Zofunikira Zoyambirira
Mutu 20: Dongosolo la Unsembe


Image
Akuluakulu Olamulira kumsonkhano waukulu

Adindo oyang’anira ansembe a Mpingo ndi Atsogoleri Woyamba ndi Koramu ya Atumwi Khumi ndi Awiri. Palinso amuna ndi akazi ena ambiri amene amathandiza kutsogolera ntchito ya Mpingo.

Mutu 20

Dongosolo la Unsembe

Kodi munthu angapeze bwanji ulamuliro wochita ntchito ya Atate athu Akumwamba?

Pamene Munthu Ali ndi Unsembe, Akhonza Kuchita Zinthu M’malo mwa Atate athu Akumwamba

Unsembe ndi ulamuliro umene Atate athu Akumwamba amapereka kwa azibambo ndi anyamata oyenera kuchita nthito Yake padziko lapansi. Adapereka ulamuliro umenewu kwa Yesu. Yesu wapereka ulamuliro umenewu kwa anthu padziko lapansi. Azibambo ndi anyamata amene ali ndi unsembe amaimira Atate athu Akumwamba ndi Yesu. Amakhonza kuchita zinthu zomwe azibambo ndi anyamata ena sangachite. Atha kukhala mamishonale ndi kuphunzitsa uthenga woona wa Yesu Khristu. Iwo akhonza kudalitsa odwala. Akhonza kuchita ntchito zopatulika mu Mpingo.

Yesu watiuza njira yomwe munthu angapereke unsembe kwa mzibambo kapena mnyamata. Mzibambo amene ali ndi unsembe amaika manja ake pa mutu pa mzibambo kapena mnyamata. Kenako amapereka unsembe kwa iye m’dzina la Yesu Khristu ndi ulamuliro waunsembe umene alinawo.

Mzibambo yekhayo kapena mnyamata amene amamvera malamulo a Yesu angalandire unsembe. Yesu adzalora abambo ndi anyamata kugwira ntchito yake pokhapokha ngati amvera malamulo ake.

Palibe munthu wamkulu padziko lapansi kuposa mzibambo kapena mnyamata amene amagwiritsa ntchito unsembe m’njira yoyenera.

Zokambirana

  • Kodi unsembe ndi chiyani?

  • Ndindani angalandire unsembe?

Unsembe Wagawidwa Magawo Awiri

Magawo awiri a unsembe ndi Unsembe wa Aroni ndi Unsembe wa Melkizedeki. Unsembe wa Aroni nthawi zina umatchedwa unsembe wochepera. Unsembe wa Melkizedeki nthawi zina umatchedwa unsembe waukulu.

Unsembe wa Aroni

Unsembe wa Aroni umatchedwa Aroni, m’bale wake wa Mose, mneneri. Aroni adali mtsogoleri m’nthawi ya Mose.

Membala wa mwamuna woyenelera wa Mpingo akhonza kulandira Unsembe wa Aaroni kuyambira mu Januwale chaka chomwe akufika zaka 12 zakubadwa. Azibambo ndi anyamata amene ali ndi Unsembe wa Aroni akhonza kuphunzitsa anthu. Ena amene ali ndi Unsembe wa Aroni akhonza kubatiza anthu. Iwo amathandiza anthu kukumbukira Yesu. Iwo angathandize anthu m’njira zambiri.

Unsembe wa Melkizedeki

Unsembe wa Melkizedeki umatchedwa dzina la munthu wotchedwa Melkizedeki. Melkizedeki adali munthu wolungama kwambiri amene adali ndi unsembe. Iye adali moyo munthawi ya Abrahamu. Iye adali wankulu wa nsembe. Unsembe usadatchulidwe dzina lake, unkatchedwa Unsembe Woyera mu dongosolo la Mwana wa Mulungu. Dzina la unsembe lidasinthidwa kukhala Melkizedeki kuti anthu asagwiritse ntchito dzina la Mulungu mopyoleza.

Membala wamwamuna woyenelera wa Mpingo ayenera kukhala osachepera dzaka 18 kuti akhale ndi Unsembe wa Melkizedeki. Abambo amene ali ndi Unsembe wa Melkizedeki ali ndi mphamvu yopereka madalitso kwa ena. Yesu amaulula kwa iwo zinthu zimene afunikira kuzidziŵa ndi kunena popereka madalitso ameneŵa.

Zokambirana

  • Kodi unsembe uwiri mu mpingo ndi uti?

Unsembe Uliwonse Uli Ndi Maudindo Ndi Ulamuliro Wosiyana

Munthu akalandira unsembe, amadzodzedwa kukhala ndi udindo mu unsembe. Unsembe wa Aroni ndi Unsembe wa Melkizedeki onsewa ali ndi maudindo angapo. Uliwonse uli ndi ntchito zapadera.

Azibambo ndi anyamata omwe ali ndi Unsembe wa Aroni ndipo adzodzedwa mu udindo wa wansembe mu unsembe uwu ali ndi mphamvu yochita zinthu izi:

  1. Kuphunzitsa Uthenga Wabwino.

  2. Kubatiza.

  3. Kukonzekera, kudalitsa, ndikuperekera mgonero.*

  4. Kuthandiza iwo omwe ali ndi Unsembe wa Melkizedeki poyendera ndi kuthandiza mamembala a Mpingo.

  5. Kupeleka Unsembe wa Aroni kwa ena.

Azibambo omwe ali ndi Unsembe wa Melkizedeki ali ndi ulamuliro wochita zinthu izi:

  1. Kutsogolera Mpingo.

  2. Kulalikira uthenga wabwino.

  3. Kupereka mphatso ya Mzimu Woyera.

  4. Kupereka madalitso apadera.

  5. Kupereka maina kwa ana ndi mdalitso.

  6. Kuchilitsa odwala.

  7. Kupereka unsembe kwa ena.

  8. Kuchita zinthu zonse zimene azibambo ndi anyamata amene ali ndi Unsembe wa Aroni angachite.

Zokambirana

  • Kodi iwo amene ali ndi Unsembe wa Melkizedeki ali ndi ulamuliro wochita chiyani?

  • Kodi amene ali ndi Unsembe wa Aroni ali ndi ulamuliro wochita chiyani?

Maudindo a Unsembe wa Aroni ndi Ntchito Zawo

Maudindo a Unsembe wa Aroni ndi dikoni, mphunzitsi, wansembe, ndi bishopu.

Dikoni

Membala wa mwamuna wa Mpingo woyenelera akhonza kulandira unsembe ndi kudzodzedwa kukhala dikoni kuyambira mu Januwale chaka chomwe akukwanitsa zaka 12. Ayenera kumvera malamulo a Yesu ndi malamulo a mpingo.

Izi ndi ntchito za dikoni:

  1. Kuperekera m’gonero.

  2. Kuthandizira atsogoleri ake.

  3. Kuthandizira aphunzitsi a Unsembe wa Aroni kuti azichita ntchito zawo akatumidwa.

Dikoni sangapereke unsembe kwa munthu wina. Iye sangabatize aliyense. Sangadalitse m’gonero.

Mphunzitsi

Membala wa Mpingo wamwamuna woyenelera akhonza kulandira unsembe ndi kudzodzedwa kukhala mphunzitsi kuyambira mu Januwale chaka chomwe akukwanitsa zaka 14. Ayenera kumvera malamulo a Yesu ndi malamulo a mpingo.

Izi ndi ntchito za mphunzitsi:

  1. Kuyang’anira mamembala a Mpingo, kuwathandiza kukwaniritsa zosowa zawo zakuthupi ndiza uzimu.

  2. Kuwathandiza mamembala kumvera malamulo a Yesu.

  3. Kuwathandiza iwo omwe ali ndi Unsembe wa Melkizedeki potumikira nawo ku mabanja ndi kuwathandiza kutumikira ndi kuphunzitsa uthenga wabwino kwa mabanjawa.

  4. Kukonza m’gonero.

  5. Pakafunika kutero, kuchita zonse zimene dikoni amachita.

Mphunzitsi sangapereke unsembe kwa munthu wina. Sangathenso kubatiza aliyense. Siangadalitse m’gonero.

Wansembe

Membalawa Mpingo wa mwamuna woyenelera akhonza kulandira unsembe ndi kudzodzedwa kukhala wansembe kuyambira mu Januwale chaka chomwe akukwanitsa zaka 16. Ayenera kumvera malamulo a Yesu ndi malamulo a mpingo.

Izi ndi ntchito za wansembe:

  1. Kuphunzitsa Uthenga Wabwino.

  2. Kulimbikitsa mamembala kumvera malamulo a Yesu.

  3. Kubatiza.

  4. Kudalitsa m’gonero.

  5. Kudzodza ma dikoni ena, aphunzitsi, ndi ansembe.

  6. Kutsogolera misonkhano pamene palibe aliyense mu msonkhanomo amene ali ndi Unsembe wa Melkizedeki.

Wansembe akhonza kuchita zonse zimene mphunzitsi ndi dikoni amachita. Iye sangakhonze kudzodza aliyense ku udindo wa bishopu kapena ku maudindo aliwonse a Unsembe wa Melkizedeki.

Bishopu

Bishopu ndi mtsogoleri wa wodi.

Izi ndi ntchito za bishopu (pulezidenti wanthambi ali ndi udindo wofanana mu nthambi):

  1. Kutsogolera wodi.

  2. Kukhala ngati pulezidenti wa kolamu la ansembe.

  3. Kufunsa mafunso a keyeneredwe kwa mamembala a wodi.

  4. Kulangiza mamembala a wodi.

  5. Kuthandiza mamembala a wodi kuti akhale odzidalira ndi kukonzekera zinthu zochitika zadzidzidzi.

  6. Kuyang’anira zam’mabuku ndi zachuma ndi kagwiritsidwe ntchito ndi chitetezo cha nyumba yochitira misonkhano.

Pulezidenti wa Mpingo amatsogolera apulezidenti a siteki kuti adzodze azibambo kuti akhale mabishopu.

Zokambirana

  • Kodi ntchito za dikoni, mphunzitsi, wansembe, ndi bishopu ndi ziti?

Maudindo a Unsembe wa Melkizedeki ndi Ntchito Zawo

Maudindo a Unsembe wa Melkizedeki ndi mkulu, wankulu wa nsembe, kholo, a Makumi asanu ndi awiri, ndi Mtumwi. Uliyonse mwa maudindo awa uli ndi ntchito zake.

Mkulu

  1. Kubatiza.

  2. Kupeleka mphatso ya Mzimu Woyera.

  3. Kuchititsa misonkhano.

  4. Kutsogolera misonkhano ngati palibe wamkulu wa nsembe.

  5. Kulalikira uthenga wabwino.

  6. Kadalitsa odwala.

  7. Kudalitsa makanda.

  8. Kupereka unsembe kwa ena ndi kuwadzodza ku maudindo a akulu, ansembe, aphunzitsi, kapena dikoni.

  9. Pakafuni kakutero, kuchita ntchito zonse za wansembe, mphunzitsi, kapena dikoni.

Wankulu wa nsembe

Ntchito yaikulu ya wankulu wa nsembe ndi kukhala mtsogoleri wa anthu mu mpingo ndi kuyang’anira zinthu zauzimu. Mkulu wa ansembe akhonza kugwira ntchito iliyonse ya mkulu, wansembe, mphunzitsi, kapena dikoni ngati pakufunika kutero.

Kholo

Kholo ndi wamkulu wa nsembe amene amapereka madalitso apadera kwa mamembala a mpingo. Madalitso amenewa amatchedwa madalitso a makolo. Madalitso a makolo amathandiza mamembala kumvetsetsa zinthu zimene Yesu amafuna kuti iwo achite.

Makumi asanu ndi awiri

Makumi asanu ndi awiri ndi mboni zapadera za Yesu Khristu kudziko lapansi. Amagwira ntchito motsogozedwa ndi Atumwi pomanga Mpingo.

Mtumwi

Mtumwi ndi mboni yapadera ya Yesu Khristu kudziko lonse lapansi. Atumwi amatsogolera zochitika za mpingo pa dziko lonse lapansi. Mtumwi aliyense ali ndi ulamuliro wonse wa unsembe. Koma Pulezidenti wa Mpingo yekha, yemwenso ndi Mtumwi, angagwiritse ntchito mphamvu zonse za unsembe. Atumwi ena amagwiritsa ntchito ulamuliro wawo monga momwe Pulezidenti wa Mpingo amawauzira.

Mafungulo a Unsembe Ndi Ulamuliro Wotsogolera Kagwiritsidwe Ntchito ka Unsembe

Unsembe ndi ulamuliro wochita zinthu mu dzina la Yesu ndi kutitsogolera ife kubwelera kwa Atate athu Akumwamba. Kugwiritsiridwa ntchito kwa ulamuliro wa unsembe kumalamulidwa ndi iwo amene ali ndi mfungulo zake. Mfungulo izi ndi ufulu wotsogolera ndi kutsogoza mpingo muulamuliro wake. Ambuye Yesu Khristu ali ndi mfungulo zonse za unsembe. Iye wapereka kwa Atumwi Ake mfungulo zomwe ziri zofunikira kuti azilamulira mpingo wake. Ndi Mtumwi wamkulu yekha, Pulezidenti wa Mpingo, angagwiritse ntchito (kapena kuloleza munthu wina kuti agwiritse ntchito) mfungulozi pakulamulira mpingo wonse. Pulezidenti wa Mpingo amavomereza apulezidenti a makachisi, mamishoni, masiteki, ndi zigawo; mabishopu ndi apulezidenti a nthambi; ndi apulezidenti a koramu kuti atenge mfungulo za unsembe omwe amafunikira kuti atsogolere.

Ansembe ali ndi ulamuliro wochita zinthu zina popanda chilorezo chapadera. Mwachitsanzo, azibambo amene ali ndi Unsembe wa Melkizedeki akhonza kudalitsa odwala ndipo amuna okwatira kapena bambo akhonza kudalitsa mabanja awo. Komabe, zinthu zina zimafuna chilorezo kuchokera kwa omwe ali ndi mfungulo zofunikira. Mwachitsanzo, wansembe ali ndi udindo wobatiza. Koma siangabatize aliyense mpaka bishopu kapena pulezidenti wa nthambi amulore kutero. Bishopu kapena Pulezidenti wa nthambi ali ndi mfungulo za Unsembe wa Aroni mu gawo limenelo la Mpingo.

Zokambirana

  • Kodi mfungulo za unsembe ndi chiyani?

Okhala ndi Unsembe Amakhazikitsidwa M’makolamu

Azibambo ndi anyamata amene ali ndi udindo wofanana wa unsembe amaikidwa m’magulu. Magulu wa amatchedwa makolamu. Mu Unsembe wa Aroni muli makolamu a madikoni, makolamu a aphunzitsi, ndi makolamu a ansembe. Mu Unsembe wa Melkizedeki muli makolamu a akulu ndi makolamu a akulu ansembe.

Pamene mzibambo kapena mnyamata akadzodzedwa mu udindo wa unsembe, amakhala membala wa kolamu ya ansembe yopangidwa ndi anthu amene ali ndi udindo womwewo. Iye amakhalabe mu kolamuyi kufikira atadzodzedwe udindo wina. Atsogoleri akolamu amaphunzitsa ndi kuthandiza membala aliyense wa kolamu.

Kolamu ya Madikoni

Kolamu ya madikoni litha kukhala ndi madikoni okwana 12. Ngati mu wodi muli madikoni oposera 12, kolamu ina ya madikoni ikhonza kupangidwa. Kolamu ya madikoni ili ndi pulezidenti ndi alangizi awiri.

Kolamu ya aphunzitsi

Kolamu ya aphunzitsi itha kukhala ndi aphunzitsi 24. Ngati pali aphunzitsi oposera 24 m’ma wodi, kolamu ina ya aphunzitsi itha kupangidwa. Kolamu ya aphunzitsi ili ndi pulezidenti ndi alangizi awiri.

Kolamu ya Ansembe

Kolamu ya ansembe itha kukhala ndi ansembe 48. Ngati pali ansembe oposera 48 mu wodi, kolamu ina ya ansembe ikhonza kupangidwa. Pulezidenti wa kolamu ya ansembe ndi bishopu kapena Pulezidenti wa nthambi. Amasankha ansembe awiri kuchokera pa kolamu kuti akhale omuthandizira.

Kolamu ya Akulu

Kolamu ya akulu imatha kukhala ndi chiŵerengero cha akulu kufikira pa 96, ndipo imakhala ndi akulu onse okhala mu wodi. Ngati pali akulu oposera 96, kolamu ina ya akulu itha kupangidwa. Azibambo amene sanalandirebe Unsembe wa Melkizedeki akhonza kukumana ndi akulu kuti aphunzire, kucheza nawo, ndi kutumidwa ntchito.

Pulezidenti ndi alangizi awiri amatsogolera kolamu ya akulu.

Kolamu ya Akulu Ansembe

Kolamu ya akulu ansembe imakhala ndi akulu ansembe omwe amatumikira mu maitanidwe ena a utsogoleri mu siteki. Pulezidenti wa siteki ndi alangizi ake awiri amatsogolera kolamu ya akulu ansembe.

Zokambirana

  • Kodi kolamu ndi chiyani?

  • Ndi mamembala angati omwe amapanga kolamu ya madikoni, aphunzitsi, ansembe, akulu, akulu ansembe?

  • Kodi mamembala a kolamu angathandizane bwanji?

Print