Malembo Oyera
Alima 22


Mutu 22

Aroni aphunzitsa atate a Lamoni zokhudzana ndi Chilengedwe, Kugwa kwa Adamu, ndi dongosolo la chiwombolo kudzera mwa Khristu—Mfumu ndi banja lake lonse atembenuka—Kugawanika kwa dziko pakati pa Anefi ndi Alamani kulongosoledwa. Mdzaka dza pafupifupi 90–77 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano, pamene Amoni adali kuphunzitsa motere anthu a Lamoni mosalekeza, tidzabwelera ku nkhani ya Aroni ndi abale ake; pakuti iye atachoka ku dziko la Midoni adatsogozedwa ndi Mzimu kupita ku dziko la Nefi, ngakhale kunyumba ya mfumu imene idali pa dziko lonse kupatula dziko la Ismaeli; ndipo iye adali atate ake a Lamoni.

2 Ndipo zidachitika kuti iye adapita kwa iye ku nyumba yachifumu, ndi abale ake ndipo adagwada pamaso pa mfumuyo, ndipo adati kwa iyo: Taonani, O mfumu, ife ndi abale ake a Amoni, amene inu mwamutulutsa kuchoka ku ndende.

3 Ndipo tsopano, O mfumu, ngati inu musunge miyoyo yathu, ife tidzakhala adzakazi anu. Ndipo mfumuyo idati kwa iwo: Dzukani, pakuti ndidzapereka kwa inu miyoyo yanu, ndipo sindidzalola kuti inu mukhale adzakazi anga; koma ndidzaumilira inu kuti munditumikire ine; pakuti ndakhala penapake osautsika m’maganizo chifukwa cha kupereka ndi ubwino wa mawu a m’bale wanu Amoni; ndipo ndikukhumbira kuti ndidziwe chifukwa chimene iye sadabwere kuchokera ku dziko la Midoni ndi inu.

4 Ndipo Aroni adati kwa mfumuyo: Taonani, Mzimu wa Ambuye wamuitanira iye ku njira ina; iye wapita ku dziko la Ismaeli, kukaphunzitsa anthu a Lamoni.

5 Tsopano mfumuyo idati kwa iwo: Kodi ndi chiyani ichi mukunena zokhudzana ndi Mzimu wa Ambuye? Taonani, ichi ndi chimene chikundisautsa ine.

6 Ndiponso, ndi chiyani chimene Amoni adanena kuti—Ngati inu mudzalape mudzapulumutsidwa, ndipo ngati inu simudzalapa, mudzatayidwa patsiku lomaliza?

7 Ndipo Aroni adamuyankha iye ndi kunena kwa iye: Kodi mukukhulupilira kuti kuli Mulungu? Ndipo mfumuyo idati: Ndikudziwa kuti Aamaleki amati kuli Mulungu, ndipo ine ndapereka kwa iwo kuti amange malo opatulika, kuti adzisonkhana wonse pamodzi kulambira iye. Ndipo ngati tsopano inu mukunena kuli Mulungu, taonani ine ndikhulupilira.

8 Ndipo tsopano pamene Aroni adamva izi, mtima wake udayamba kukondwera, ndipo adati: Taonani, ndithudi monga inu muli moyo, O mfumu, kuli Mulungu.

9 Ndipo mfumuyo idati: Kodi Mulungu ndi Mzimu Waukulu uja umene udatulutsa makolo athu kuchokera ku dziko la Yerusalemu?

10 Ndipo Aroni adati kwa iye: Inde, iye ndi Mzimu Waukulu, ndipo adalenga zinthu zonse zakumwamba ndi pa dziko lapansi. Kodi mukukhulupilira izi?

11 Ndipo iye adati: Inde, ndikukhulupilira kuti Mzimu Waukulu udalenga zinthu zonse, ndipo ndikukhumba kuti iwe undiuze ine zokhudzana ndi zinthu zonsezi, ndipo ndidzakhulupilira mawu ako.

12 Ndipo zidachitika kuti pamene Aroni adaona kuti mfumuyo ikhulupilira mawu ake, adayambira kuchokera pa chilengedwe cha Adamu, kuwerenga malembo oyera kwa mfumuyo—m’mene Mulungu adalengera munthu m’chifaniziro chake, ndipo kuti Mulungu adampatsa iye malamulo, ndipo kuti chifukwa cha kulakwitsa, munthu adagwa.

13 Ndipo Aroni adatanthauzira kwa iyo malembo oyera kuyambira pa kulengedwa kwa Adamu, kuyala kugwa kwa munthu pamaso pake, ndi chikhalidwe chawo chathupi ndiponso dongosolo la chiwombolo, limene lidakonzedwa kuyambira pa maziko a dziko lapansi, kudzera mwa Khristu, kwa aliyese amene adzakhulupilire mu dzina lake.

14 Ndipo popeza munthu adagwa, iye sakadatha kuyenerera kalikonse mwa iye yekha; koma mazunzo ndi imfa ya Khristu idatetezera iwo ku machimo awo, kudzera mu chikhulupiliro ndi kulapa, ndi zina zotero; ndipo kuti iye adadula nsinga za imfa, kuti manda adzakhale opanda chipambano, ndi kuti mbola ya imfa imezedwe mu ziyembekezo za ulemelero; ndipo Aroni adafotokoza zinthu zonsezi kwa mfumuyo.

15 Ndipo zidachitika kuti Aroni atamaliza kutanthauzira zinthu izi kwa iyo, mfumuyo idati: Ndingapange chiyani kuti ndikhale ndi moyo wamuyaya umene iwe wakamba? Inde, ndingapange chiyani kuti ine ndibadwe mwa Mulungu, kukhala ndi mzimu woipawu kuzulidwa kuchokera pachifuwa panga, ndi kulandira Mzimu wake, kuti ndidzadzidwe ndi chisangalalo, kuti ndisadzatayike pa tsiku lotsiriza? Taonani, adatero iye, ndidzapereka zonse zomwe ndili nazo, inde, ndidzasiya ufumu wanga, kuti ndilandire chisangalalo chachikuluchi.

16 Koma Aroni adati kwa iyo: ngati mukhumbira chinthu ichi, ngati inu mudzagwada pansi pamaso pa Mulungu, inde, ngati inu mudzalapa machimo anu onse, ndi kugwada pansi pamaso pa Mulungu, ndi kuitanira pa dzina lake m’chikhulupiliro, kukhulupilira kuti inu mudzalandira, pamenepo mudzalandira chiyembekezo chimene inu mukukhumbiracho.

17 Ndipo zidachitika kuti pamene Aroni adanena mawu awa, mfumuyo idagwada pansi pamaso pa Ambuye, pa mawondo ake; inde, mpakana iyo idadzigoneka yokha pansi, ndi kulira mwamphamvu, nati:

18 O Mulungu, Aroni wandiuza ine kuti kuli Mulungu; ndipo ngati kuli Mulungu, ndipo ngati inu muli Mulungu, dziwonetsereni nokha kwa ine, ndipo ine ndidzasiya machimo anga wonse kuti ndikudziweni inu, ndipo kuti ine ndidzaukitsidwe kwa akufa, ndi kupulumutsidwa pa tsiku lotsiriza. Ndipo tsopano, pamene mfumuyo idanena mawu awa, idakanthidwa ngati kuti yamwalira.

19 Ndipo zidachitika kuti adzakazi ake adathamanga ndi kukauza mfumukazi zonse zimene zidachitika kwa mfumuyo. Ndipo iye adabwera kwa mfumuyo; ndipo pamene adaona iyo itagona ngati kuti yamwalira, ndiponso Aroni ndi abale ake ataima ngati kuti ndi amene achititsa kugwa kwakeko, iye adakwiya nawo, ndipo adalamula kuti atumiki ake, kapena adzakazi a mfumuyo, awatenge iwo ndi kuwapha.

20 Tsopano atumikiwo adaona chimene chidachititsa mfumuyo kugwa, kotero sadayerekeze kuika manja awo pa Aroni ndi abale ake; ndipo adachondelera kwa mfumukaziyo nati: Chifukwa chiyani mukulamulira kuti ife tiphe anthu awa, pamene taonani m’modzi wa iwo ali ndi mphamvu kuposa ife tonsefe? Kotero ife tidzagwa pamaso pawo.

21 Tsopano pamene mfumukazi idaona mantha kwa atumikiwo, iyonso adayamba kuopa kwambiri, kuti mwina choipa china chingamugwere. Ndipo iyo idalamula atumiki ake kuti apite ndi kukaitana anthu, kuti adzaphe Aroni ndi azibale ake.

22 Tsopano pamene Aroni adaona kutsimikiza mtima kwa mfumukaziko, iye, podziwanso kuuma kwa mitima ya anthuwo, adaopa kuti khamu lidzasonkhana pamodzi, ndipo padzakhala mkangano waukulu ndi chisokonezo pakati pawo; kotero iye adakweza dzanja lake ndi kudzutsa mfumuyo kuchokera pansi, ndipo adati kwa iyo; Imani. Ndipo idaima ndi mapazi ake, kulandira mphamvu zake.

23 Tsopano izi zidachitidwa pamaso pa mfumukazi ndi ambiri mwa atumiki. Ndipo pamene iwo adaona izi, adazizwa kwambiri, ndipo adayamba kuopa. Ndipo mfumuyo idaima, ndi kuyamba kutumikira kwa iwo. Ndipo iyo idatumikira kwa iwo, kufikira kuti abanja lake onse adatembenukira kwa Ambuye.

24 Tsopano kudali khamu losonkhana pamodzi chifukwa cha chilamulo cha mfumukazi, ndipo padayamba kung’ung’udza kwakukulu pakati pa iwo chifukwa cha Aroni ndi abale ake.

25 Koma mfumuyo idaima pakati pawo ndi kuwatumikira iwo. Ndipo iwo adatonthozedwa kwa Aroni ndi iwo amene adali naye.

26 Ndipo zidachitika kuti pamene mfumu idaona kuti anthu adekha, idachititsa kuti Aroni ndi abale ake aime pakati pa khamulo, ndipo kuti alalikire mawu kwa iwo.

27 Ndipo zidachitika kuti mfumuyo idatumiza chilengezo m’dziko lonselo, pakati pa anthu ake wonse amene adali mu dziko lake lonse, amene adali mu m’zigawo zozungulira ngakhale ku nyanja, ku m’mawa ndi kumadzulo, ndi amene adagawanika kuchokera ku Zarahemula pafupi ndi kachigawo kakang’ono ka chipululu, chimene chimathamangira chakum’mawa kwa nyanja ngakhale ku kumadzulo kwa nyanja, ndipo kuzungulira ku malire a gombe la nyanja, ndi ku malire a chipululu chimene chidali ku mpoto kwa dziko la Zarahemula, kudzera ku malire a Manti, cha kumutu wa mtsinje wa Sidoni, kuthamanga kuchokera ku m’mawa kulowera kumadzulo—ndipo motero Alamani ndi Anefi adagawanika.

28 Tsopano, gawo lambiri la Alamani aulesi limakhala m’chipululu, ndipo amakhala m’mahema; ndipo adamwazikana kuzungulira chipululu chaku madzulo, mu dziko la Nefi; inde, ndiponso chaku madzulo kwa dziko la Zarahemula, mu malire ndi gombe la nyanja, ndi chaku madzulo a dziko la Nefi, mu malo a cholowa choyamba cha makolo awo, ndipo motero kuchita malire ndi gombe la nyanja.

29 Ndiponso kudali Alamani ambiri chaku m’mawa kwa gombe la nyanja, kumene Anefi adawathamangitsira iwo. Ndipo motero Anefi adazunguliridwa ndi Alamani; komabe Anefi adali atatenga madera wonse akumpoto kwa dziko loyandikana ndi chipululu, pamwamba pa mtsinje wa Sidoni, kuchokera kum’mawa mpaka kumadzulo, mozungulira mbali ya chipululu; cha kumpoto, ngakhale mpakana adabwera ku dziko limene adalitcha Lochuluka.

30 Ndipo lidachita malire ndi dziko limene iwo adalitcha Bwinja, ilo lokhala kutali chakumpoto kuti lidafika ku dziko limene mudali anthu ndipo adawonongedwa, amene mafupa awo ife tayankhulapo, amene adapezedwa ndi anthu a Zarahemula, iwo wokhala malo amene iwo adafikira koyamba.

31 Ndipo adachokera kumeneko nakwera kuchipululu cha kum’mwera. Motero dziko la kumpoto linkatchedwa Bwinja, ndipo dziko la kum’mwera linkatchedwa Lochuluka, ilo lokhala chipululu chimene chidali chodzadza ndi mitundu yonse ya zinyama zakutchire za mitundu yosiyasiyana, gawo limene lidabwera kuchokera dziko lakumpoto kusaka chakudya.

32 Ndipo tsopano, udali ulendo wa mtunda watsiku limodzi ndi theka lokha kwa Mnefi, ku malire a Lochuluka ndi dziko la Bwinja, kuchokera kum’mawa kupita ku nyanja yakumadzulo; ndipo motero dziko la Nefi ndi dziko la Zarahemula lidali pafupifupi kuzunguliridwa ndi madzi, kumene kudali khosi laling’ono la nthaka pakati pa dziko lakumpoto ndi dziko lakum’mwera.

33 Ndipo zidachitika kuti Anefi adakhala mu dziko la Lochuluka, ngakhale kuchokera ku m’mawa kufikira ku nyanja yakumadzulo, ndipo motero Anefi mu nzeru zawo, ndi alonda awo ndi magulu ankhondo awo, adali atatsekereza Alamani kum’mwera, kuti mwa kutero iwo asakhalenso ndi cholowa cha kumpoto; kuti asapitirire kulanda dziko lakumpoto.

34 Kotero Alamani sakadatha kukhala ndi zinthu mu dziko la Nefi, ndi kuzungulira m’chipululu. Tsopano izi zidali nzeru mwa Anefi—pakuti Alamani adali adani awo, sakadalora mazunzo awo pa dzanja lirilonse, ndiponso kuti iwo akakhale ndi dziko limene iwo angathawire molingana ndi zokhumba zawo.

35 Ndipo tsopano ine, nditamaliza kunena izi, ndikubwelera ku nkhani ya Amoni ndi Aroni, Omineri ndi Himuni, ndi abale awo.

Print