Malembo Oyera
Alima 41


Mutu 41

Mu chiukitso anthu adzabwera mu chikhalidwe cha chisangalalo chosatha kapena chisoni chosatha—Kuipa sikudakhalepo chisangalaro—Anthu achithupithupi ndi opanda Mulungu pa dziko lapansi—Munthu aliyense amalandiranso mu chibwenzeretso makhalidwe ndi machitidwe amene adalinawo mu chisabvundi. Mdzaka dza pafupifupi 74 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, mwana wanga, ndili ndi zina zakuti ndinene kwa iwe zokhudzana ndi chibwenzeretso chimene chayankhulidwa; pakuti taona, ena adalimbana ndi malembo woyera, ndipo asokonekera chifukwa cha chinthu ichi. Ndipo ndikuona kuti malingaliro ako akhala odandaulanso mokhudzana ndi chinthu ichi. Koma taona, ndikufotokozera ichi kwa iwe.

2 Ndikunena ndi iwe, mwana wanga, kuti dongosolo la chibwenzeretso ndilofunikira ndi chilungamo cha Mulungu; pakuti ndikofunikira kuti zinthu zonse zidzabwenzeretsedwe mu ndondomeko yake yoyenera. Taona, ndikofunikira ndi kolungama, molingana ndi mphamvu ndi chiukitso cha Khristu, kuti mzimu wa munthu udzabwenzeretsedwe ku thupi lake, ndipo kuti gawo lina lililonse la thupi lidzabwelere kwalokha.

3 Ndipo ndikofunikira ndi chilungamo cha Mulungu kuti anthu aweruzidwe molingana ndi ntchito zawo; ndipo ngati ntchito zawo zidali zabwino mu moyo uno, ndipo zokhumba za mtima wawo zidali zabwino, kuti iwo akuyeneranso, pa tsiku lomaliza, kubwenzeretsedwa ku icho chimene chili chabwino.

4 Ndipo ngati ntchito zawo zidali zoipa iwo adzabwenzeretsedwa ku choipa. Kotero, zinthu zonse zidzabwenzeretsedwa ku ndondomeko yake yoyenera, chilichonse ku chilengedwe chake—chakufa kuukitsidwa chosafa, chibvundi ku chisabvundi—kuukitsidwa ku chisangalalo chosatha kukalandira ufumu wa Mulungu, kapena ku chisoni chosatha kukalandira ufumu wa mdyerekezi, m’modzi ku dzanja limodzi ndipo wina ku lina—

5 M’modziyo kuukitsidwa ku chisangalalo molingana ndi zokhumba za chisangalalo. kapena zabwino molingana ndi zokhumba zake za bwino; ndipo wina ku choipa molingana ndi zokhumba zake zoipa; pakuti monga iye ali ndi zokhumba zochita zoipa tsiku lonse monga choncho iye adzalandira mphoto yake ya zoipa pamene usiku udzafika.

6 Ndipo motero zili ku dzanja linali. Ngati iye alapa machimo ake, ndi kukhumbira chilungamo kufikira mapeto a masiku ake, monga choncho iye adzalandira mphoto ya chilungamo.

7 Awa ndi iwo amene awomboledwa mwa Ambuye, inde, awa ndi iwo amene atatulutsidwa, amene ali wopulumutsidwa kuchokera ku usiku wa mdima wosatha uja; ndipo choncho iwo amaima kapena kugwa; pakuti taona, iwo ali oweruza a iwo eni, kaya kuchita zabwino kapena kuchita zoipa.

8 Tsopano, malamulo a Mulungu sangasinthidwe, kotero, njira yakonzedwa kuti aliyense amene angafune ayende m’menemo ndipo adzapulumuka.

9 Ndipo tsopano taona, mwanawanga, usadziikire mulandu wina wolakwira Mulungu wako pa mfundo za chiphunzitso izo, zimene iwe udaziyika iwe pa chiopsezo kufikira tsopano kuti uchite tchimo.

10 Usaganize, chifukwa zayankhulidwa zokhudzana ndi chibwenzeretso, kuti iwe udzabwenzeretsedwa kuchoka ku tchimo kufika ku chisangalalo. Taona, ndinena kwa iwe, kuipa sikudakhalepo chisangalalo.

11 Ndipo tsopano, mwana wanga, anthu onse amene ali mu mkhalidwe wa chilengedwe, kapena ndinganene, mu khalidwe la chithupithupi, ali mu ndulu yowawa ndipo mu nsinga ya uchimo; ali opanda Mulungu mu dziko lapansi, ndipo iwo apita kosemphana ndi chilengedwe cha Mulungu; kotero, ali mu khalidwe losemphana ndi chikhalidwe cha chisangalalo.

12 Ndipo tsopano taona, kodi tanthauzo la mawu achibwenzeretso ndikutenga chinthu cha mkhalidwe wa chilengedwe ndi kuchiika mu khalidwe lachosalengedwa, kapena kuchiika mu mkhalidwe osemphana ndi chilengedwe chake?

13 O, mwana wanga, izi sizili choncho; koma tanthauzo la mawu a chibwenzeretso ndi kubwenzeretsa kachiwiri choipa ku choipa, chithupithupi ku chithupithupi, waudyerekezi ku waudyerekezi—chabwino ku icho chimene chili chabwio, chilungamo ku chimene chili cholungama; choyenera ku chimene chili choyenera; chifundo ku chimene chili chifundo.

14 Kotero, mwana wanga, ona kuti uli wa chifundo kwa abale ako; udzichita choyenera, udziweruza molungama, ndi kuchita zabwino mosalekeza; ndipo ngati uchita zinthu zonsezi ndiye udzalandira mphoto yako; inde, iwe udzakhala ndi chifundo chobwenzeretsedwanso kwa iwe; udzakhala ndi chilungamo kubwenzeretsedwanso kwa iwe; iwe udzakhala ndi chiweruzo cholungama kubwenzeretsedwanso kwa iwe; ndipo iwe udzalandira chabwino chopatsidwanso kwa iwe.

15 Pakuti chimene iwe utumiza kunja chidzabweleranso kwa iwe, ndi kubwenzeretsedwa; kotero, liwu loti chibwenzeretso kwatunthu limaweruza ochimwa ndipo silimamulungamitsa iye konse.

Print