Zofunikira Zoyambirira
Mawu Oyenera Kudziwa


Mawu Oyenera Kudziwa

Abale otumikira:Amuna apatsidwa mayitanidwe kuti azitha kusamalira zosowa zauzimu ndi zakuthupi za mamembala a mu wodi mwawo. Maitanidwe awa akuperekedwa kwa amuna onse mu Mpingo. Iwo amapatsidwa mabwenzi ndipo amatumidwa kuti akatumikire anthu ena ndi mabanja.

Alongo otumikira:Amayi opatsidwa mayitanidwe kuti azitha kusamalira zosowa zauzimu ndi zakuthupi za mamembala awo. Maitanidwe amenewa apita kwa akazi onse mu mpingo. Nthawi zambiri amapatsidwa mabwenzi ndipo amapatsidwa ntchito yotumikira amayi ena.

Ambuye:Dzina la Mulungu. Nthawi zina limanenanso za Atate athu Akumwamba komanso nthawi zina Yesu Khristu.

Atate Akumwamba:Onani Atate Kumwamba.

Atate Kumwamba:Munthu wangwiro yemwe amaoneka ngati munthu wachivundi koma ali ndi thupi loukitsidwa la mnofu ndi mafupa. Iwo ndi Atate a mizimu yathu, amene timapemphelera. Iwo ndi amphamvu zonse ndipo ndi sadzafa. Iwo amatikonda chifukwa ndife ana awo. Timawatchanso Atate Akumwamba.

Atate Wamuyaya:Dzina lina limene timapeleka kwa Atate athu Akumwamba.

Bishopu:Ofesi mu Unsembe wa Aroni umene umapatsa mwamuna ulamuliro wa umoyo wauzimu ndi wakuthupi wa gulu la mamembala a Mpingo.

Buku la Mormoni:Buku la malemba limene lili ndi ziphunzitso za Atate athu Akumwamba kwa anthu amene ankakhala m’mayiko a ku America.

Chakhumi:Gawo limodzi mwa magawo khumi a zonse zomwe timapeza, zomwe zimaperekedwa ku mpingo.

Chigawo:Dera kapena magawo omwe amagawidwanso mumanthambi pansi pa mishoni ya Mpingo. Imayendetsedwa ndi Purezidenti ndi alangizi ake awiri.

Chilolezo cha M’kachisi:Pepala losainidwa lomwe limalowetsa munthu aliyense wa Mpingo m’kachisi. Kuti apeze pepala, munthuyo ayenera kukhala membala woyenera wa mpingo. Chivomerezocho chimasainidwa ndi atsogoleri oyenerera a unsembe, omwe amachitira umboni za kuyenera kwa munthuyo.

Chiphunzitso ndi Mapangano:Buku la malemba limene liri ndi mawu a Atate athu Akumwamba kwa anthu a masiku ano.

Chitetezero:Malipiro a Yesu, mwa kuzunzika ndi imfa, chifukwa cha machimo a anthu onse amene amawalola kumasulidwa ku zotsatira za imfa yakuthupi ndi yauzimu yobwera chifukwa cha kulakwa kwa Adamu ndi kulekanitsidwa kwa munthu ndi Atate athu Akumwamba.

Chivumbulutso:Chidziwitso choperekedwa ndi Atate athu Akumwamba kwa munthu, nthawi zambiri kudzera mu kulimbikitsidwa kwa Mzimu Woyera, chomwe chingatanthauze zinthu zakale, zamakono, kapena zamtsogolo.

Chopereka posala kudya:Kupereka ndalama zosungidwa pakusala kudya kawiri. Chimaperekedwa ku Mpingo kuti chikathandize osauka.

Dikoni:Ofesi yoyamba mu Unsembe wa Aroni, yomwe ingaperekedwe kwa mamembala oyenera a Mpingo kuyambira mu Januwale chaka chomwe amakwanitsa zaka 12. Umawapatsa ulamuliro wochita ntchito zina zosakhalitsa.

Dziko Lamizimu:Malo amene mizimu ya anthu onse imapita pambuyo pa imfa mpaka kuuka kwa akufa.

Imfa yakuthupi:Imfa yomwe timakumana nayo pamene matupi athu alekanitsidwa ndi mizimu yathu.

Imfa yauzimu:Mkhalidwe wakulekanitsidwa ndi Atate athu Akumwamba.

Kachisi:Nyumba yopatulika, yomwe nthawi zambiri imatchedwa nyumba ya Ambuye, momwemo miyambo yopatulika imachitikira, kuphatikizapo mwambo wa ukwati wamuyaya.

Kholo:Udindo mu Unsembe wa Melkizedeki woperekedwa kwa yemwe ali kale wamkulu wansembe, amene pambuyo pa kudzodzedwa ku udindo wa kholo lakale amapereka madalitso apadera, otchedwa madalitso a makholo, kwa mamembala oyenera a Mpingo.

Kolamu:Gulu lokhazikitsidwa la amuna kapena anyamata omwe ali ndi maudindo ofanana mu unsembe. Koramu ilolonse imayendetsedwa ndi pulezidenti ndi alangizi awiri.

Kubatiza:Kumiza munthu m’madzi ndikum’tulutsa m’madzi kuti akhale ndi moyo watsopano. Onani Ubatizo.

Kubwera Kwachiwiri:Kubweranso kwa Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu, kudzayamba Zakachikwi, kapena nyengo ya mtendere ya zaka chikwi.

Kudzodza:Kupatsa munthu woyenera udindo mu unsembe mwa kusanjika manja.

Kugwa kwa Adamu:Kusintha kumene kunadza kwa Adamu ndi Hava chifukwa cha kudya chipatso choletsedwa. Atate athu Akumwamba adawachotsa pamaso pawo, ndipo adakhala achivundi. Zimenezi zidapangitsa kuti anthu onse adzibadwa komanso adzifa.

Kukwezedwa:Moyo wapamwamba kwambiri mu ufumu wakuselestiyo. Iwo amene alandira kukwezedwa adzakhala ngati Atate athu Akumwamba.

Kulapa:Njira imene munthu wochimwa ayenera kudutsamo kuti akhululukidwe. (Onani Mutu 14.)

Kumidima:Malo amene Satana ndi amene asankha kumutsatira adzakhalamo. Iwo amene amakhala kumeneko sadzakondwa ndi chikoka cha Mzimu Woyera ndipo adzakhala opanda kuwala ndi choonadi.

Kumwamba:Malo amene Atate athu Akumwamba amakhala. Nthawi zina ankatanthauza malo amene mizimu yathu inkakhala isadabwere padziko lapansi, ndiponso kumene imapita tikamwalira (dziko la mizimu). Komanso dzina la malo amene olungama adzakhala ndi moyo kosatha akadzaukitsidwa (ufumu wakuselestiyo).

Kutsindikiza:Mwambo wochitidwa mu kachisi womwe umagwirizanitsa kwamuyaya mwamuna ndi mkazi, kapena ana kwa makolo awo.

Kuuka kwa akufa:Kulumikizananso kwa thupi ndi mzimu, pambuyo pa imfa, kupanga thupi loti silidzafa.

Lamulo la kudzisunga:Lamulo la Atate athu Akumwamba loti munthu azigonana ndi mwamuna kapena mkazi wake basi.

Madzulo a Banja Kunyumba:Msonkhano wa banja, kaŵirikaŵiri Lolemba lililonse madzulo, umene amaimba, kuphunzira uthenga wabwino, kukambirana za vuto lililonse limene ali nalo, kuchita maseŵera, ndi kuchita zinthu zina monga banja.

Mafungulo a unsembe:Ufulu wopereka chilolezo chochita miyambo ya unsembe.

Makumi asanu ndi awiri:Ofesi mu Unsembe wa Melkizedeki. Mwamuna amene ali ndi udindo umenewu ndi mboni yapadera ya Yesu Khristu ndipo amathandiza Atumwi kulamulira mpingo.

Mapangano:Malonjezo opatulika opangidwa pakati pa Atate athu Akumwamba ndi munthu.

Mawu a Nzeru:Lamulo lochokera kwa Atate athu Akumwamba limatiuza zomwe tikuyenera kudya kapena kumwa. Limanena mwachindunji kuti sitikuyenera kumwa mowa, fodya, tiyi, ndi khofi. (Onani Mutu 27.)

Mgonero:Mwambo umene mamembala a Mpingo amadya mkate ndi madzi kuyimira thupi ndi mwazi wa Yesu kutikumbutsa ife za Chitetezero Chake cha machimo.

Mileniyamu:Zaka chikwi za mtendere zimene zidzayamba pamene Yesu adzabweranso padziko lapansi pa nthawi imene ikutchedwa Kudza Kwachiwiri.

Mishoni:(1) Dera la dziko lapansi limene mpingo ukuchita ntchito yaumishonare kapena ukuyenera kutero. Nthawi zambiri amagawidwa m’magawo ang’onoang’ono otchedwa zigawo. (2) Maitanidwe a mtsogoleri wa mpingo kuti alalikire uthenga wabwino kapena kupereka utumiki kwa nthawi yoyikika.

Mitundu khumi:Mbadwa za khumi mwa ana khumi ndi aŵiri a Israeli (Yakobo) amene adatengedwa kupita ku ukapolo ndipo kumene malo awo adatayika kuchokera pa chidziŵitso cha anthu.

Mkulu:Ofesi yoyamba mu Unsembe wa Melkizedeki yoperekedwa kwa amuna oyenera omwe ali ndi zaka 18 kapena kupitilira apo. Zimawapatsa ulamuliro wochita miyambo ina, yomwe ndi madalitso m’miyoyo ya anthu ena.

Mkulu Wansembe:Ofesi mu Unsembe wa Melkizedeki yomwe ili ndi udindo woyang’anira zinthu zauzimu.

Mlosi:Amene angathe kuoneratu zam’tsogolo chifukwa zaululidwa kwa iye ndi Atate athu Akumwamba. Owona amafanana ndi mneneri.

Mneneri:Munthu woitanidwa ndi Atate athu Akumwamba amene amalankhulana ndi Iwo ndi kuwalankhulira.

Moyo:Zimatanthauza chimodzimodzi munthu (thupi ndi mzimu pamodzi). Komabe, nthawi zina mawuwa amagwiritsidwa ntchito kutanthauza mzimu wa munthu.

Moyo Wamuyaya:Izi sizikutanthauza kukhala ndi moyo kwamuyaya kokha komanso kukhala ndi moyo womwe Atate athu Akumwamba amakhala nawo ndikukhala ngati Iwo. Kumatanthauza chimodzimodzi monga kukwezedwa.

Mpatuko:(1) Mkhalidwe wa kuchoka kwa uzimu kwa Atate athu Akumwamba. (2) Nthawi imene ziphunzitso za Atate athu Akumwamba ndi unsembe Wawo padalibe padziko lapansi.

Mphatso:Madalitso amene amaperekedwa ndi Atate athu Akumwamba mu makachisi ndipo ndiofunikira kuti tikwezedwe.

Mphatso ya Mzimu Woyera:Ufulu wokhala nayo mphamvu yosalekeza ya Mzimu Woyera. Mphatso imeneyi imaperekedwa pambuyo pa ubatizo.

Mphunzitsi:Ofesi mu Unsembe wa Aroni, yomwe ingaperekedwe kwa mamembala oyenerera a Mpingo kuyambira mu Januwale chaka chomwe amakwanitsa zaka 14. Dzinali limachokera ku umodzi mwa maudindo a ofesiyi, omwe ndi kuphunzitsa mamembala a mpingo.

Mpingo:Onani Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza.

Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza:Dzina lovomerezeka la Mpingo wa Yesu Khristu, limene Iye adalibwenzeretsa kudzera mwa Mneneri Joseph Smith mu nthawi yathu. Mpingo uwu nthawi zina umatchedwa dzina la Mpingo wa Mormoni.

Mpulumutsi:Wopulumutsa mnzake ku chinthu chovulaza. Yesu ndi Mpulumutsi wathu chifukwa anatipulumutsa ku imfa yakuthupi ndi yauzimu.

Mtumwi:Ofesi mu Unsembe wa Melkizedeki. Atumwi ndi mboni zapadera za Yesu Khristu padziko lonse lapansi.

Mulungu:Wam’mwambamwamba ndi wolamulira wa chilengedwe chonse. Dzina lakuti Mulungu nthawi zambiri limatanthauza Atate athu Akumwamba, koma nthawi zina m’malemba limanena Yesu.

Mwambo:Mwambo wochitidwa kudzera mu ulamuliro wa unsembe.

Mzimu:Zimene zimapatsa thupi moyo. Ndi mbali ya thupi imene idalipo moyo uno usadakhalepo ndipo imapitirizabe kukhalapo tikamwalira. Mzimu ndi thupi zidzagwirizananso pa chiukitsiro, sizidzalekanitsidwanso.

Mzimu Woyera:Munthu wauzimu amene alibe thupi lanyama ndipo cholinga chake ndi kuchitira umboni zimene Atate athu Akumwamba ndi Yesu adanena ndi kuchita. Tikamanena kuti Mzimu wa Atate athu Akumwamba uli nafe, tikunena za Mzimu Woyera.

Ndende ya Uzimu:Gawo la dziko la mizimu kumene mizimu ya mitundu itatu ya anthu imapita pambuyo pa imfa: amene adali oipa m’moyo uno, amene adakhala ndi moyo wabwino koma sadavomereze kapena kukhala ndi uthenga wabwino, ndi amene sadakhale ndi mwayi womva uthenga wabwino. Pamapeto pake anthu onsewo adzaukitsidwa.

Ngale Yamtengo Wapatali:Bukhu la malembo lokhala ndi zolemba za Mose, Abrahamu, ndi Joseph Smith. Dzinali kwenikweni limatanthauza mwala wamtengo wapatali kwambiri, umene ndi mmene bukuli limaonedwera ndi mamembala a Tchalitchi.

Nsembe:(1) Kale, kupha nyama pakumvera lamulo la Atate athu Akumwamba. (2) Lerolino, kusiya chinthu chimene chili chaphindu kwa ife, monga ngati nthaŵi ndi chuma chathu, kuti tithandize ena.

Nthambi:Kugwiritsiridwa ntchito kophiphiritsa kwa tsinde la mtengo kuimira kagawo kakang’ono kapena gulu lokonzekera la banja lalikulu la Mpingo. Kugawanikaku kumachokera ku malire a malo omwe mamembala amakhala ndikukumana pamodzi pansi pa ulamuliro wa atumiki ovomerezeka a Atate athu Akumwamba.

Nyumba ya Israeli:Aliyense mwa mbadwa zachibadwa kapena zotengedwa mwa ana khumi ndi awiri a Yakobo, amene dzina lake lidasinthidwa kukhala Israeli (onani Genesis 32:28).

Ofesi:Udindo waulamuliro mkati mwa unsembe. (Onani Dikoni, Mphunzitsi, Wansembe, ndi zina zotero.)

Oyera mtima:Mawuwa amagwiritsidwa ntchito kuzindikiritsa membala wa Mpingo woona wa Yesu.

Paradizo:Gawo la dziko la mizimu kumene kuli mizimu yolungama.

Siteki:Mgwirizano wa mamembala mkati mwa dera lomwe mpingo uli wakhazikitsidwa mokwanira ndikulamuliridwa ndi atsogoleri osankhidwa a unsembe. Amagawidwa m’magulu ang’onoang’ono otchedwa mawodi ndi nthambi.

Tsiku la Sabata:Tsiku la mpumulo losankhidwa ndi Yesu kukhala tsiku lolambira Atate athu Akumwamba ndi kutumikira ena. Limatsatidwa pa Lamlungu m’malo ambiri padziko lapansi.

Ubatizo:Mwambo wofunika wa uthenga wabwino umene munthu amachita mapangano ndi Atate athu Akumwamba kuti awamvera Iwo ndipo Atate athu Akumwamba amalonjeza kukhululukira ndi kuyeretsa munthuyo ku uchimo ndi kumulora iye kukhala membala wa Mpingo Wawo. Mwambowu ukuyimira kubadwanso mwatsopano pakumizidwa m’madzi ndi kuukitsidwa ku moyo watsopano. Mwambowu umachitidwa ndi iwo omwe aloledwa kukhala ndi unsembe ndikuchita mwa Atate athu Akumwamba.

Ubatizo wa akufa:Ubatizo m’kachisi ya Atate athu Akumwamba wa munthu wamoyo amene amalowa m’malo mwa munthu amene wamwalira.

Ufumu wakuselestiyo:Ufumu umenewo kumene olungama amakhala pamaso pa Atate athu Akumwamba ndi kulandira zonse zimene ali nazo.

Ufumu wakutelestiyo:Ufumu wotsikitsitsa mwa maufumu atatu aulemerero omwe anthu adzapatsidwa pambuyo pa chiukitsiro. Ufumu umenewu wasungidwira anthu abodza, ambanda, akuba, ndi anthu ena oipa.

Ufumu wakuterestriyo:Ufumu wa ulemelero umene udindo wake uli pansi pa ufumu wakuselestiyo koma pamwamba pa ufumu wakutelestiyo. Iwo wasungidwira anthu abwino a padziko lapansi amene sadachite zonse zimene Atate athu Akumwamba adafuna kwa iwo.

Ukwati Wamuyaya:Ukwati umene watsindikizidwa mu kachisi ndipo umapitilira kwamuyaya tikamwalira ngati tili oyenera kukhala ndi Atate athu Akumwamba.

Uneneri:Mawu ouziridwa a mneneri, nthawi zambiri okhudza zochitika zamtsogolo.

Unsembe:Ulamuliro umene Atate athu Akumwamba amapereka kwa anthu kuti agwire ntchito yawo ndi kuwalankhulira. Pali magawo awiri: waukulu kapena Unsembe wa Melkizedeki ndi waung’ono kapena wa Aroni.

Unsembe wa Aroni:Ulamuliro wochepa wa unsembe uwiri umene Atate athu Akumwamba Apereka kwa anthu padziko lapansi kuti achite mu dzina Lawo kaamba ka chipulumutso cha ana Awo. Unsembe waung’ono uwu udatenga dzina lake kuchokera kwa Aroni, m’bale wake wa Mose, ndipo ndi wosiyana ndi waukulu kapena Unsembe wa Melkizedeki. Unsembe wa Aroni umaphatikizapo maudindo a dikoni, mphunzitsi, wansembe, ndi bishopu.

Unsembe wa Melkizedeki:Ukulu wa unsembe uwiriwo, umene uli ndi maudindo a mkulu, nkulu wansembe, kholo, Amakumi asanu ndi awiri, ndi Atumwi.

Uthenga Wabwino:Ziphunzitso za Yesu Khristu, zimene zikatsatiridwa, zidzalola munthu kubwelera kukakhala pamaso pa Atate athu Akumwamba.

Wansembe:Ofesi mu Unsembe wa Aroni, yomwe ingaperekedwe kwa mamembala oyenera a Mpingo kuyambira mu Januwale chaka chomwe amakwanitsa zaka 16. Ofesi iyi imawapatsa iwo ulamuliro wochita maubatizo ndi kudzodza kwa Unsembe wa Aroni, kudalitsa mgonero, ndi kuchita ntchito zina.

Wodi:Gulu la mamembala a Mpingo lokonzedwa mkati mwa siteki, omwe amalamuliridwa ndi bishopu ndi alangizi ake awiri.

Yerusalemu Watsopano:Mzinda umene udzamangidwa m’chigawo cha Missouri, m’dziko la United States, zaka chikwi zisanayambe. Yesu adzayendetsa boma lake, ufumu wa Atate athu Akumwamba padziko lapansi, kuchokera kumalo ano mu nthawi ya Zaka chikwi.

Yesu Khristu:Wamkulu wa ana auzimu a Atate athu Akumwamba, Mlengi wa dziko lapansi, ndi Mpulumutsi ndi Muomboli wathu. Iye adabwera padziko lapansi kudzalipira machimo a tonsefe. (Onani makamaka mitu 3, 11, ndi 12.)

Ziyoni:Dzina lina la Yerusalemu Watsopano, mzinda umene Yesu adzalamulira dziko lapansi m’kati mwa Zaka zikwi.

Print