Malembo Oyera
2 Nefi 9


Mutu 9

Yakobo afotokoza kuti Ayuda adzasonkhanitsidwa mu m’maiko awo onse a lonjezano—Chitetezero chimaombola munthu ku kugwa—Matupi a okufa adzatulu m’manda, ndipo mizimu yawo kuchokera ku gahena ndi ku paradiso—Iwo adzaweruzidwa—Chitetezero chimapulumutsa ku imfa, gahena, mdyerekezi, ndi mazunzo osatha—Olungama adzapulumuka mu ufumu wa Mulungu—Zilango za uchimo zikhazikitsidwa—Oyera wa Israeli ndiye mlonda wa chipata. Mdzaka dza pafupifupi 559–545 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, abale anga okondedwa, ndawerenga zinthu izi kuti mudziwe zokhudzana ndi mapangano a Ambuye amene adapangana ndi onse a nyumba ya Israeli—

2 Kuti iye adayankhula kwa Ayuda, ndi pakamwa pa aneneri ake oyera, ngakhale kuyambira pa chiyambi kufikira ku m’badwo ndi m’badwo, kufikira nthawi ikudza imene iwo adzabwenzeretsedwa ku mpingo oonadi ndi khola la Mulungu; pamene adzasonkhanitsidwe kwawo ku maiko a cholowa chawo, ndipo adzakhazikika m’maiko awo a lonjezo.

3 Taonani, abale anga okondedwa, ndikuyankhula kwa inu zinthu izi kuti musangalale, ndi kukweza mitu yanu kunthawi zosatha, chifukwa cha madalitso amene Ambuye Mulungu adzapeleke kwa ana anu.

4 Pakuti ndikudziwa kuti inu mudafufuza zambiri, ambiri mwa inu, kuti mudziwe za zinthu zirinkudza; kotero ndikudziwa kuti mukudziwa kuti thupi lathu liyenera kuonongeka ndi kufa; komabe, m’matupi athu tidzamuona Mulungu.

5 Inde, ndikudziwa kuti mukudziwa kuti mu thupi iye adzadzionetsera yekha kwa iwo amene ali ku Yerusalemu, kumene ife tidachokera; pakuti kuli koyenera kwambiri kutizikhale pakati pawo; pakuti ndichoyenera mlengi wankulu kuti adzilolere yekha kukhala wogonjera kwa munthu mu thupi, ndi kufera anthu onse, kuti anthu onse athe kukhala ogonjera kwa iye.

6 Pakuti monga imfa idutsa kwa anthu onse, kukwaniritsa dongosolo la chifundo cha mlengi wankulu, pakuyenera kukhala mphamvu ya chiukitso, ndipo chiukitso chikuyenera kubwera kwa munthu chifukwa cha kugwa; ndipo kugwa kudabwera chifukwa cha kulakwitsa; ndipo chifukwa munthu adagwa, adachotsedwa pamaso pa Ambuye.

7 Kotero, chikuyenera kukhala chitetezero chopanda malire—pokhapokha chili chitetezero chopanda malire chivundi ichi sichikadavala chisavundi. Kotero, chiweruzo choyamba chimene chidabwera kwa munthu chikadakhala chopanda malire. Ndipo ngati ziri choncho, thupi ili likadaikidwa kuti livunde ndi kufumbutuka ku dothi, osadzaukanso.

8 O nzeru za Mulungu, chifundo chake ndi chisomo! Pakuti taonani, ngati thupi silidzaukanso, mizimu yathu ikuyenera kukhala yomvera kwa mngelo amene adagwa kuchokera pamaso pa Mulungu wa Muyaya, ndi kukhala mdyerekezi, osadzaukanso.

9 Ndipo mizimu yathu ikadayenera kukhala ngati iye, ndipo tikadakhala ziwanda, angelo a mdyerekezi, kutsekeledwa pamaso pa Mulungu wathu, ndi kukhala ndi tate wamabodza, m’masautso, ngati iye mwini; inde, kwa munthu amene adanamiza makolo athu oyamba, amene adadzisandutsa yekha ngati mngelo wa kuunika, ndipo amautsa ana a anthu ku migwirizano yachinsinsi ya kupha ndi zina zonse za zintchito zachinsinsi za mumdima.

10 O ndiwaukulu motani ubwino wa Mulungu wathu, amene wakonza njira yoti tithawe ku kugwidwa ndi chilombo choipa ichi; inde, chilombo icho, imfa ndi gahena, imene ine ndikuitcha imfa ya thupi, ndiponso imfa ya mzimu.

11 Ndipo chifukwa cha njira ya chiwombolo ya Mulungu wathu, Oyera wa Israeli, imfa iyi, imene ndakamba, yomwe ndiyanthawi yochepa, idzapereka akufa ake; amene imfa yake ndi manda.

12 Ndipo imfa iyi imene ndakambayi, imene ndi imfa ya uzimu, idzapereka akufa ake; imene imfa yauzimu ndi gahena; kotero, imfa ndi gahena ziyenera kupereka akufa awo, ndipo gahena akuyenera kupereka mizimu ya m’nsinga, ndipo manda akuyenera kupereka matupi am’nsinga, ndipo matupi ndi mizimu ya anthu zidzabwenzeretsedwa wina kwa nzake; ndipo ndi mwa mphamvu ya chiukitso ya Oyera wa Israeli.

13 O ndi lalikulu bwanji dongosolo la Mulungu wathu! Pakuti ku dzanja lina, ku paradiso wa Mulungu akuyenera kupereka mizimu ya anthu olungama, ndipo manda kupereka thupi la olungama; ndipo mzimu ndi thupi zidzabwenzeretsedwa kwa izo zokha kachiwiri, ndipo anthu onse adzakhala a chisavundi, ndi osafa, ndipo iwo ali moyoyo yamoyo, yokhala ndi chidziwitso chonse monga ife mu thupi, kupatula kuti ife chidziwitso chathu chidzakhala chamngwiro.

14 Kotero, tidzakhala ndi chidziwitso chonse cha zolakwa zathu zonse, ndi zodetswedwa zathu, ndi umaliseche wathu; ndipo olungama adzakhala ndi chidziwitso chonse cha chisangalalo chawo, ndi chilungamo chawo, atavekedwa ndi chiyero, inde ngakhale ndi mwinjoro wa chilungamo.

15 Ndipo zidzachitika kuti pamene anthu onse adzadutsa ku imfa yoyamba iyi ndikukhala moyo, kwambiri pamene adzakhale osafa, iwo ayenera kuonekera pafupi ndi mpando wa chiweruzo wa Oyera wa Israeli; ndipo kenako kudzabwera chiweruzo, ndipo kenako iwo ayenera kuweruzidwa molingana ndi chiweruzo choyera cha Mulungu.

16 Ndipo motsimikiza, monga Ambuye ali wamoyo, pakuti Ambuye Mulungu wachiyankhula, ndipo ndi mawu ake a muyaya, amene sadzatha, kuti iwo amene ali olungama adzakhalabe olungama, ndipo iwo amene ali onyansa adzakhalabe onyansa, kotero, iwo amene ali onyansa ndi a mdyerekezi ndi angelo ake; ndipo adzapita ku moto osatha, udakonzeredwera iwo; ndipo kuzunzika kwawo kuli ngati nyanja ya moto ndi sulufure, imene lawi lake likwera m’mwamba kunthawi zosatha ndipo liribe malire.

17 O ukulu ndi chilungamo cha Mulungu wathu! Pakuti iye amachita mawu ake onse, ndipo apita kuchokera pakamwa pake, ndipo lamulo lake likuyenera kukwaniritsidwa.

18 Koma, taonani, olungama, oyera mtima a Oyera wa Israeli, iwo amene adakhulupilira mwa Oyera wa Israeli, iwo amene adapilira mitanda ya dziko lapansi, nanyoza manyazi ake, iwo adzalandira ufumu wa Mulungu, umene adawakonzera kwa iwo kuchokera pa maziko a dziko lapansi, ndipo chimwemwe chawo chidzakhala chodzadza kunthawi zosatha.

19 O ukulu wa chifundo cha Mulungu wathu, Oyera wa Israeli! Pakuti amawombola oyera mtima ake ku chilombo choopsya mdyerekezi, ndi gahena, ndi nyanja ya moto ndi sulufure, chimene chili mazunzo chosatha.

20 O ndi chachikulu bwanji chiyero cha Mulungu wathu! Pakuti iye amadziwa zinthu zonse, ndipo palibe chinthu koma iye amadziwa.

21 Ndipo akubwera ku dziko lapansi kuti adzapulumutse anthu onse ngati iwo adzamvera mawu ake; pakuti taonani, iye amamva kuwawa kwa anthu onse, inde, zowawa za cholengedwa cha moyo chilichonse, onse abambo, amayi, ndi ana, amene ali a banja la Adamu.

22 Ndipo amamva zowawa izi kuti chiukitso chifikire kwa anthu onse, kuti onse adzathe kuyima pamaso pake pa tsiku lalikulu la chiweruzo.

23 Ndipo walamulira anthu onse kuti akuyenera kulapa, ndi kubatizidwa mu dzina lake, kukhala ndi chikhulupiliro chonse mwa Oyera wa Israeli, kupanda apo sangapulumutsidwe mu ufumu wa Mulungu.

24 Ndipo ngati sadzalapa ndi kukhulupilira mu dzina lake, ndi kubatizidwa mu dzina lake, ndi kupilira kufikira chimaliziro, ayenera kudzalangidwa, pakuti Ambuye Mulungu, Oyera wa Israeli, wayankhula izi.

25 Kotero, iye wapereka lamulo; ndipo pamene palibe lamulo loperekedwa palibe chilango, ndipo pamene palibe chilango, palibe kutsutsidwa, ndipo pamene palibe kutsutsidwa zifundo za Oyera wa Israeli zikhala zilipo pa iwo, chifukwa cha chitetezero; pakuti iwo apulumutsidwa ndi mphamvu yake.

26 Pakuti chitetezero chimakwaniritsa zofuna za chilungamo chake kwa onse amene alibe lamulo lopatsidwa kwa iwo, kuti iwo awomboledwe ku chilombo choopsya icho, imfa ndi gahena, ndi mdyerekezi, ndi nyanja ya moto ndi sulufure, imene ndi mazunzo osatha; ndipo abwenzeretsedwa kwa Mulungu amene adawapatsa mpweya, amene ali Oyera wa Israeli.

27 Koma tsoka kwa iye amene wapatsidwa lamulo, inde, amene ali ndi malamulo onse a Mulungu, ngati ife, ndipo awalakwira, ndi kutaya masiku a kuyesedwa kwake, pakuti kakhalidwe kake ndikoopsya!

28 O dongosolo lochenjera monama la oyipayo! O zachabechabe, zofooka ndi kupusa kwa anthu! Pamene aphunzira amaganiza kuti ali ndi nzeru, ndipo samvera malangizo a Mulungu, pakuti amawaika pambali, kuganiza kuti iwo amadziwa mwaokha, kotero, nzeru zawo ndi zopusa ndipo siziwapindulira. Ndipo adzawonongedwa.

29 Koma kuphunzira ndikwabwino ngati iwo amvera malangizo a Mulungu.

30 Koma tsoka kwa olemera, amene ali olemera monga ku zinthu za padziko lapansi. Pakuti chifukwa ndi olemera amanyoza osauka ndipo iwo kuzunza ofatsa, ndipo mitima yawo ili pa chuma chawo; kotero, chuma chawo ndi mulungu wawo. Ndipo taonani, chuma chawo chidzatha limodzi ndi iwo omwe.

31 Ndipo tsoka kwa ogontha amene sadzamva; pakuti adzaonongedwa.

32 Tsoka kwa akhungu amene sadzaona, pakuti nawonso adzaonongedwa.

33 Tsoka kwa osadulidwa mu mtima, pakuti chidziwtso cha kusaweruzika kwawo kudzawakantha patsiku lotsiriza.

34 Tsoka kwa wabodza, pakuti adzaponyedwa ku gahena.

35 Tsoka kwa okupha amene amapha mwadala, pakuti iye adzafa.

36 Tsoka kwa iwo ochita zachiwerewere, pakuti adzaponyedwa ku gahena.

37 Inde, tsoka kwa iwo amene amapembedza mafano, pakuti mdyerekezi wa ziwanda zonse akondwera nawo.

38 Ndipo, pomaliza, tsoka kwa iwo amane amafa mu uchimo wawo; chifukwa adzabwelera kwa Mulungu, ndipo adzapenya nkhope yake, ndi kukhalabe mu uchimo.

39 Inu, abale anga okondedwa, kumbukirani kuipa kwa kulakwira Mulungu Oyerayo, ndiponso kuipa kwa kugonjera ku zokopa za woipayo. Kumbukirani, kukhala ndi maganizo-athupi ndi imfa, ndipo kukhala ndi maganizo-auzimu ndi moyo wamuyaya.

40 Inu, abale anga okondedwa, tchelani khutu ku mawu anga. Kumbukirani ukulu wa Oyera wa Israeli. Musanene kuti ndayankhla zinthu zovuta kwa inu; pakuti mukatero, mukutsutsana ndi choonadi; pakuti ndayankhula mawu a Mlengi wanu. Ndikudziwa kuti mawu a choonadi ndi ovuta motsutsana ndi zodetsedwa zonse; koma olungama samawaopa, pakuti amakonda choonadi ndipo samagwedezeka.

41 Inu tsono, abale anga okondedwa, bwerani kwa Ambuye, Oyerayo. Kumbukirani kuti njira zake ndi zolungama. Taonani, njira ya munthu ndi yopapatiza, koma imakhala njira yolunjika pamaso pake, ndipo mlonda wapachipata ndiye Oyera wa Israeli; ndipo salemba wantchito pamenepo; ndipo palibe njira ina koma pa chipata; pakuti iye sanganamizidwe, pakuti Ambuye Mulungu ndiye dzina lake.

42 Ndipo iye amene agogoda, kwa iye adzatsekulilidwa, ndipo anzeru, ndi ophunzira, ndi awo amene ali olemera, amene ali odzitukumula chifukwa cha kuphunzira kwawo, ndi nzeru zawo, ndi chuma chawo—inde, ndi iwo amene iye amadana nawo; ndipo pokhapokha adzataya zinthu izi, ndi kudziyesa okha opusa pamaso pa Mulungu, ndipo kudzitsitsa pansi mu kuya kwa kudzichepetsa, iye sadzawatsekulira iwo.

43 Koma zinthu za anzeru, ndi ochenjera zidzabisidwa kwa iwo ku nthawi zosatha—inde, chimwemwe chimene chakonzedwa kwa oyera mtima.

44 Inu, abale anga okondedwa, kumbukirani mawu anga. Taonani, ndivula chovala changa, ndipo ndachisasa pamaso panu; ndikupemphera Mulungu wa chipulumutso changa kuti andione ine ndi diso lake loona-zonse; kotero, inu mudzadziwa pa tsiku lomaliza; pamene anthu onse adzaweruzidwe ku ntchito zawo, kuti Mulungu wa Israeli adachitira umboni kuti ndidasasa mphulupulu zanu m’moyo wanga, ndipo kuti ndikuima ndi kuwala pamaso pake, ndipo ndachotsa mwazi wanu pa ine.

45 Inu, abale anga okondedwa, tembenukani ku machimo anu, gwedezani maunyolo a iye amene akufuna kukumangani inu, bwerani kwa Mulungu amene ali thanthwe la chipulumutso chanu.

46 Konzekeretsani miyoyo yanu ku tsiku la ulemelero pamene chilungamo chidzapelekedwa kwa olungama, ngakhale tsiku la chiweruzo, limene inu musadzakhale ndi mantha oopsya; kuti musadzathe kukumbukira kulakwa kwanu konse mu ungwiro, ndi kukakamizika kunena kuti: Oyera, oyera ndi maweruzo anu, O Ambuye Mulungu wa mphamvu zonse—koma ndikudziwa kulakwa kwanga; ndidalakwira malamulo anu, ndipo kulakwitsa kwanga ndi kwanga; ndipo mdyerekezi wanditenga ine, kuti ndine ogwidwa ku masautso ake oopsya.

47 Koma taonani, abale anga, ndikoyenera kuti ndikudzutseni inu ku zoopsa zenizeni za zinthu izi? Kodi ndikadakhumudwitsa moyo wanu ngati maganizo anu adali oyera? Kodi ndikadayankhula zomveka kwa inu molingana ndi kumveka kwa choonadi ngati inu mudali omasulidwa ku tchimo?

48 Taonani, mukadakhala oyera ndikadayankhula nanu za chiyero; koma chifukwa inu si oyera, ndipo mumayang’ana kwa ine ngati mphunzitsi, kuyenera kukhala koyenera kuti ndikuphunzitseni zotsatira za uchimo.

49 Taonani, moyo wanga unyansidwa ndi tchimo, ndipo mtima wanga ukondwera ndi chilungamo; ndipo ndidzalemekeza dzina loyera la Mulungu wanga.

50 Bwerani, abale anga, aliyense amene akumva ludzu, bwerani ku madzi; ndipo iye amene alibe ndalama, bwerani mudzagule ndi kudya, inde bwerani mudzagula vinyo ndi mkaka opanda ndalama ndi opanda mtengo.

51 Kotero, musaononge ndalama pa zinthu zimene zili zopanda pake, ngakhale kugwira ntchito pa zinthu zomwe sizingakwaniritse. Mvetserani mwakhama kwa ine, ndipo kumbukirani mawu amene ndayankhula; ndikubwera kwa Oyera wa Israeli, ndikudyelera zomwe sizingaonongeke, kapena sichingavunde, ndipo lolani moyo wanu ukondwere mu zonona.

52 Taonani, abale anga okondedwa, kumbukirani mawu a Mulungu wanu, pempherani kwa iye mosalekeza masana, ndi kuyamika dzina lake loyera usiku. Lolani mitima yanu ikondwere.

53 Ndipo taonani ndi aakulu bwanji mapangano a Ambuye, ndipo ndikwakukulu bwanji kudzichepetsa kwake kwa ana a anthu; ndipo chifukwa cha ukulu wake, ndi chisomo chake ndi chifundo chake, wapanga lonjezo kwa ife kuti mbewu yathu siidzaonongedwa, molingana ndi thupi, koma kuti iye adzateteza iwo; ndipo mibadwo yamtsogolomo idzakhala nthambi yolungama ya nyumba ya Israeli.

54 Ndipo tsopano, abale anga, ndikadati ndiyankhule kwa inu zambiri; koma mawa ndikuuzani inu mawu anga otsalira. Ameni.

Print