Zofunikira Zoyambirira
Mutu 29: Mabanja Ndi Ofunika


Image
banja kutsogolo kwa kachisi

Mabanja akhonza kukhala pamodzi kwamuyaya.

Mutu 29

Mabanja Ndi Ofunika

Nchifukwa chiyani Atate athu Akumwamba adakonza zoti tidzakhale ngati mabanja padziko lapansi pano?

Atate athu Akumwamba Adatikonzera Kuti Tizikhala Monga Mabanja

Banja lathu pano padziko lapansi liri ngati banja lathu lakumwamba. Tisadabwere padziko lapansi, tidali m’banja lakumwamba. Tidali ana auzimu a Mulungu, amene ali Atate athu Akumwamba. Iwo amatikonda ndipo amatisamalira. Iwo amatifunira zabwino ndipo amafuna kuti tibwelere kukakhala nawo tsiku lina.

Atate athu Akumwamba adaika pamodzi banja loyamba pamene adapereka Hava kwa Adamu mu ukwati. Adawauza kuti akhale ndi ana. Izi zidali choncho kuti ana auzimu a Atate athu Akumwamba alandire matupi amnofu ndi mafupa. Adawauza kuti azipatsa ana awo zinthu zimene ankafunikira. Adawauzanso kuti aziphunzitsa ana awo uthenga wabwino ndi kuwathandiza kuti alandire miyambo ya uthenga wabwino.

Atate athu Akumwamba atiika m’mabanja pa zifukwa zingapo.

Choyamba, kuchokera kwa makolo athu timalandira matupi a mnofu ndi mafupa. Timafunika matupi amnofu ndi mafupa kuti tiphunzire zinthu zimene tikuyenera kuchita kuti tikakhale ndi Atate athu Akumwamba kwamuyaya.

Chachiŵiri, mabanja akhoza kutipatsa zinthu zofunika pa dziko lapansili. Makolo akhoza kupereka chakudya, zovala, pogona, chikondi, ndi zinthu zina zofunika kwa ana awo. Pambuyo pake, ana amatha kusamalira makolo awo makolowo akakula kwambiri moti sangathe kudzisamalira okha.

Chachitatu, makolo akhoza kuphunzitsa ana awo uthenga wabwino wa Yesu Khristu. Iwo angawaphunzitse kumvera malamulo a Atate athu Akumwamba. Ndipo angatsimikizire kuti anawo alandira miyambo imene Yesu adanena kuti tikuyenera kulandira.

Zokambirana

  • Nchifukwa chiani Atate athu Akumwamba adatilinganiza kuti tibwele padziko lapansi monga mabanja?

  • Ndi banja liti lomwe lidali loyamba kubwera padziko lapansi?

  • Kodi Atate athu Akumwamba adakonza zotani kuti mabanja athu atichitire?

Atate athu Akumwamba Amafuna Kuti Anthu M’banja Adzikondana

Banja lathu padziko lapansi litha kukhala monga mmene banja lathu lakumwamba lidaliri kumwamba. Banja litha kumva chikondi chimene chingawapangitse kukhala ofunitsitsa kuthandizana ndi kuchita ndi kulankhula zinthu zabwino kwa wina ndi mnzake.

Mwamuna ndi mkazi m’banja akuyenera kukondana. Akuyenera kukhala okoma mtima ndi kuthandizana. Sakuyenera kunena kapena kuchita chirichonse chimene chingakhumudwitse winayo.

Makolo akuyenera kukonda ana awo. Akuyenera kuphunzitsa ana awo kukondana. Akuyenera kuwaphunzitsa kuthandizana ndi kusamalirana.

Ana akuyenera kukonda makolo awo. Akuyenera kulemekeza, kumvera, ndi kuthandiza makolo awo.

Zokambirana

  • Werengani Aefeso 4:29–32.

  • Kodi tingathandize bwanji achibale kuti azikondana?

  • Ndi chifukwa chiyani Atate athu Akumwamba amafuna kuti anthu a m’banja mwawo adzikondana?

Chinthu Chofunika Kwambiri Chomwe Tingachite Ndi Kugwira Ntchito Kuti Tikhale ndi Banja Lachimwemwe ndi Lolungama

Kugwira ntchito yolera banja lolungama ndi ntchito yofunika kwambiri imene tingachite. Ngakhale titachita bwino motani m’zinthu zina, ngati sitiphunzitsa banja lathu kukonda ndi kumvera Atate athu Akumwamba, ndiye kuti talephera pa ntchito yathu yofunika kwambiri. Nthawi zina, ana athu atha kusankha kusakonda ndi kusamvera Atate athu Akumwamba, koma tikuyenera kuchita zonse zomwe tingathe kuti tiziwaphunzitsa njira zawo. Ngati makolo achita zonse zomwe angathe kuti aphunzitse ana awo moyenera, Atate athu Akumwamba sadzawaimba mulandu chifukwa cha zolakwa za ana awo. Makolo amalephera pokhakokha pamene asiya kuyesa kukhala makolo abwino.

Mabanja athu atha kutipatsa chimwemwe chachikulu m’moyo. Timachita bwino kwambiri tikamagwira ntchito mwakhama kulera ana kuti akhale mamembala abwino a mpingo komanso kukhala nzika zabwino m’dziko limene akukhala.

Banja ndi gawo lofunika kwambiri la Mpingo. Atate athu Akumwamba adakonza Mpingo Wawo kuti athandize mabanja kuchita zonse zomwe akuyenera kuchita kuti abwelere kwa Iwo. Mpingo umafuna kuthandiza banja lirilonse kukhala pamodzi kwamuyaya.

Satana amadziwa kufunika kwa mabanja mu dongosolo la Atate athu Akumwamba. Amayesetsa kutichititsa kuchita zinthu zimene zingasokoneze mabanja athu.

Zokambirana

  • Kodi banja lanu ndi lofunika bwanji kwa inu?

Atate athu Akumwamba adatiuza Mmene Tingakhalire ndi Banja Labwino

Tonsefe timafuna kukhala ndi banja labwino komanso losangalala. Nazi zina mwa zinthu zomwe zingathandize banja:

  1. Banja likuyenera kupemphera pamodzi m’maŵa ndi usiku.

  2. Makolo akuyenera kupemphera pamodzi tsiku lirilonse.

  3. Makolo akuyenera kuphunzitsa ana uthenga wabwino.

  4. Banja likuyenera kuwerengera limodzi malemba tsiku lirilonse.

  5. Banja likuyenera kumapita kumisonkhano yampingo limodzi Lamlungu lirilonse.

  6. Banja likuyenera kusala limodzi kamodzi pamwezi anawo akakula mokwanira kuti atha kusala komanso kumvetsa cholinga cha kusala kudya.

  7. Banja likuyenera kusonkhana mlungu uliwonse ku msonkhano wa banjalo wotchedwa madzulo panyumba* kuti likambirane zinthu zabwino zimene banjalo lachita. Akuyeneranso kukambirana momwe angathetsere mavuto aliwonse omwe ali nawo. Pamsonkhanowu angathenso kuimba, kukhala ndi phunziro, kuphunzira ndime zina za m’Malemba, kuchita masewera, ndiponso kukhala ndi chakudya chapadera kapena chakumwa.

  8. Banja likuyenera kugwilira ntchito limodzi ndi kuŵerengera pamodzi.

  9. Achibale akuyenera kukhala okoma mtima ndi oleza mtima kwa wina ndi mnzake.

  10. Banja likuyenera kusunga mbiri ya zinthu zomwe amachita.

Ngati tikumbukira kupemphera tokha komanso monga banja, Atate athu Akumwamba adzakhala pafupi nafe. Iwo adzamva mapemphero athu ndi kuwayankha m’njira yotithandiza kwambiri.

Zokambirana

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene tingachite kuti tikhale ndi banja labwino?

Print