Zofunikira Zoyambirira
Mutu 11: Moyo wa Yesu Khristu


Image
Onani Mwana wankhosa wa Mulungu, wolemba Walter Rane

Mpulumutsi, Yesu Khristu, adabadwira m’khola. Yesu ali mnyamata adaphunzitsa anthu ophunzira m’kachisi.

Mutu 11

Moyo wa Yesu Khristu

Yesu Khristu ndiye yekhayo amene angatitsogolere kuti tibwelere kwa Atate athu Akumwamba. Mukudziwa chiyani za Iye?

Anthu ambiri Adadikira ndi Chikhumbo Chachikulu cha Kubwera kwa Yesu Khristu

Yesu adadzipereka kukhala Mpulumutsi wathu. Iye adanena kuti adzabwera padziko lapansi kudzatisonyeza mmene tingabwelere kwa Atate athu Akumwamba. Anthu ambiri amene adakhalako Yesu asadabadwe ankakhulupilira kuti iye adzakhala Mpulumutsi wawo. Iwo ankayembekezera kudza kwake. Iwo ankadziwa kuti akhonza kuwapulumutsa kuti asalandire chilango chamuyaya chifukwa cha machimo awo.

Aneneri onse amene adakhalako Yesu asadabadwe adauza anthu kuti iye adzabwera. Atate athu Akumwamba adatumiza mngelo kukauza Adamu kuti Yesu adzabwela padziko lapansi.

Zaka zambiri Yesu asadabadwe, mneneri wina dzina lake Yesaya adaona m’masomphenya kuti Yesu adzazunzika kuti alipire machimo athu. Yesaya adati anthu adzadana ndi kukana Yesu ndipo Yesu adzamva chisoni chachikulu.

Nefi, mneneri amene timamuwerenga mu Buku la Mormoni, adawona zinthu zomwe Yesu atadzachite. Nefi adaona zinthu izi zaka zambiri Yesu asadabadwe. Adaona Yesu wakhanda ali m’manja mwa amayi ake. Mngelo adauza Nefi kuti mwanayo adali Mwana wa Atate athu Akumwamba.

Timawerenga za mneneri wotchedwa Benjamin mu Buku la Mormoni. Adauza anthu kuti Yesu abwela padziko lapansi posachedwa. Benjamini adawauza kuti Yesu adzachiritsa odwala, kuchititsa olumala kuyenda, kuchititsa akhungu kupenya, ndi kupangitsa ogontha kumva. Adzatulutsanso mizimu yoipa ndi kuukitsa anthu akufa. Benjamini adanena kuti Yesu adzaphunzitsa anthu kukonda Atate athu Akumwamba ndi kukondana wina ndi mnzake.

Aneneri onse amene adakhalako Yesu atabadwa amatiuza kuti iye adabweradi. Popanda Yesu Khristu, dongosolo la Atate athu Akumwamba likadalepheleka.

Zokambirana

  • Ndichifukwa chiyani Yesu adalonjeza kuti adzabwela padziko lapansi?

  • Kodi ena mwa aneneri amene adachitira umboni kuti Iye adzabwera adali ndani?

Kubadwa kwa Yesu Kudabweretsa Chimwemwe Chachikulu Padziko Lapansi

Yesu adabadwira m’nzinda waung’ono wotchedwa Betelehemu. Angelo adayimba pamene Iye adabadwa chifukwa adali osangalala kwambiri. Kumwamba kudaonekera nyenyezi yatsopano. Abusa ndi anthu anzeru adapita kukamuona ndi kumulambira. Anthu ambiri padziko lonse amakondwelerabe kubadwa kwake.

Yesu adali wosiyana ndi mwana aliyense amene adabadwa. Atate a Yesu adali Atate athu Akumwamba. Atate athu Akumwamba sadali Atate wa mzimu wa Yesu yekha komanso Atate a thupi Lake la mnofu ndi mafupa. Yesu adalandira mphamvu kuchokera kwa Atate ake zimene anthu ena alibe. Anthu sakadatha kutenga moyo wake pokhapokha atawalola kuutenga. Iye atafa, Iye adali ndi mphamvu yopangitsa thupi Lake kukhala lamoyo kachiwiri.

Amayi ake a Yesu adali Mariya. Iye adali mtsikana wangwiro amene adakhalako dzaka pafupifupi 2,000 zapitazo m’nzinda wotchedwa Nazareti. Pamene adali namwali wamng’ono, asadakwatiwe, mngelo wochokera kwa Atate athu Akumwamba adabwera kwa iye. Mngeloyo adamuuza kuti adzakhala mayi wa Yesu Khristu. Mngeloyo adamuuza kuti Atate athu Akumwamba adzakhala Atate a Yesu. Palibe munthu padziko lapansi amene akadakhala Atate ake.

Mngeloyo adafikanso kwa mwamuna amene Mariya ankafuna kumukwatira. Munthuyo dzina lake adali Yosefe. Mngelo adauza Yosefe kuti mwana amene adzabadwe adzakhala Mwana wa Atate athu Akumwamba osati mwana wa munthu aliyense padziko lapansi. Mngeloyo adamuuza kuti akwatile Mariya. Choncho Yosefe ndi Mariya adakwatirana. Yesu atabadwa, Yosefe adamusamalira ngati kuti Yesu adali mwana wake.

Popeza kuti amayi ake adali oti adzafa, Yesu ankamva njala, ludzu, ndi zowawa, ndipo Adali oti akhonza kufa.

Zokambirana

  • Kodi tikudziwa bwanji kuti kubadwa kwa Yesu kudali chochitika chofunika kwambiri?

  • Kodi Yesu adalandira mphamvu zotani kwa Atate ake?

  • Kodi Yesu adamva zinthu ziti chifukwa chakuti adali ndi mayi wapadziko lapansi?

Image
Yesu wazaka khumi ndi ziwiri mu Kachisi, zolembedwa ndi Carl Heinrich Bloch

Mpulumutsi, Yesu Khristu, adabadwira m’khola. Yesu ali mnyamata adaphunzitsa anthu ophunzira m’kachisi.

Yesu Adadza Kudzatiphunzitsa Uthenga Wake Wabwino

Yesu Adali Wopanda Tchimo

Yesu adalibe tchimo. Adachita zonse zimene Atate athu Akumwamba ankafuna kuti achite. Yesu adakula mofanana ndi mmene ana ena amakulira. Pamene adali kukula, adapeza nzeru. Iye adali ndi mphamvu ya Atate athu Akumwamba.

Pamene Yesu adali ndi dzaka 12, adadziŵa kuti adatumidwa kukachita zimene Atate athu Akumwamba adafuna kuti achite. Iye ankadziwa kuti ali ndi ntchito yapadera yoti agwire padziko lapansi.

Tsiku lina adapita ku Yerusalemu ndi Mariya ndi Yosefe. Pamene Mariya ndi Yosefe adali kubwelera kwawo, adaona kuti Yesu palibe. Iwo adabwelera ku Yerusalemu kuti akamuyang’ane. Patapita masiku atatu, iwo adamupeza mukachisi, akulankhula ndi anzeru ndi kuyankha mafunso awo. Aliyense amene adamumva adadabwa kuti amadziwa zambiri ndipo ankatha kuyankha mafunso awo. Yosefe ndi Mariya adasangalala kwambiri atamupeza, koma sadasangalale chifukwa choti sadakhale nawo limodzi. Yesu adawauza kuti chinali chifukwa chakuti adayenera kuchita ntchito ya Atate ake Akumwamba.

Yesu Adabatizidwa*

Yesu ali ndi dzaka 30, adapita kwa Yohane M’batizi kuti abatizidwe. Yohane adaganiza kuti sayenera kubatiza Yesu, chifukwa Yesu sadachimwepo. Koma Yesu adauza Yohane kuti amubatize. Yesu ankafuna kumvera malamulo onse a Atate athu Akumwamba. Yohane adabatiza Yesu, namuika kwathunthu pansi pa madzi ndi kumutulutsanso. Yesu atabatizidwa, Atate athu Akumwamba adalankhula kuchokera kumwamba kuti Yesu ndi Mwana wawo komanso kuti Atate athu Akumwamba ankasangalala naye kwambiri. Mzimu Woyera adadzanso kwa Yesu pamene adabatizidwa.

Satana Adayesa Yesu

Yesu atabatizidwa, adapita kuchipululu kukasala kudya ndi kupemphera. Yesu atasala kudya kwa masiku 40, Satana adabwera ndikumuyesa. Satana ankadziwa kuti ngati atachititsa kuti Yesu achite tchimo limodzi, Yesu sakanatha kuchita zimene adatumidwa. Ndiye dongosolo la Atate athu Akumwamba lidzalephera.

Yesu adakana mayesero onse a Satana. Pomaliza, adauza Satana kuti achoke. Satana atachoka, angelo adabwera kudzaona Yesu.

Yesu Adatiphunzitsa Kukonda Atate athu Akumwamba ndi Kukondana wina ndi mnzake

Atatsutsa Satana, Yesu adayamba kuphunzitsa anthu. Chifukwa chimodzi chimene adadzera padziko lapansi ndichakuti adzatiphunzitse mmene tikuyenera kukhalira.

Yesu adaphunzitsa kuti tiyenera kukonda Atate athu Akumwamba ndi mtima wathu wonse, maganizo athu onse, ndi mphamvu zathu zonse. Adaphunzitsa kuti tikuyenera kukondanso anthu ena mmene timadzikondera tokha. Tiyeneranso kukhululukira ndi kutumikira anthu ena. Yesu adatisonyeza mmene tingachitire zimenezi. Iye adasonyeza chikondi chake kwa Atate athu Akumwamba pochita zonse zimene Atate athu Akumwamba adamupempha kuti achite.

Yesu Adakonda Anthu Onse

Yesu ankakonda aliyense. Iye adachiritsa odwala. Adapangitsa akhungu kupenya ndi olumala kuyenda. Iye adatenga ana aang’ono m’manja mwake ndi kuwadalitsa iwo.

Yesu adasonyeza chikondi kwa anthu amene adachimwa. Adawaphunzitsa kuti azimvera chisoni machimo awo komanso kuti asamachimwenso. Yesu ankakonda ngakhale amene adamupha. Iye adawapemphelera iwo kwa Atate athu Akumwamba. Yesu adaphunzitsa kuti tiyenera kukondana monga mmene iye adatikondera.

Zokambirana

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene tingachite kuti tisonyeze kuti timawakonda Atate athu Akumwamba?

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene tingachite kuti tisonyeze kuti timawakonda?

Yesu Adakhazikitsa Mpingo

Yesu ankafuna kuti anthu onse adziwe njira yobwelera kwa Atate athu Akumwamba. Njira yake imatchedwa Uthenga Wabwino. Yesu adakonza mpingo kuti anthu onse aphunzire uthenga wabwino.

Yesu adasankha amuna khumi ndi awiri otchedwa Atumwi kuti azitsogolera mpingo. Adzaphunzitsa anthu uthenga wabwino atabwelera kumwamba. Yesu adapatsa atumwi khumi ndi awiri mphamvu kuti amuyimilire Iye. Adatha kuphunzitsa uthenga wabwino kwa anthu onse ndi kuwabatiza. Iwo akadatha kusankha ena kuti athandize kuphunzitsa uthenga wabwino ndi kuchita zonse zimene Iye ankafuna kuti zichitidwe.

Zokambirana

  • Ndichifukwa chiyani Yesu adasankha Atumwi khumi ndi awiri?

Tikamaphunzira za Yesu, timadziwa kuti Iye ndi Munthu Wamkulu

Yesu adathandiza aliyense wa ife mukutisonyeza mmene tingakhalire ndi moyo. Tikaphunzira kukhala ngati iye, timaphunzira kuchita zinthu zimene zimatipatsa chimwemwe. Titha kuphunziranso zinthu zimene zingatithandize kubwelera kumwamba kukakhala ndi Atate athu Akumwamba.

Tikadziwa kuti Yesu amatikonda, timakhala ndi mtendere. Timakhala otetezeka komanso opanda mantha. Tikudziwa kuti tikhonza kudalira Iye kuti akhale mtsogoleri wathu. Timadziwa kuti amamvetsa mavuto athu. Ziphunzitso zake zimatithandiza kuthetsa mavuto athu. Tikamvetsetsa zonse zimene Yesu watichitira, chikondi chathu pa Iye chimakula. Chikondi chathu pa Iye chimatipangitsa kufuna kumumvera. Timayembekezera mwachidwi nthawi imene tidzakhala ndi Iye.

Zokambirana

  • Kodi kuphunzira za Yesu kumatithandiza bwanji?

  • Kodi mumamva bwanji mukamaphunzira za Yesu?

Print