolondola. Akhonza kupangitsa mneneri wonyenga kuoneka ngati mneneri woona. Iye amatha kuchita zozizwitsa kuti anyenge anthu. Anyanga, olankhula ndi mizimu, olosera, ndi ena onga iwo amalandira mphamvu zimene ali nazo kwa Satana ndipo sali otsatira a Yesu. Tiyenera kukhala kutali ndi iwo.

Satana akhonza kupangitsa kuti zinthu zizioneka ngati zoona moti njira yokhayo imene tingadziwire kuti ndi yabodza ndiyo kufunsa Atate athu Akumwamba. Tidzakhala ndi malingaliro okayikitsa, osati amtendere, pamene Satana kapena otsatira ake atsanzira mphatso zauzimu. Mphatso yodziwa pamene mphatso zauzimu zili zenizeni ndiponso pamene zili zotsanzira Satana imatchedwa mphatso ya chizindikiritso.

Zokambirana

  • Kodi mphatso zauzimu ndi chiyani?

  • Kodi tingasiyanitse bwanji mphatso zauzimu zenizeni ndi zotsanzira za Satana?

Tikuyenera Kugwira Ntchito Kukulitsa ndi Kugwiritsa Ntchito Mphatso Zomwe Tiri Nazo

Tikhonza kuziphunzira mphatso zimene tiri nazo ngati tiphunzira, kusala kudya, ndi kupemphera. Tikhonza kugwiritsa ntchito mphatso zathu pokhapokha titamvera malamulo a Yesu. Tikatero tidzafuna kuzigwiritsa ntchito pothandiza ena ndi kuthandiza kumanga Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza. Ngati sitikulitsa ndi kugwiritsa ntchito mphatso zathu, zidzatitayika.

Yesu adanena kuti sitikuyenera kudzitamandira chifukwa cha mphatso zauzimu zimene tadalitsidwa nazo. Sitikuyenera kulankhula za izo kwa anthu amene sangazione kukhala zopatulika. Mphatso zimenezi zimaperekedwa kwa ife kuti zitithandize ife ndi kudalitsa anthu ena. Tizikumbukira kuti mphatso zimenezi ndi zopatulika. Yesu amatipatsa ife mphatso izi kudzera mwa Mzimu Woyera. Amangopempha kuti tizimuthokoza komanso kugwiritsa ntchito mphatso zimenezi mmene iye amafunira kuti zigwiritsidwe ntchito.

Zokambirana

  • Kodi tingadziŵe bwanji mphatso zimene tili nazo?

  • Kodi timasunga bwanji mphatso zauzimu kukhala zopatulika?

Mphatso ya Mzimu Woyera Ikhonza kukhala Yamtengo Wapatali kwa Ife

Nthawi zonse tiyenera kuyesetsa kuchita zabwino ndi kumvera Yesu, apo ayi mphamvu ya Mzimu Woyera singakhale ndi ife. Tiyenera kuyesetsa kuganiza bwino. Tikachita chinthu cholakwika, tiyenera kulapa. Tiyenera kuyesa kumvetsetsa zinthu zomwe Mzimu Woyera umatiuza. Tiyenera kutsatira malangizo amene umapereka.

Ngati tifunitsitsa kumvera Yesu, mphatso ya Mzimu Woyera idzadalitsa miyoyo yathu. Zidzatithandiza kukhala ndi moyo wosangalala panopa komanso kukonzekera kukakhala ndi Atate athu Akumwamba.

Zokambirana

  • Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mzimu Woyera utithandize?

Print