Malembo Oyera
Alima 40


Mutu 40

Khristu amabweretsa chiukitso cha anthu onse—Akufa olungama amapita ku paradiso ndipo oipa kunja kwa mdima kukayembekezera tsiku la chiukitso—Zinthu zonse zidzabwenzeretsedwa m’chimake mu chiukitso. Mdzaka dza pafupifupi 74 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano mwana wanga, izi ndi zina zowonjezera zomwe ndinene kwa iwe; pakuti ndikuona kuti malingaliro ako akudandaula zokhudzana ndi chiukitso cha akufa.

2 Taona, ndikunena ndi iwe, kuti palibe chiukitso—kapena, nditi, m’mawu ena, kuti chivundichi sichivala chisabvundi, choolachi sichivala chosaola—kufikira Khristu atabwera.

3 Taona, iye adzabweretsa chiukitso cha akufa. Koma taona, mwana wanga, chiukitso sichidafike. Tsopano, ine ndikuululira kwa iwe chinsinsi, komabe, pali zinsinsi zambiri zimene zasungidwa, kuti palibe angazidziwe kupatula Mulungu iye mwini. Koma ndikuonetsa iwe chinthu chimodzi chimene ine ndafunsa modzipereka kwa Mulungu kuti ndichidziwe—chimene chili chokhudzana ndi chiukitso.

4 Taona, pali nthawi yoikika yoti wonse adzabwera kuchokera kwa akufa. Tsopano pamene nthawi imeneyi ikubwera palibe akudziwa; koma Mulungu akudziwa nthawi imene yaikidwa.

5 Tsopano, kaya padzakhala nthawi imodzi, kapena nthawi yachiwiri, kapena nthawi yachitatu, yoti anthu adzabwera kuchokera kwa akufa, zilibe kanthu; pakuti Mulungu akudziwa zinthu zonsezi; ndipo ndizokwanira kwa ine kudziwa kuti izi ndi m’mene ziliri—kuti ilipo nthawi yosankhika imene onse adzauka kwa akufa.

6 Tsopano pakuyenera kukhala mpata pakati pa nthawi ya imfa ndi nthawi ya chiukitso.

7 Ndipo tsopano ndikufunsa chidzachitike ndi chiyani pa moyo wa anthu kuchokera pa nthawi yakufa kufikira ku nthawi yosankhidwa ya chiukitso?

8 Tsopano kaya pali nthawi yoposa imodzi yosankhidwa kwa anthu kuuka zilibe kanthu; pakuti onse samafa pa nthawi imodzi, ndipo izi zilibe kanthu; zonse zili ngati tsiku limodzi ndi Mulungu, ndipo nthawi imangoyezedwa kwa anthu.

9 N’chifukwa chake, pali nthawi yosankhidwa kwa anthu imene iwo adzauke kwa akufa; ndipo pali mpata pakati pa nthawi ya kufa ndi chiukitso. Ndipo tsopano, zokhudzana ndi mpata wa nthawi, chomwe chimachitika kwa moyo wa anthu ndi chinthu chimene ine ndafunsa molimbika kwa Ambuye kuti ndidziwe; ndipo ichi ndi chinthu chimene ine ndikudziwa.

10 Ndipo pamene nthawiyo idzafika imene onse adzauka, pamenepo adzadziwa kuti Mulungu amadziwa nthawi zonse zimene zasankhidwa kwa munthu.

11 Tsopano, zokhudzana ndi kukhala kwa mzimu pakati pa imfa ndi chiukitso—Taona, zadziwitsidwa kwa ine ndi mngelo, kuti mizimu ya anthu onse, posakhalitsa pomwe iwo achoka kuchokera ku thupi lachibvundili, inde mizimu ya anthu onse, kaya ndi abwino kapena oipa, imatengedwa kwa Mulungu amene adawapatsa moyo.

12 Ndipo kenako zidzachitika, kuti mizimu ya iwo amene ali olungama idzalandiridwa mkhalidwe wa chisangalalo, umene umatchedwa paradiso, mkhalidwe wopumula, mkhalidwe wamtendere, kumene iwo adzapumule ku mavuto awo onse ndi ku zolabadira zonse ndi chisoni.

13 Ndipo kenako zidzachitika, kuti mizimu ya oipa, inde, amene ali oipa—pakuti taona, alibe mbali kapena gawo la Mzimu wa Ambuye; pakuti taona, iwo adasankha ntchito zoipa m’malo mwa zabwino; kotero mzimu wa mdyerekezi udalowa mwa iwo, ndi kutenga ulamuliro wa mnyumba yawo—ndipo amenewa adzaponyedwa kumidima kunja; kumene kudzakhala kulira, ndi kupfuula ndi kukukuta mano, ndipo izi n’chifukwa cha zolakwa zawo, potsogoleredwa mu ukapolo ndi chifuniro cha mdyerekezi.

14 Tsopano uwu ndiwo mkhalidwe wa mzimu wa oipa, inde, mumdima, ndi mkhalidwe oopsya, mwamantha kuyang’anira ukali wamoto wa mkwiyo wa Mulungu pa iwo; motero iwo akhala mu mkhalidwe umenewu, chimodzimodzi ngati olungama mu paradiso, kufikira nthawi ya chiukitso chawo.

15 Tsopano, pali ena amene adamvetsa kuti mkhalidwe umenewu wa chisangalalo ndi mkhalidwe wa chisoni cha mzimu, pasadafike chiukitso, udali chiukitso choyamba. Inde, ndikuvomereza zikhonza kutanthauza chiukitso, kuuka kwa mzimu kapena moyo ndi kukhazikidwa kwawo mu chisangalalo kapena chisoni, molingana ndi mawu amene ayankhulidwa.

16 Ndipo tsopano, kachiwiri zayankhulidwa, kuti pali chiukitso choyamba, chiukitso cha onse amene adali, kapena ali, kapena adzakhale, kufikira chiukitso cha Khristu kwa akufa.

17 Tsopano, sitikuganiza kuti ichi ndi chiukitso choyamba, chimene chayankhulidwa mu njira iyi, chingakhale chiukitso cha miyoyo ndi kukhazikidwa kwake mu chisangalalo kapena chisoni. Iwe siungaganize kuti izi ndi zomwe zikutanthauza.

18 Taona, ndikunena ndi iwe, Ayi: Koma zikutanthauza kulumikizana kwa mzimu ndi thupi, la iwo kuchokera ku masiku a Adamu kutsikira ku chiukitso cha Khristu.

19 Tsopano, kaya mizimu ndi matupi a iwo amene ayankhulidwa adzaluzanitsidwa pakamodzi, oipa chimodzimodzi ndi olungama, ine sindikunena, izi zikwanile, kuti ndikunena kuti onse adzabwera; kapena m’mawu ena, chiukitso chawo chidzabwera pasadafike chiukitso cha iwo amene afa pambuyo pa chiukitso cha Khristu.

20 Tsopano, mwana wanga, sindikunena kuti chiukitso chawo chikubwera pa chiukitso cha Khristu; koma taona, ndikupereka ngati maganizo anga, kuti mizimu ndi matupi a olungama zidzalumizana, pa chiukitso cha Khristu, ndi kukwera kwake kumwamba.

21 Koma kaya chidzakhala pa chiukitso chake kapena pambuyo, sindikunena; koma izi zokha ndikunena, kuti kuli mpata pakati pa imfa ndi chiukitso cha thupi, ndi mkhalidwe wa mzimu mu chisangalalo kapena chisoni kufikira nthawi imene yasankhidwa ndi Mulungu kuti akufa adzabwera, ndi kulumikizana, zonse mzimu ndi thupi, ndi kubweretsedwa kudzaima pamaso pa Mulungu, ndi kudzaweruzidwa molingana ndi ntchito zawo.

22 Tsopano, izi zikubweretsa kubwenzeretsa kwa zinthu izo zomwe zimene zayankhulidwa ndi pakamwa pa aneneri.

23 Mzimu udzabwenzeretsedwa ku thupi; ndipo thupi lidzabwenzeretsedwa ku mzimu; inde, chiwalo ndi fupa zidzabwenzeretsedwa ku thupi lake; ngakhale tsitsi lakumutu silidzasowa; koma zinthu zonse zidzabwenzeretsedwa m’chimake.

24 Ndipo tsopano mwana wanga, ichi ndicho chibwenzeretso chimene chayankhulidwa ndi pakamwa pa aneneri—

25 Ndipo kenako olungama adzawala mu ufumu wa Mulungu.

26 Koma taona, imfa yoopsya ikubwera pa oipa, pakuti iwo afa monga ku zinthu zokhudzana ndi zinthu za chilungamo; pakuti iwo ndiwodetsedwa, ndipo palibe chinthu chodetsedwa chingalandire ufumu wa Mulungu; koma iwo adzaponyedwa kunja, ndi kuikidwa kolandira zipatso za ntchito yawo kapena zochita zawo, zimene zakhala zoipa, ndipo adzamwa msenga za achikho chowawa.

Print