Zofunikira Zoyambirira
Mutu 30: Udindo Wathu Wothandiza Achibale


Mutu 30

Udindo Wathu Wothandiza Achibale

Kodi aliyense m’banja angathandize bwanji kuti banja likhale losangalala?

Aliyense M’banja Ndi Wofunika

Kukhala ndi banja lachikondi ndi losangalala kumafuna ntchito. Atate athu Akumwamba apereka udindo kwa munthu aliyense m’banja. Aliyense m’banjamo akuyenera kukhala wothandiza, wansangala, ndi wokoma mtima kwa ena. Tikamapemphera, kugwira ntchito, kuimba komanso kusewera limodzi, mabanja athu amakhala osangalala.

Kukonda anthu ena a m’banja lathu kumatithandiza kuchita zinthu zimene Atate athu Akumwamba amafuna. Tikamakonda banja lathu, tikuyenera kuchita zonse zomwe tingathe kuti tiwathandize. Ngakhale zinthu zovuta kuchita zimakhala zosavuta ngati tizichita mwachikondi. Pamafunika nthawi ndi ntchito kuti mukhale m’bale wabwino wabanja.

Zokambirana

  • Kodi aliyense m’banja angathandize bwanji kuti panyumba pakhale malo osangalala?

  • Nchifukwa chiyani aliyense m’banja ali wofunika?

Atate Athu Akumwamba Adapatsa Makolo Udindo Wapadera

Abambo ndi amayi akuyenera kugwilira ntchito limodzi kusamalira ana awo ndi kuwapatsa zinthu zofunika. Akuyeneranso kuphunzitsa ana awo uthenga wabwino. Akuyenera kuwaphunzitsa kupemphera ndi kumvera malamulo a Atate athu Akumwamba.

Abambo ndi amayi akuyenera kumvetsetsa kuti nthawi zina ana amatha kusankha zolakwika ngakhale ataphunzitsidwa zoyenera.

Ana akalakwa, makolo sakuyenera kuleka kuwathandiza. Makolo akuyenera kupitiliza kukonda ndi kuphunzitsa ana awo. Akuyeneranso kukhala zitsanzo zabwino kwa iwo ndi kuwasalira kudya ndi kuwapemphelera.

Makolo akuyenera kupatsa mabanja awo zinthu zina:

  1. Akuyenera kukonda ana awo ndi kuphunzitsa ana awo kukonda ena.

  2. Akuyenera kuphunzitsa ana awo uthenga wabwino.

  3. Akuyenera kuphunzitsa anthu a m’banjamo mmene angapemphelere.

  4. Akuyenera kuphunzitsa ana kupereka chakhumi ndi zopereka popereka chakhumi ndi zopereka zawo.

  5. Akuyenera kuphunzitsa ana awo kugwira ntchito.

  6. Akuyenera kupereka nyumba yaukhondo, zovala, ndi chakudya.

  7. Akuyenera kutsimikizira kuti ana awo akuphunzira kuŵerenga, kulemba, ndi masamu oyambilira powatumiza kusukulu kapena kuwaphunzitsa kunyumba.

  8. Akuyenera kuchita zonse zomwe angathe kuti ana awo aphunzire ntchito inayake n’kukhala okonzeka kupeza ndalama zokwanira zogulira zinthu zofunika pamoyo.

  9. Akuyenera kusonyeza ana awo mmene angagwiritsire ntchito ndalama mwanzeru ndi kusunga ndalama zoti adzagwiritse ntchito m’tsogolo.

  10. Akuyenera kuthandiza ana awo kukulitsa luso lawo ndi kuthekera kwawo. Zimenezi zingakhale monga luso lophunzitsa, kupanga nyimbo, kuimba, kukonza zinthu, kapenanso kukhala omvetsetsa ena.

Makolo akuyenera kukhala ofunitsitsa kuthandiza ana awo. Atate athu Akumwamba adanena kuti makolo akuyenera kuonetsetsa kuti ana awo akuchitirana zinthu zabwino komanso kuti ali ndi chakudya ndi zovala.

Makolo akuyenera kukonzekera kuti adzapereka zinthu zimenezi ngakhale atadwala, atachotsedwa ntchito, kapena akakhala ndi mavuto ena. Atha kuchita zimenezi mwa kusunga ndalama ndi kusunga chakudya, zovala, ndi mafuta owonjezera m’madera amene amaloledwa kuchita zimenezi.

Zokambirana

  • Kodi makolo angachite chiyani kuti asamalire mabanja awo?

  • Kodi makolo angachite chiyani kuti akonzekere nthawi imene atha kukumana ndi mavuto?

Image
banja kuphika pamodzi

Atate Ali Ndi Udindo Wapadera

Bambo ndi mtsogoleri wa unsembe wa banja. Bambo akuyenera kutsogolera banja lake mwachikondi komanso mokoma mtima. Akuyenera kusonyeza banja lake mmene angakhalire m’malamulo a Atate athu Akumwamba powatsatira iye mwini. Akuyeneranso kuphunzitsa banja lake uthenga wabwino. Azisonkhanitsa banja lonse kuti lichite pemphero la banja m’maŵa ndi madzulo. Mkazi wake akuyenera kumuthandiza kuchita zimenezi.

Bambo akuyenera kugwiritsa ntchito unsembe wake kudalitsa anthu a m’banja lake. Iye atha kupatsa ana ake aang’ono mdalitso ndi dzina. Iye akhoza kuwabatiza ali ndi dzaka zisanu ndi zitatu. Iye akhonza kudzodza ana ake aamuna ku unsembe ndi kupereka kwa ana ake madalitso apadera pamene akuwafuna. Iye akhoza kuwadalitsa akadwala.

Bambo akuyenera kukhala ndi nthawi yocheza ndi mwana aliyense payekha. Akuyenera kukambirana nawo ndi kuphunzira kumvetsa zosowa zawo ndi nkhawa zawo. Akuyenera kuwalimbikitsa ndi kuwauza kuti amawakonda. Akuyenera kuwauza kuti akhonza kubwera kwa iye kuti awathandize pa vuto lirilonse limene angakhale nalo.

Zokambirana

  • Kodi udindo wa abambo ndi wotani?

  • Kodi angagwiritse ntchito bwanji unsembe omwe ali nawo pothandiza banja lake?

Mayi Ali ndi Udindo Wapadera

Udindo waukulu wa mayi ndi kubereka ana ndi kuwasamalira ndi kuwaphunzitsa. Kupereka matupi amnofu ndi mafupa kwa Atate athu Akumwamba ana auzimu ndi ntchito yopatulika. Mayi akamachita zimenezi amakhala mnzake wa Atate athu Akumwamba. Kubereka ana ndi imodzi mwa madalitso aakulu kwambiri.

Mayi akuyenera kukhala wachikondi. Akuyenera kuthandiza kuphunzitsa mwana aliyense uthenga wabwino. Akuyenera kuthandiza ndi kugwira ntchito ndi mwana aliyense. Mayi akuyenera kupangitsa mwana wake aliyense kumva kuti ndi wofunika komanso akuyenera kuwathandiza kumvetsetsa zinthu zomwe zimamuzungulira. Akuyenera kugwira ntchito limodzi ndi mwamuna wake kuchita zinthu zimenezi.

Buku la Mormoni limatiuza za gulu la anyamata olungama amene adamvera ziphunzitso za amayi awo. Amayi a anyamatawa adawaphunzitsa kukhala oona mtima, olimba mtima, ndi olungama. Amayi awo adawaphunzitsanso kuti Atate athu Akumwamba adzawateteza ngati ali ndi chikhulupiliro mwa Yesu. Anyamatawa adayenera kukhala asilikali kuti ateteze dziko lawo. Chifukwa chakuti achinyamatawa ankatsatira zimene amayi awo ankaphunzitsa komanso adali ndi chikhulupiliro, adalimba mtima kuchita ntchito yawo ngakhale pa nthawi imene zinthu zidali zoopsa. Mayi aliyense akhonza kukhudza kwambiri moyo wa ana ake.

Zokambirana

  • Kodi udindo wa amayi ndi wotani?

  • Ndi chifukwa chiyani umayi umatchedwa mgwirizano ndi Atate athu Akumwamba?

Pamene Pali Kholo Limodzi Lokha

Nthawi zina bambo kapena mayi amasiyidwa yekha kuti alere banja ndipo akuyenera kugwira ntchito ya bambo ndi mayi. Atate athu Akumwamba amadziwa kuti kuchita zimenezi n’kovuta. Ngati munthu woteroyo, amene timamutchula kuti kholo limodzi, apempha Atate athu Akumwamba, Atate athu Akumwamba amatha kumuthandiza munthuyo kusamalira banja lake.

Kholo limodzi likhoza kuthandizidwa ndi abale otumikira* ndi alongo otumikira* (mamembala a Mpingo amene apatsidwa ntchito yoyang’anira mamembala ena a Mpingo).

Zokambirana

  • Ndi ndani angathandize makolo olera okha ana?

Ana Amakhalanso ndi Udindo Wapadera

Ana akuyenera kuthandiza makolo awo kupanga nyumba yawo kukhala malo osangalatsa. Ana akuyenera kuthandiza makolo awo kukonza m’nyumba ndi malo ozungulira. Angathandizenso kuphika chakudya cha banjalo, kutsuka mbale, ndi kuchapa zovala. Angathandizenso abale ndi alongo awo aang’ono.

Ana akuyenera kuyesetsa kwambiri kuphunzira zimene makolo awo amawaphunzitsa. Akuyenera kuphunzira kugwira ntchito molimbika ndi kugwira ntchito bwino. Akuyenera kuphunzira kugwira ntchito zomwe apatsidwa.

Ana akuyenera kumvera malamulo a Yesu. Akuyenera kuthandiza achibale ena. Atate athu Akumwamba sasangalala ana akamakangana. Atate athu Akumwamba adauza ana kuti azimvera ndi kulemekeza makolo awo.

Ana akuyenera kukonda makolo awo. Akuyenera kuwamvera ndi kuwalemekeza. Ana akuyeneranso kuwasamalira akadwala kapena akakalamba ndipo sangathenso kudzisamalira.

Zokambirana

  • Kodi Atate athu Akumwamba amafuna kuti ana adzichita chiyani?

  • Kodi ana akuyenera kuwachitira chiyani makolo awo akakalamba?

  • Kodi ana akuyenera kuchita chiyani kuti adzimvera komanso kulemekeza makolo awo?

Kufunika Kolimbikitsa Banja

M’dzikoli masiku ano, anthu ambiri oipa akuyesetsa kusintha maganizo athu pa nkhani ya banja. Makanema, mafilimu, ndi magazini amawonetsa malingaliro achilendo ndi olakwika okhudza amuna ndi akazi komanso momwe amachitirana wina ndi mnzake. Malingaliro oipa amaphunzitsidwa kudzera m’mapulogalamu amene amapangidwa kukhala oseketsa ndi osangalatsa. Kusadzisunga kumawonetsedwa ngati kosangalatsa komanso kofunikira. Ana akujambulidwa akusonyeza kusalemekeza kwambiri makolo awo. Mabanja abwino amasekedwa. Nthaŵi zina ana athu samaona m’mafilimu kapena pawailesi yakanema mmene moyo wabwino wapanyumba uliri kwenikweni.

Makolo akuyenera kuyesetsa kuteteza ana awo kuti asaonere mafilimu ndi mapulogalamu a pa kanema ngati amenewa. Akuyenera kuphunzitsa ana awo chifukwa chimene sakuyenera kuonera mapulogalamu kapena mafilimu oipa. Koposa zonse, makolo akuyenera kusonyeza chitsanzo chabwino nthaŵi zonse m’nyumba zawo. Ngati ana amaona chitsanzo chabwino tsiku ndi tsiku m’nyumba, adzakhala ana abwino, ndipo pambuyo pake, adzakhala makolo abwino. Ngati aona makolo awo akusonyezana chikondi, iwo angafune kukhala kholo loterolo.

Zokambirana

  • Nchifukwa chiyani tikuyenera kusankha mosamala zinthu zimene ana athu amaloledwa kuziona pa kanema kapena m’mafilimu?

Atate athu Akumwamba Amafuna Kuti Tizithandizana

Aliyense m’banjamo akuyenera kukondana ndi kuthandizana. Timaphunzira kuthandiza ena poyamba kuthandiza makolo athu ndi abale ndi alongo athu. Tikuyeneranso kuthandiza achibale athu akafuna thandizo. Sitikuyenera kupempha ena kuti atithandize ngati tili okuti titha kudzipezera tokha. Ngati titero, Atate athu Akumwamba sakondwera nafe.

Yesu ankakonda anthu onse ndipo adabwera padziko lapansi kudzatithandiza. Iye adatiphunzitsa kukonda ndi kuthandiza aliyense. Tikamakonda anthu ngati mmene Yesu ankachitira, tidzayesetsa kuwathandiza.

Ena a ife timapempha Atate athu Akumwamba kuti athandize amene akufunika thandizo, komano sitichita chirichonse kuti tiwathandize. Izi sizolondola. Tikuyenera kukumbukira kuti Atate athu Akumwamba amathandiza ena kudzera mwa ife. Choyamba tikuyenera kupemphelera amene akufunika thandizo kenako n’kuwathandiza m’njira iliyonse imene tingathe.

Tonsefe timafunikira thandizo kuchokera kwa anthu ena. Pamene tili ana, makolo athu amatidyetsa, kutiveka, ndi kutisamalira. Tikamakula, anthu ena amatiphunzitsa zinthu zimene tikuyenera kudziwa komanso kuchita. Ambiri a ife timafunikira thandizo la ena tikadwala.

Tikamathandiza anthu ena, timadalitsidwa. Kukonda kwathu kumakula, timakhala osadzikonda, ndipo mavuto athu amaoneka ochepa kwambiri. Atate athu Akumwamba adanena kuti amene akufuna kukhala naye limodzi akuyenera kukonda ndi kuthandiza ana ake onse.

Zokambirana

  • Ndi chifukwa chiyani Atate athu Akumwamba amafuna kuti tizithandiza ena?

  • Ndi ndani amapindula ndi thandizo lathu?

Print