Zofunikira Zoyambirira
Mutu 3: Mpulumutsi Wathu


Mutu 3

Mpulumutsi Wathu

Kodi ndani amene angatitsogolere kuti tibwelere kwa Atate athu Akumwamba? Chifukwa chiyani tiyenera kumutsatira Iye?

Tinkafunikira Mtsogoleri

Atate athu Akumwamba adadziwa kuti pamene tidzakhale pa dziko lapansi sitidzakumbukira moyo wathu ndi Iwo. Sitidzadziwa zinthu zimene tiyenera kuchita kuti tibwelere kwa Iwo. Adadziwanso kuti tidzachimwa. Chifukwa cha machimo athu, tidzalangidwa pakulekanitsidwa ndi Iwo kwamuyaya. Ndipo pamene tidzafa, sitidzakhalanso ndi matupi athu a mnofu ndi mafupa.

Tidzafunikira munthu wina kuti atithandize ku mavuto amenewa. Munthu ameneyu adzatiphunzitsa zomwe tikuyenera kuchita kuti tibwelere kwa Atate athu Akumwamba. Iye adzatithandiza kugonjetsa zoipa zimene tidzachite. Iye adzatikonzeranso njira yoti tidzakhalenso ndi matupi athu amnofu ndi mafupa tikadzamwalira. Munthu ameneyu adzatchedwa Mpulumutsi wathu. Iye yekha ndi amene adzatipulumutse kuchilango cha zinthu zimene tingadzachite zolakwika. Ndi Iye yekha amene angadzatithandize kuphunzira kumvera Atate athu Akumwamba. Ndi Iye yekha amene akanatha kutipangitsa kukhala ndi matupi athu a mnofu ndi mafupa pambuyo pa imfa.

Zokambirana

  • Ndi mavuto ati ena amene Atate athu Akumwamba adadziŵa kuti tidzakumana nawo pa dziko lapansi?

  • Ndi chifukwa chiyani tifunika Mpulumutsi kuti atithandize?

Atate athu Akumwamba Adasankha Yesu Kukhala Mpulumutsi Wathu

Atate athu Akumwamba amatikonda, ndipo ankadziwa kuti tidzafunikira thandizo. Iwo ankadziwa kuti tidzakhala achisoni kwambiri ngati sitidzakhala ndi matupi amnofu ndi mafupa ndipo sitidzatha kubwelera kukakhala nawo kwa muyaya. Tinkafunikira munthu woti atithandize. Atate athu Akumwamba ankafuna kuti munthu wina akhale Mpulumutsi wathu. Awiri mwa abale athu adadzipereka kukhala Mpulumutsi wathu.

M’bale wathu wamkulu, Yesu, adapempha Atate athu Akumwamba kuti amutumize. Iye adati adzatsatira dongosolo la Atate athu Akumwamba. Iye adzabwera pa dziko lapansi ndi kutiphunzitsa zinthu zimene tifunika kuchita kuti tibwelere kwa Atate athu Akumwamba. Iye adzafa kuti atilipilire chifukwa cha zoipa zimene tidzachita. Adzachititsanso kuti tikhalenso ndi moyo tikadzamwalira. Iye adzatilora ife kusankha tokha kumvera kapena kusamvera Atate athu Akumwamba.

Yesu ankadziwa kuti kudzakhala kofunika kwa ife kusankha mwatokha zinthu zoti tingachite. Ngati wina atikakamiza kumvera, sitingathe kuphunzira ndi kukhala ngati Atate athu Akumwamba. Yesu adafuna kuti Atate athu Akumwamba akhale ndi ulemelero ndi ulemu wonse.

Satana, amene ankatchedwa Lusifala, adapemphanso Atate athu Akumwamba kuti amusankhe kukhala Mpulumutsi wathu. Iye adanena kuti adzabwera pa dziko lapansi n’kutikakamiza kuchita zimene tikuyenera kuchita. Iye adanena kuti palibe aliyense wa ife amene adzatayike. Sadakatilora kuti tizidzisankhila tokha. Monga mphotho yake, iye adafuna ulemelero ndi ulemu wonse umene Atate athu Akumwamba adali nawo.

Chifukwa chakuti Atate athu Akumwamba amatikonda, adasankha Yesu kukhala Mpulumutsi wathu. Pachifukwa chimenechi, Yesu nthawi zambiri amatchedwa Yesu Khristu. Khristu amatanthauza wosankhidwa ndi Atate athu Akumwamba kukhala Mpulumutsi. Atate athu Akumwamba adasankha Yesu osati Satana chifukwa Atate athu Akumwamba sadafune kuti titaye ufulu wathu wosankha tokha. Iwo ankadziwa kuti tiyenera kuchita zinthu zabwino chifukwa chofuna kutero, osati chifukwa chakuti wina watikakamiza.

Zokambirana

  • Kodi Yesu ankafuna kutichitira chiyani?

  • Kodi Satana ankafuna kuchita chiyani?

  • Ndi chifukwa chiyani Atate athu Akumwamba adasankha Yesu kukhala Mpulumutsi wathu?

Image
Khristu ku Emmaus, wolemba Carl Heinrich Bloch

Atate Akumwamba adasankha Yesu kukhala Mpulumutsi wathu.

Yesu ndiye Mpulumutsi ndi Mtsogoleri Wathu

Pamene Atate athu Akumwamba adasankha Yesu, Satana adakwiya kwambiri. Iye adanyengelera gawo limodzi mwa magawo atatu a mizimu yakumwamba kuti imutsatire. Onse pamodzi adamenyana ndi Yesu ndi otsatira ake. Iwo ankafuna kukakamiza Atate athu Akumwamba kuti avomereze dongosolo la Satana. Atate athu Akumwamba adapangitsa Satana ndi otsatira ake kuchoka kumwamba.

Satana ndi otsatira ake sadzalandira matupi a mnofu ndi mafupa. Sadzatha kubwelera ndi kukakhala ndi Atate athu Akumwamba. Ndi okhawo amene adavomereza Yesu kukhala Mpulumutsi wawo angakhale ndi matupi a mnofu ndi mafupa.

Tikudziwa, chifukwa tiri ndi matupi amnofu ndi mafupa, kuti tidavomereza Yesu kukhala Mpulumutsi wathu. Tidasankha zinthu zabwino kumwamba. Tiyenera kupitiriza kusankha zinthu zoyenera pa dziko lapansi pano. Tikuyenera kutsatira Yesu. Iye yekha ndi amene angatiphunzitse m’mene tingabwelelere kwa Atate athu Akumwamba. Akhonza kutithandiza kugonjetsa zoipa zimene timachita ndi kutithandiza kuphunzira kuchita zinthu zabwino mpaka titakhala ngati Atate athu Akumwamba.

Atate athu Akumwamba amafuna kuti tizitsatira ndikumvera Yesu. Iwo amadziwa kuti Yesu adzatiphunzitsa njira ya Atate athu yakuchitira zinthu, kotero tikamvera Yesu, timakhalanso tikumvera Atate athu Akumwamba. Lamulo kapena uthenga wochokera kwa Yesu ndi lamulo kapena uthenga wochokera kwa Atate athu Akumwamba.

Zokambirana

  • Kodi tikudziwa bwanji kuti tidasankha Yesu kukhala Mpulumutsi wathu?

  • Kodi ndani yekha amene angatisonyeze m’mene tingabwelerele kwa Atate athu Akumwamba?

  • Ndi chifukwa chiyani tikuyenera kutsatira Yesu?

Print